Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yowotcha Mtembo wa Munthu?

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yowotcha Mtembo wa Munthu?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo silipereka malangizo aliwonse pa nkhani yowotcha mtembo. Komanso mulibe lamulo loti mtembo wa munthu uziwotchedwa kapena kuikidwa m’manda.

 M’Baibulo muli nkhani za atumiki okhulupirika a Mulungu omwe anaika m’manda mitembo ya achibale awo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Abulahamu anagula manda omwe anaikamo mkazi wake Sara.​—Genesis 23:2-20; 49:29-32.

 Baibulo limanenanso za anthu okhulupirika omwe anawotcha mitembo ya anthu. Mwachitsanzo, Mfumu Sauli ya ku Isiraeli ndi ana ake aamuna atatu ataphedwa ku nkhondo, mitembo yawo inakhalabe m’dera la adani ndipo siinasungidwe mwaulemu. Asilikali okhulupirika a ku Isiraeli atamva za nkhaniyi, anakatenga mitemboyo. Ataitenga anaiwotcha ndi kukaika phulusa lake. (1 Samueli 31:8-13) Ndipo Baibulo limasonyeza kuti zomwe zinachitikazi zinali zovomerezeka.​—2 Samueli 2:4-6.

Maganizo olakwika omwe anthu ambiri amakhala nawo pa nkhani yowotcha mtembo

 Maganizo olakwika: Kuwotcha mtembo sikulemekeza womwalirayo.

 Zoona zake: Baibulo limanena kuti munthu akamwalira amabwerera kufumbi. Zimenezi ndi zoona chifukwa thupi la munthuyo likawola limadzakhala fumbi. (Genesis 3:19) Kuwotcha mtembo kumachititsa kuti zimenezi zichitike mofulumira chifukwa thupilo limasanduka phulusa kapena fumbi.

 Maganizo olakwika: Kalelo, mitembo ya anthu okhawo omwe sankatumikira Mulungu ndi imene inkawotchedwa.

 Zoona zake: Ndi zoona kuti mitembo ya anthu osakhulupirika ngati Akani ndi anthu a m’banja lake inawotchedwa. (Yoswa 7:25) Komabe zimenezi zinangochitika ndipo silinali lamulo. (Deuteronomo 21:22, 23) Monga mmene taonera kumayambiriro kwa nkhaniyi, ngakhalenso mitembo ya anthu okhulupirika ngati Yonatani yemwe anali mwana wa Mfumu Sauli, inawotchedwa.

 Maganizo olakwika: Mulungu sadzaukitsa anthu omwe mitembo yawo inawotchedwa.

 Zoona zake: Mulungu adzaukitsa anthu kaya mitembo yawo inaikidwa m’manda, kuwotchedwa, kumira m’madzi kapenanso kudyedwa ndi zinyama. (Chivumbulutso 20:13) Mulungu Wamphamvu yonse sangakanike kulenganso matupi atsopano a anthu omwe anamwalirawo.​—1 Akorinto 15:35, 38.