Pitani ku nkhani yake

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yokhala ndi Anzathu?

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yokhala ndi Anzathu?

Yankho la m’Baibulo

 Kukhala ndi anzathu kumathandiza kuti tikhale osangalala komanso kuti zinthu zizitiyendera bwino. Anzathu abwino angatilimbikitse komanso kutithandiza kukhala anthu abwino.—Miyambo 27:17.

 Koma Baibulo limatsindika za kufunika kosankha mosamala anthu omwe tikufuna kuti akhale anzathu. Limatichenjeza za zimene zingachitike tikamacheza ndi anthu oipa. (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) Anthu oterewa angachititse kuti tisankhe zinthu mopanda nzeru komanso kuti tisiye kukhala ndi makhalidwe abwino.

Zimene zili munkhaniyi

 Kodi mnzathu wabwino tingamudziwe bwanji?

 Baibulo limaphunzitsa kuti sitiyenera kungopeza anzathu amene amakonda zosangalatsa zimene ifenso timakonda. Mwachitsanzo, lemba la Salimo 119:63 limanena kuti: “Ine ndine mnzawo wa anthu okuopani, a ndiponso wa anthu osunga malamulo anu.” Wolemba Baibuloyu ananena kuti iye ankasankha anzake amene ankaopa Mulungu komanso omwe ankafunitsitsa kutsatira mfundo zake.

 Baibulo limafotokozanso makhalidwe abwino amene mnzathu wabwino ayenera kukhala nawo. Mwachitsanzo limati:

  •   “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

  •   “Pali mabwenzi amene amafuna kuthyolana, koma pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.”—Miyambo 18:24.

 Mavesiwa amasonyeza kuti mnzathu wabwino ndi munthu wokhulupirika, wachikondi, wokoma mtima komanso wopatsa. Mnzathu weniweni ndi munthu amene tingamudalire kuti atithandiza pa nthawi zabwino ndi zovuta zomwe. Komanso mnzathu weniweni amalimba mtima n’kutichenjeza tikafuna kuchita zinthu zosayenera kapena kusankha zinthu mopanda nzeru.—Miyambo 27:6, 9.

 Kodi m’Baibulo muli zitsanzo ziti za anthu amene anali mabwenzi abwino?

 M’Baibulo muli zitsanzo za anthu amene anali ndi anzawo abwino ngakhale kuti ankasiyana misinkhu, kochokera, chikhalidwe komanso udindo. Tiyeni tione zitsanzo zitatu.

  •   Rute ndi Naomi. Rute anali mpongozi wa Naomi ndipo n’kutheka kuti ankasiyana kwambiri zaka. Komanso Rute anali wachikhalidwe chosiyana ndi cha Naomi. Ngakhale kuti ankasiyana chonchi, ankagwirizana komanso kukondana kwambiri.—Rute 1:16.

  •   Davide ndi Yonatani. Ngakhale kuti zikuoneka kuti Yonatani anali wamkulu kwa Davide ndi zaka 30, Baibulo limanena kuti Davide ndi Yonatani ’ankagwirizana kwambiri.’—1 Samueli 18:1.

  •   Yesu ndi atumwi ake. Yesu anali ndi udindo waukulu kuposa atumwi ake chifukwa anali mphunzitsi komanso mbuye wawo. (Yohane 13:13) Koma iye sankawaona kuti ndi osayenera kukhala anzake. M’malomwake, Yesu ankakonda kwambiri anthu amene ankatsatira zimene iye ankaphunzitsa. Iye anati: “Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.”—Yohane 15:14, 15.

 Kodi n’zotheka kukhala mnzake wa Mulungu?

 Inde, n’zotheka anthu kukhala anzake a Mulungu. Baibulo limanena kuti: “Yehova amakonda anthu owongoka mtima.” (Miyambo 3:32) Choncho Mulungu amagwirizana ndi anthu amene ali ndi makhalidwe abwino, oona mtima, aulemu komanso amene amayesetsa kutsatira mfundo zake zokhudza zoyenera ndi zosayenera. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Abulahamu, yemwe anali munthu wokhulupirika, anali bwenzi la Mulungu.—2 Mbiri 20:7; Yesaya 41:8; Yakobo 2:23.

a Mavesi ena a mu salimoli amasonyeza kuti mawu oti “okuopani,” amanena za anthu oopa Mulungu.