Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHINSINSI CHA BANJA LOSANGALALA

Kodi Mungatani Kuti Musamakangane ndi Mwana Wanu?

Kodi Mungatani Kuti Musamakangane ndi Mwana Wanu?

“Mwana wanga ali ndi zaka 14, anayamba kukula mtima. Ndikamuuza kuti, ‘Tiye tikadye chakudya,’ ankandiyankha kuti ‘Ndakuuzani kuti ndikufuna kudya?’ Ndikamufunsa ngati wamaliza ntchito, ankandiyankha kuti ‘Iii, kodi ndine wantchito wanu?’ Nthawi zambiri tinkakangana kwambiri.”—Anatero MAKI, wa ku JAPAN. *

Kulera wachinyamata ndi kovuta kwambiri ndipo kumafuna kuti makolo akhale odekha. Mayi wina wa ku Brazil dzina lake Maria, yemwe akulera mwana wa zaka 14 anati: “Zimandipsetsa mtima kwambiri mwana wanga akamandiderera.” Zimenezi zikufanana ndi zimene mayi winanso wa ku Italy, dzina lake Carmela, ananena. Iye anati: “Ndikakangana ndi mwana wanga wamwamuna, tonse timakhumudwa kwambiri. Nkhani yabwinobwino imasanduka mkangano woopsa. Zikatere mwana wanga amangolowa kuchipinda n’kudzitsekera.”

N’chifukwa chiyani achinyamata ena amakhala ovuta chonchi? Kodi amawapangitsa ndi anzawo? Mwina kapena. Chifukwa Baibulo limanena kuti munthu akhoza kukhala ndi makhalidwe abwino kapena oipa chifukwa chotengera anthu amene amacheza nawo. (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) Chinanso chimene chimapangitsa kuti ana masiku ano azikhala osamvera makolo ndi zosangalatsa zimene zimawalimbikitsa kuti akhale ovuta komanso opanda ulemu.

Koma pali mavuto ena amene si ovuta kuwathetsa ngati mwadziwa chimene chikupangitsa mwanayo kuchita zimenezo. Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zingakuthandizeni.

PHUNZITSANI MWANA WANU KUMAGANIZA

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene ndinali kamwana, ndinali kulankhula ngati kamwana, kuganiza ngati kamwana, ndiponso kuona zinthu ngati kamwana. Koma tsopano pamene ndakula, ndasiya zachibwana.” (1 Akorinto 13:11) Monga mmene Paulo ananenera palembali, mwana amaganiza mosiyana  kwambiri ndi munthu wamkulu. Kodi amasiyana bwanji?

Achinyamata amafuna kuoneratu ngati chinthucho chili choipa kapena chabwino. Pamene munthu wamkulu amaona patali, ndipo asanasankhe zochita, amaganizira kaye za zotsatira zake. Mwachitsanzo, munthu wamkulu amayamba waganiza kaye mmene zinthuzo zingakhudzire ena. Ndipo akhoza kukhala anazolowera kuchita zimenezi. Koma achinyamata saganiza choncho, chifukwa amakhala asanazolowere kusankha zinthu m’njira imeneyi.

Baibulo limalimbikitsa achinyamata kuti “azitha kuganiza bwino.” (Miyambo 1:4) Koma limalimbikitsanso Akhristu onse kuti azigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza.” (Aroma 12:1, 2; Aheberi 5:14) Komabe, nthawi zina mwana wanu akhoza kumakangana nanu pa zinthu zing’onozing’ono chifukwa cha mmene amaganizira. Kapena angakuuzeni maganizo ake, omwe angaoneke ngati opanda nzeru. (Miyambo 14:12) Ngati zitatero, kodi mungatani kuti musakangane?

TAYESANI IZI: Muyenera kudziwa kuti mwana wanuyo akuphunzira kusankha zinthu payekha. Izi zikutanthauza kuti zimene angakuuzeni, sikuti amakhala atatsimikiza kuti achitadi zimenezo. Kuti mudziwe zimenedi akuganiza, choyamba muyenera kumuyamikira ponena maganizo ake. Mungathe kunena kuti: “Ndasangalala ndi mmene ukuganizira pa nkhaniyi. Komabe ine ndikuganiza mosiyana pang’ono ndi mmene iwe ukuganizira.” Kenako muthandizeni kuona mavuto amene angakhalepo ngati angachite zimene akuganizazo. Mungamufunse kuti: “Kodi ukuganiza kuti zimenezi n’zothandiza nthawi zonse?” Mungadabwe ndi zimene mwana wanuyo anganene pambuyo poti waganiziranso zimene ankafunazo.

Chenjezo: Mukamakambirana ndi mwana wanuyo, pewani kumusonyeza kuti zimene mukunenazo ndiye zolondola. Ngakhale zitakhala kuti akuonetsa kuti sakumva zimene mukumuuza pa nthawiyo, muyenera kuzindikira kuti iye angathe kuphunzirapo kanthu pa zimene mwanena ngakhale kuti sangasonyeze zimenezo. Simuyenera kudabwa ngati mutaona kuti posapita nthawi, mwanayo watsatira zimene munkamulangizazo. Mwina angayambenso kunena kuti zimene wasankhazo wachita kuganiza yekha.

Bambo wina wa ku Japan, dzina lake Kenji anati: “Nthawi zina ndinkakangana ndi mwana wanga wamwamuna pa nkhani zing’onozing’ono monga, kumuletsa kuwononga zinthu kapena akamanyoza mchemwali wake. Koma nthawi zambiri ankafuna kuti ine ndimufunse chifukwa chimene akuchitira zimenezo. Ankafunanso ndimusonyeze kuti ndikumvetsa zimene zamuchititsa kuchita zimenezo. Iye akanasangalala ndikanamuuza kuti: ‘Owoo, kodi ndi mmene zinakhalira.’ Ndikuona kuti ndikanachita zimenezi, mwina sitikanakangana.”

AZIDZIWA ZOYENERA KUCHITA

Makolo anzeru amalola ana awo kufotokoza zinthu momasuka

Udindo waukulu umene makolo amakhala nawo polera achinyamata, ndi kuwathandiza kuti tsiku lina adzadziimire paokha. (Genesis 2:24) Zimenezi zimaphatikizapo kumuthandiza mwanayo kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Wachinyamata amene ali ndi makhalidwe abwino angakane kuchita zoipa osati chifukwa choopa chilango, koma amaganiziranso kuipa kwa zimene angachitezo. Komanso angathe kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndine munthu wotani? Kodi ndimayendera mfundo ziti? Kodi munthu amene amayendera mfundo zimenezi akanatani pa nkhani ngati imeneyi?’—2 Petulo 3:11.

M’Baibulo muli nkhani ya Yosefe, yemwe anali wachinyamata amene ankadziwika kuti anali ndi makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, mkazi wa Potifara atamukakamiza kuti agone naye, Yosefe anayankha kuti: “Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?” (Genesis 39:9) Ngakhale kuti pa nthawiyi lamulo loletsa kuchita chigololo linali lisanaperekedwe kwa Aisiraeli, Yosefe ankayendera maganizo a Yehova pa nkhaniyi. Mawu akuti “ndingachitirenji” akusonyeza kuti ankatsatira kwambiri mfundo za Yehova ndipo ankaziona kuti n’zofunika pa moyo wake.—Aefeso 5:1.

Mwana wanuyonso akulimbana n’kuti apeze mfundo zimene aziyendera pa moyo wake. Zimenezitu n’zofunika chifukwa zingamuthandize kuti azilimbana ndi mavuto amene amakumana nawo kuchokera kwa achinyamata anzake. (Miyambo 1:10-15) Koma dziwani kuti zingam’chititsenso kuti azilimbana ndi inuyo. Kodi muyenera kuchita chiyani ngati zimenezi zitachitika?

TAYESANI IZI: M’malo mokwiya ndi zimene mwana wanu wanena, yesani kungobwereza zimene iye wanenazo ponena kuti: “Ndikufuna ndingomvetsa zimene ukunena, paja wati . . . ” Kenako mufunseni kuti: “N’chifukwa chiyani ukuganiza choncho?” Kapena “N’chiyani chakupangitsa kuti unene zimenezi?” Muloleni kufotokoza maganizo ake. Ngati mukuona kuti mukungosiyana zokonda, ndipo sikuti mwana wanuyo walakwa chinachake, mungachite bwino kungololera maganizo akewo ngakhale kuti simukugwirizana ndi zimene wasankha.

Zimene mwana wanuyo akuchita pofuna kupeza mfundo zimene angamayendere pa moyo wake si zachilendo ndiponso zingamuthandize. Komanso pajatu  Baibulo limanena kuti Akhristu sayenera kukhala ngati ana aang’ono ‘otengekatengeka ngati kuti akukankhidwa ndi mafunde, ndiponso otengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso chonyenga.’ (Aefeso 4:14) Choncho thandizani mwana wanu kukhala ndi makhalidwe abwino omwe angamuthandize kuti asatengere makhalidwe oipa.

Mayi wina wa ku Czech Republic, dzina lake Ivana anati: “Ana anga aakazi ndikawasonyeza kuti ndine wofunitsitsa kuwamvetsera, savuta kumvera zimene ndikuwauza, ngakhale zitakhala zosiyana ndi zimene iwo amafuna. Koma ndimasamala kuti ndisamawakakamize kuchita zimene ineyo ndikufuna, koma kuti aziona okha ubwino wotsatira zimene ndikuwauzazo.”

MUSAMASINTHESINTHE KOMABE MUZIKHALA OLOLERA

Monga mmene ana aang’ono amachitira, achinyamata ena angauze makolo nkhani imodzimodziyo kangapo n’cholinga choti makolo awo atope ndi nkhaniyo n’kuwavomera kuchita zimene akufuna. Ngati mwana wanu amachita zimenezi, muyenera kusamala. Ngakhale kuti kuvomereza kuti achite zimene akufunazo kungapangitse kuti musakangane, zingachititse kuti mwanayo azikuvutitsani kuti apeze zimene akufuna. Kodi mungachite chiyani kuti muthane ndi vuto limeneli? Muzitsatira malangizo a Yesu akuti: “Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi.” (Mateyu 5:37) Achinyamata sangakukakamizeni kuti muyendere maganizo awo ngati simusinthasintha zimene mwanena.

Komabe kumbukirani kuti muyenera kukhala ndi mtima wololera pamene mukuchita zimenezi. Mwachitsanzo, muloleni wachinyamata wanu kuti afotokoze zifukwa zimene muyenera kusinthira nthawi yoti azifikira pakhomo. Mukamachita zimenezi, sikuti mukukakamizika kutsatira zimene mwana wanu akufuna, koma mukusonyeza kuti mukutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.”—Afilipi 4:5.

TAYESANI IZI: Muzipeza nthawi yokhala pansi ndi ana anu n’kukambirana za nthawi yoti anawo azifikira pakhomo komanso malamulo ena amene ayenera kumatsatira. Asonyezeni kuti ndinu ofunitsitsa kumvetsera zimene iwo anganene. Kenako muyenera kuganizira zonse zimene ana anu akufotokozerani musanasankhe zochita. Bambo wina wa ku Brazil, dzina lake Roberto, anati: “Achinyamata aziona kuti makolo awo savuta kuwavomereza zinthu, ngati zinthuzo sizikuphwanya mfundo za m’Baibulo.”

N’zoona kuti palibe kholo limene sililakwitsa zinthu. Baibulo limati: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yakobo 3:2) Mukaona kuti mwalakwitsa zinazake, musachedwe kupepesa mwana wanuyo. Ngati mutavomereza kuti munalakwitsa, mungapereke chitsanzo chabwino kwa mwanayo kuti nayenso azipepesa akalakwitsa zinazake.

Kenji wa ku Japan, yemwe tamutchula mu nkhani ino ananenanso kuti: “Tikakangana pa nkhani inayake, ndimapepesa kwa mwana wanga chifukwa chomukalipira. Ndimachita zimenezi mtima wanga ukakhala m’malo. Izi zimapangitsa kuti nayenso mtima wake ukhale m’malo ndipo sizivuta kuti azimvetsera zimene ndikumuuza.”

^ ndime 3 Mayina m’nkhani ino asinthidwa.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi ineyo ndinachita chiyani chimene chinapangitsa kuti ndikangane ndi mwana wanga?

  • Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji mfundo za m’nkhaniyi kuti ndizimumvetsa bwino mwana wanga?

  • Kodi ndingatani kuti ndisamakangane ndi mwana wanga?