Pitani ku nkhani yake

Oimira Mboni za Yehova, anakumana ndi mkulu wa Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu ku Korea kuti akambirane mmene ndondomeko yoperekera ntchito zosakhudzana ndi usilikali ikuyendera. Pambuyo pa zokambiranazo, bungweli linalembera boma chikalata chofotokoza mmene mavutowa angathetsedwere

27 JANUARY, 2022
SOUTH KOREA

Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu ku Korea Lapempha Boma Kuti Liunikenso Bwino Ntchito Zomwe Zimaperekedwa kwa Anthu Okana Usilikali

Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu ku Korea Lapempha Boma Kuti Liunikenso Bwino Ntchito Zomwe Zimaperekedwa kwa Anthu Okana Usilikali

Akuluakulu oona za ufulu wa anthu ku South Korea, alembera boma chikalata ndi kuliuza kuti ndondomeko zomwe bomali likutsatira popereka ntchito zosakhudzana ndi usilikali, sizikugwirizana ndi mfundo zatsopano zokhudza ufulu wa anthu padziko lonse.

Pa 2 December 2021, mkulu watsopano wa Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu ku Korea (NHRCK), a a Song Doo-hwan analemba chikalatachi pa webusaiti yawo chofotokoza kuti ndondomeko zoperekera ntchito zosakhudzana ndi usilikali ziyenera kusinthidwa. Pa 26 October 2020, boma la South Korea linayamba kupereka ntchito zina kwa anthu omwe amakana kulembedwa ntchito yausilikali.

Zina zomwe mtsogoleriyu ananena ndi zakuti: “Ngakhale kuti boma linayamba kupereka ntchito zina kwa anthu okana usilikali, kuyambira pomwe Khoti Loona za Malamulo linapereka chigamulo chake mu 2018, ndikugwirizana ndi maganizo oti ndondomeko yoperekera ntchitozi iyenera kuonedwanso kuti igwirizane ndi mfundo za padziko lonse zoona za ufulu wa anthu . . .”

Chikalatachi chinalembedwa a Song atakumana ndi oimira nthambi ya Mboni za Yehova ku South Korea komanso bungwe la Mboni za Yehova la Asia-Pacific Association of Jehovah’s Witnesses (APAJW) pa 3 November, 2021. Abale anapereka kwa a Song lipoti lamutu wakuti, “Lipoti la 2021 Lonena za Ntchito Zosakhudzana ndi Usilikali ku South Korea” lomwe linalembedwa ndi bungwe la Asia-Pacific Association of Jehovah’s Witnesses (APAJW).

Lipotilo linafotokoza kuti ndondomeko ya boma la South Korea loperekera ntchito zosakhudzana ndi usilikali, ikuphwanya mfundo za padziko lonse. Munthu wokana usilikali, amaikidwa pa ndondomekoyi kwa miyezi 36 yomwe ndi kuwirikiza kawiri nthawi imene munthu amakhala akuchita maphunziro ausilikali. Anthu omwe ali pa ndondomekoyi amasungidwa ngati akaidi. Panopa, anthu omwe amakana kulembedwa ntchito yausilikali chifukwa chotsatira zomwe amakhulupirira, amagwira ntchitozi ali kundende ndipo m’mwezi wawo woyamba, saloledwa kutuluka kundendeko. Mweziwo ukatha, m’pamene amaloledwa kutuluka. Koma amatuluka pokhapokha ngati apatsidwa chilolezo ndipo amafunika kuti azikhala atabwerako pofika 9:30 usiku.

Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu ku Korea likuonanso madandaulo omwe aperekedwa opempha kuti ndondomeko yoperekera ntchito zina iunikidwenso bwino. Ngakhale kuti bungweli lilibe mphamvu zosintha malamulo, koma limatha kupereka maganizo ake kwa anthu omwe ali ndi udindo wokonza malamulo.

Timalimbikitsidwa kwambiri tikaganizira chikhulupiriro chomwe abale athu ku South Korea akusonyeza. Tikudziwa kuti Yehova adzawadalitsa chifukwa cha khama lawo.—Salimo 55:22.

LIPOTI LAPADERA: Lipoti la 2021 Lonena za Ntchito Zosakhudzana ndi Usilikali ku South Korea

a Bungwe Loona za Ufulu wa Anthu ku Korea linakhazikitsidwa mu 2001.