Pitani ku nkhani yake

Anadzipereka Ndi Mtima Wonse ku Bulgaria

Anadzipereka Ndi Mtima Wonse ku Bulgaria

 A Mboni za Yehova ku Bulgaria akugwira mwakhama ntchito yophunzitsa anthu choonadi chokhudza Mulungu ndiponso Mawu ake, Baibulo. Kuyambira mu 2000, a Mboni ambirimbiri ochokera kumayiko ena akhala akusamukira ku Bulgaria pofuna kuthandiza nawo pa ntchitoyi. Kodi ndi mavuto otani amene akumana nawo chifukwa chosamukira kudziko lina kuti akalalikire? Nanga apeza madalitso otani? Taonani zimene abale ndi alongo ena omwe anasamukira ku Bulgaria ananena.

Tinadziikira Cholinga

 Darren yemwe amakhala ku England anati: “Kuyambira kalekale, tinkafunitsitsa kukatumikira kudziko lina kumene kukufunika olalikira ambiri. Nditangokwatirana ndi Dawn, tinasamukira ku London kuti tikagwire nawo ntchito yophunzitsa anthu Baibulo m’chinenero cha Chirasha. Tinayesera maulendo angapo kukonza zinthu pa moyo wathu kuti tisamukire kudziko lina, koma tinkalephera pa zifukwa zosiyanasiyana. Tinangotsala pang’ono kusintha maganizo, koma mnzathu wina anatithandiza kuti tiganizirenso mmene zinthu zasinthira pa moyo wathu ndipo tinaona kuti titha kusamuka.” Choncho Darren ndi Dawn anayamba kufufuza dziko limene likufunika olalikira ambiri ndiponso lomwe angakwanitse kusamukirako. Mu 2011, anasamukira ku Bulgaria.

Darren ndi Dawn

 Anthu ena amene poyamba analibe zolinga zokalalikira kumayiko ena, amalimbikitsidwa akaona chimwemwe chimene anthu omwe amasamukira kumayiko ena kuti akalalikire amakhala nacho. Giada yemwe anakhalapo ku Italy ndi mwamuna wake Luca, anati: “Ndinakumana ndi alongo ena omwe ankasangalala kutumikira mwakhama ku South America ndi ku Africa. Zinandikhudza kwambiri atandifotokozera zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo kumeneko ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndiwonjezere zomwe ndimachita potumikira Yehova.”

Luca ndi Giada

 Tomasz ndi Veronika anasamuka ku Czech Republic kupita ku Bulgaria mu 2015 limodzi ndi ana awo awiri, Klara ndi Mathias. Kodi n’chiyani chinawalimbikitsa kuti akhale ndi maganizo ofuna kusamuka? Tomasz akuti: “Tinaganizira kwambiri zitsanzo za anthu ena omwe anasamukira kumayiko ena kuphatikizapo achibale athu komanso zinthu zabwino zomwe akumana nazo. Tinachita chidwi kwambiri kuona chimwemwe chomwe ali nacho ndipo tinakambirana nkhaniyi ndi banja langa lonse.” Panopa Tomasz ndi banja lake akusangalala kulalikira m’gawo latsopano mumzinda wa Montana ku Bulgaria.

Klara, Tomasz, Veronika, ndi Mathias

 Wa Mboni winanso amene anasamukira ku Bulgaria ndi Linda. Iye anati: “Zaka zingapo m’mbuyomu ndinapita ku Ecuador ndipo ndinakumana ndi a Mboni ena omwe anasamukira m’dzikolo kukalalikira. Zimenezi zinandichititsa kuganiza kuti mwina nanenso ndingasamukire komwe kukufunika olalikira ambiri.” Petteri ndi mkazi wake Nadja a ku Finland nawonso anaganizira zitsanzo za a Mboni ena. Iwo anati: “Mumpingo mwathu tinali ndi ofalitsa ena omwe anasamukira komwe kukufunika olalikira ambiri. Nthawi zonse ankalankhula zinthu zabwino zomwe zinawachitikira pa zaka zonse zimene ankachita utumiki umenewu. Iwo ananena kuti zaka zimenezi zinali zosangalatsa kwambiri pa moyo wawo.”

Linda

Nadja ndi Petteri

Kukonzekera

 Anthu amene akufuna kukatumikira kudziko lina amafunika kukonzekera bwino. (Luka 14:28-30) Nele, wa ku Belgium anati: “Maganizo ofuna kukatumikira kudziko lina atayamba kukula, ndinapemphera ndipo ndinayamba kufufuza nkhani zam’mabuku athu zokhudza kukatumikira kudziko lina. Ndinayamba kuwerenga nkhanizi n’kuona zinthu zomwe ndinayenera kuchita pokonzekera kusamuka.”

Nele (kumanja)

 Kristian ndi Irmina a ku Poland nawonso anakhala ku Bulgaria kwa zaka zopitirira 9. Iwo anaona kuti kusonkhana ndi kagulu kolankhula Chibugaliya pa nthawi yomwe anali ku Poland kunawathandiza kwambiri asanasamuke. Abale ndi alongo am’kagulu komwe ankasonkhana anawathandiza kuphunzira chinenerochi. Kristian ndi Irmina anati: “Tinaona kuti munthu ukakhala ndi mtima wodzipereka, Yehova Mulungu amakuthandiza ndipo amakupatsa zomwe ukufunikira. Ukangomuuza Yehova kuti, ‘Ine ndilipo! Nditumizeni,’ umatha kuchita zinthu zomwe unkaganiza kuti sungakwanitse.”—Yesaya 6:8.

Kristian ndi Irmina

 Reto ndi mkazi wake Cornelia a ku Switzerland, anasankha kukhala moyo wosalira zambiri n’cholinga choti akonzekere ndi kusunga ndalama zoti zikawathandize akasamuka. Iwo anati: “Kutatsala chaka kuti tisamuke, tinapita ku Bulgaria n’kukakhalako mlungu umodzi kuti tikaone mmene zinthu ziliri m’dzikolo. Titafika, tinacheza ndi banja lina lomwe linkachita umishonale ndipo linatipatsa malangizo othandiza kwambiri.” Reto ndi Cornelia anayesetsa kugwiritsa ntchito malangizowo ndipo panopa akhala ali ku Bulgaria kwa zaka zoposa 20.

Cornelia ndi Reto, limodzi ndi ana awo Luca ndi Yannik

Kupirira Mavuto

 Anthu amene asamukira kudziko lina angafunike kuzolowera zinthu zatsopano mwinanso kupirira mavuto atsopano. (Machitidwe 16:9, 10; 1 Akorinto 9:19-23) Vuto lalikulu limene anthu ambiri amakumana nalo ndi kuphunzira chinenero. Luca amene tamutchula koyambirira uja anati: “Nthawi zonse tinkasangalala kuyankha m’mawu athuathu pamisonkhano yampingo. Komabe, kwa nthawi ndithu, ine ndi mkazi wanga tinkavutika kukonzekera ngakhale ndemanga yosavuta mu Chibugaliya. Tinkangokhala ngati ana. Komabe, ana akumeneko ankayankha ndemanga zomveka bwino kuposa ifeyo.”

 Ravil, wa ku Germany anati: “Kuphunzira chinenero chatsopano kunali kotopetsa. Koma ndinkangodziuza kuti, ‘Ukalakwitsa usakhumudwe, uzingoseka basi.’ Mavuto omwe ndikukumana nawo sindikuwaonanso ngati chipsinjo koma ngati utumiki wopatulika womwe ndikuchitira Yehova.”

Ravil ndi Lilly

 Linda yemwe tamutchula kale uja anati: “Ineyo ndimavutika kwambiri kuphunzira zinenero zina. Ndipo Chibugaliya ndi chovuta kuphunzira moti maulendo angapo ndinkaganiza zongosiya. Munthu umadzimva kuti uli wekhawekha ukakhala kuti sungathe kulankhula kapena kumva chinenero chomwe anthu ena akulankhula. Komabe kuti ndipitirize kulimbitsa ubwenzi wanga ndi Yehova, ndinkaphunzira zinthu zonse zauzimu mu Chiswidishi. Kenako, ndinakwanitsa kuphunzira Chibugaliya pothandizidwa ndi abale ndi alongo.”

 Vuto linanso lomwe amafunika kulimbana nalo, ndi kusowa kunyumba. Anthu amene amasamukira kudziko lina amakhala atasiya achibale ndi anzawo. Eva yemwe anasamukira ku Bulgaria ndi mwamuna wake Yannis anati: “Poyamba ndinkangoona kuti ndili ndekhandekha. Koma kuti tithane ndi vuto limeneli, nthawi zonse tinkakonda kulankhulana ndi achibale komanso anzathu kunyumba, ndipo tinapezanso anzathu ena kunoko.”

Yannis ndi Eva

 Koma palinso mavuto ena. Robert ndi Liana omwe anachokera ku Switzerland anati: “Kwa ife, vuto lalikulu linali kuphunzira chinenero ndi chikhalidwe cha kunoko, komanso tinali tisanakonzekere nyengo yozizira kwambiri.” Ngakhale zinali choncho, banjali lakwanitsa kutumikira ku Bulgaria kwa zaka 14 chifukwa chokhala ndi maganizo oyenera komanso kukhalabe achimwemwe.

Robert ndi Liana

Madalitso Omwe Apeza

 Lilly waona ubwino wokalalikira komwe kukufunika olalikira ambiri. Iye anati: “Kwandithandiza kuona mmene Yehova amathandizira atumiki ake m’njira zinanso zomwe sindikanaziona ndikanakhala kuti ndikungotumikira kwathu. Ndimathera nthawi yambiri pothandiza anthu, zomwe zandithandiza kuti ndilimbitse ubwenzi wanga ndi Yehova, ndizikhala wosangalala komanso wokhutira.” Mwamuna wake Ravil anavomereza zimene mkazi wake ananena kuti: “Umenewu ndi moyo wabwino kwambiri womwe umatipatsa mwayi wapadera wodziwana ndi Akhristu achangu omwe akhala akuphunzitsa mfundo za m’Baibulo kwa nthawi yaitali m’mayiko osiyanasiyana. Ineyo ndaphunzira zambiri kwa abale ndi alongo amenewa.”

 Mtima wofunitsitsa komanso wodzipereka umene abale ndi alongo ambiri asonyeza, wathandiza kuti ntchito yolalikira “uthenga wabwino . . . wa Ufumu . . .padziko lonse lapansi kumene kuli anthu” itheke. (Mateyu 24:14) Abale ndi alongo amene anasamukira ku Bulgaria adzionera okha mmene Yehova wakwaniritsira zokhumba za mtima wawo ndi kudalitsa khama lawo lonse chifukwa chakuti anasonyeza mtima wodzipereka.—Salimo 20:1-4.