Pitani ku nkhani yake

Lipoti la Msonkhano Wapachaka wa 2014

Patha Zaka 100 Ufumu Ukulamulira

Lipoti la Msonkhano Wapachaka wa 2014

Pa October 4, 2014, anthu pafupifupi 19,000, anapezeka pamsonkhano wapachaka wa nambala 130, wa bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Msonkhanowu unachitikira ku Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova yomwe ili ku Jersey City, New Jersey, U.S.A., ndipo anthu ena anaonera msonkhanowu pa TV m’madera angapo.

A Mark Sanderson, omwe ndi a m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, ndi amene anali tcheyamani pa msonkhanowu. Iwo anayamba n’kunena kuti msonkhanowu ndi wofunika kwambiri m’mbiri ya Mboni za Yehova chifukwa unalinso wokumbukira kuti patha zaka 100 kuchokera pamene Ufumu wa Mesiya unayamba kulamulira.

M’bale Sanderson anafotokoza zinthu zapadera zitatu zimene Ufumuwu wachita m’zaka 100 zimenezi, ndipo zinthuzi ndi:

  • Ntchito yolalikira padziko lonse. Yehova wakhala akudalitsa atumiki ake kuti alalikire mwakhama ndi kuuza anthu za uthenga wabwino wa Ufumu. Ndipotu zimenezi zachititsa kuti chiwerengero cha olalikira za Ufumuwu chomwe chinali chochepa mu 1914, chikule kwambiri n’kupitirira 8 miliyoni pofika m’chaka cha 2014. Kunena zoona, sitidzasiya kulalikira mwakhama mpaka Yehova adzanene kuti basi siyani.

  • Kuteteza nzika za Ufumu monga gulu. Akuluakulu a zipembedzo komanso a ndale ayesetsa kuchita zinthu zoipa pofuna kusokoneza ntchito yathu komanso kuthetseratu gulu la Mboni za Yehova. Komabe, Yehova wakhala akuteteza atumiki ake monga gulu. Mwachitsanzo, Khoti Lalikulu Kwambiri la ku America komanso Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, laweruza milandu yambiri mokomera gulu la Mboni za Yehova ndipo umenewu ndi umboni wakuti Yehova akupitirizabe kutiyang’anira masiku ano.

  • Kugwirizanitsa anthu a mitundu yonse. Ufumu wa Mulungu wathandiza kuti anthu a zikhalidwe, mitundu komanso zinenero zosiyanasiyana azichita zinthu mogwirizana. Iwo amathandizana pa mavuto osiyanasiyana komanso amalambira Mulungu mogwirizana. M’bale Sanderson ananena kuti: “Yehova yekha ndi amene akuchititsa kuti zimenezi zitheke.” M’baleyu ananena motsindika kuti anthu onse amene anali pamsonkhanowu anaona kuti unali mwayi waukulu kupezeka pamsonkhano wapachaka wosaiwalikawu.

Mavidiyo Akuti, Khalani Bwenzi la Yehova.

M’bale Sanderson anafotokoza za mavidiyo akuti Khalani Bwenzi la Yehova, omwe takhala tikuonera kwa zaka zoposa ziwiri. Choyamba, anauza anthu kuti aonera vidiyo yosonyeza zimene ana a m’mayiko osiyanasiyana ananena zokhudza mavidiyowa. Anthu ataonera vidiyoyi anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene anawa ananena posonyeza kuyamikira zimene aphunzira m’mavidiyowa.

Kenako anaonetsa vidiyo yatsopano yamutu wakuti Yehova Akuthandiza Kuti Ukhale Wolimba Mtima.Vidiyoyi ndi ya maminitsi 12 ndipo ndi ya nkhani ya m’Baibulo imene inachitikadi. Nkhaniyi ndi yokhudza mtsikana wachiisiraeli yemwe anauza mkazi wa Namani zokhudza Yehova molimba mtima. (2 Mafumu 5:1-14) Vidiyoyi inaikidwa pawebusaiti ya jw.org Lolemba pa October 6, 2014 ndipo ikupezeka m’zinenero zoposa 20.

Kuphunzira Chinenero pa JW.

M’bale Sanderson analengeza za kutulutsidwa kwa pulogalamu yophunzirira chinenero ya pa jw. Pulogalamuyi izithandiza a Mboni za Yehova omwe akufuna kuphunzira chinenero china kuti azitha kulalikira kwa anthu a m’chinenerocho. Pa pulogalamuyi pali zinenero 18 ndipo pamapezeka mawu oposa 4,000 a m’zinenerozi. Panopa ntchito yowonjezera mawu ena, zitsanzo za muulaliki komanso magawo ena ili mkati.

Kuulutsa Nkhani pa TV ya JW.

Anthu amene anapezeka pamsonkhanowu anali ndi chimwemwe chodzadza tsaya atamva kuti papangidwa siteshoni ya TV ya pa Intaneti ya Mboni za Yehova imene ili m’Chingelezi mokha n’cholinga chongoiyesera kaye. Siteshoni ya TV imeneyi ili ku Brooklyn, New York, m’dziko la United States komwe ndi ku likulu lathu la padziko lonse. Pasiteshoniyi pazipezeka mavidiyo, nyimbo ndi nkhani za m’Baibulo zowerengedwa ngati sewero. Kuwonjezera pamenepa, mwezi uliwonse pazikhala pulogalamu imene iziulutsidwa ndi membala wa Bungwe Lolamulira kapena wothandiza m’makomiti a bungweli.

M’bale Sanderson anasonyeza mwachidule pulogalamu yoyambirira yomwe anaulutsa a Stephen Lett, a m’Bungwe Lolamulira. Pa pulogalamuyi anaonetsa zimene zinachitika pokonza siteshoni ya TV ya JW yomwe inayamba kuoneka pa October 6, 2014 ndipo ikupezeka pawebusaiti ya tv.pr418.com.

“Ufumu Walamulira kwa Zaka 100 Ndipo Ukupitirizabe Kulamulira.”

A Samuel Herd, omwe ndi a m’Bungwe Lolamulira anafotokoza za vidiyo yomwe inasonyeza mmene Ufumu wa Mulungu wathandizira kuti olalikira za Ufumu akhale ambiri komanso kuti tiwonjezere luso lathu pa ntchito yolalikira. Vidiyoyi inasonyeza zinthu zakale, zitsanzo komanso zimene anthu amene akhala a Mboni kwa nthawi yaitali ananena. Inasonyezanso zimene zinachitika popanga vidiyo yakuti “Sewero la Pakanema la Chilengedwe” komanso mmene vidiyoyi inafalikira padziko lonse. Kuwonjezera pa zinthu zimenezi, vidiyoyi inaonetsanso mmene ankagwiritsira ntchito galamafoni, makadi ochitira umboni, ndi mmene ankalalikirira poyenda ndi zikwangwani komanso magalimoto okhala ndi zokuzira mawu. M’vidiyoyi ananenanso za sukulu zosiyanasiyana zimene zinakhazikitsidwa n’cholinga chotiphunzitsa mmene tingagwirire ntchito yolalikira.

Kodi timapindula bwanji tikamaganizira zimene Ufumu wachita pa zaka 100 zimene wakhala ukulamulira? Zimatithandiza kuona kuti Ufumuwu ndi weniweni komanso kuti tiziganizira ndiponso kuyembekezera zimene udzatichitire m’tsogolomu.

Nyimbo Zotithandiza Polambira.

Anthu onse anasangalala pamene M’bale David Splane, wa m’Bungwe Lolamulira, analengeza kuti buku lakuti Imbirani Yehova likonzedwanso. Chikuto komanso masamba a bukuli azioneka ngati a buku la Baibulo la Dziko Latsopano lomwe tikugwiritsa ntchito masiku ano. Chikuto ndi masamba amene agwiritsidwe ntchito popanga buku la nyimboli ndi olimba komanso odula kwambiri ndipo kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi ndi umboni woti nyimbo ndi zofunika kwambiri polambira.

M’bale Splane analengezanso kuti nyimbo zingapo ziwonjezeredwa m’bukuli. Anati sipakufunika kudikirira kuti buku la nyimbo latsopano lisindikizidwe kuti tiyambe kuimba nyimbo zatsopanozo koma ziziikidwa pa jw.org zikangotuluka.

Nyimbo zatsopano zitatu zimene anthu a ku Beteli anazikonzekera kwa mlungu umodzi zinaimbidwa pamsonkhanowu. M’bale Splane ndi amene anatsogolera anthu amene anaimba nyimbo yakuti “Ufumu Umene Ukulamulira Kumwamba Ubwere.” Nyimboyi inakonzedwa chifukwa chosangalala kuti Ufumu wa Mulungu wakwanitsa zaka 100 kuyambira pamene unayamba kulamulira. Anthu a ku Beteli omwe anakonzekera nyimboyi atamaliza kuimba, anthu onse amene anali pamsonkhanowu anaimba nawo. Msonkhanowu uli mkati, nthawi ina anthu a ku Beteli aja limodzi ndi ena onse anaimbanso nyimbo ina yatsopano ya mutu wakuti, “Tithandizeni Kukhala Olimba Mtima.”

Kufunsa Mafunso.

Pamsonkhanowu panaonetsedwa vidiyo yosonyeza M’bale Gerrit Lösch wa m’Bungwe Lolamulira akufunsa mafunso mabanja atatu omwe atumikira pabeteli kwa zaka zambiri. Iwo anafotokoza zinthu zambiri zimene aziona zikusintha zomwe ndi umboni wakuti anthu a Mulungu akupita patsogolo. M’bale Lösch ananena kuti Baibulo linalosera kuti zinthu zidzasintha m’gulu la Yehova ndipo analimbikitsa anthu onse kuti apitirize kuyenda ndi gululi.​—Yesaya 60:17.

“N’chifukwa Chiyani Masiku Ano Sitifotokoza Kwambiri Kuti Zinthu Zosiyanasiyana Zotchulidwa M’Baibulo Zimaphiphiritsira Zinazake?”

M’bale Splane anakamba nkhani imene inayankha funso limeneli.

M’mbuyomu tinkanena kuti anthu ambiri okhulupirika amene analembedwa m’Baibulo amaimira magulu a Akhristu okhulupirika masiku ano. Komanso tinkaganiza kuti nkhani zambiri za m’Baibulo zinali maulosi a zinthu zokhudza atumiki a Mulungu a masiku ano. Ndipotu kunena zoona, zinali zosangalatsa kuphunzira nkhani zoterezi. Komano n’chifukwa chiyani masiku ano mabuku athu safotokoza kawirikawiri zakuti zinthu zosiyanasiyana zotchulidwa m’Baibulo zimaphiphiritsira zinazake?

Malemba amasonyeza kuti anthu ena komanso zinthu zina zotchulidwa m’Baibulo zinkaimira munthu kapena chinthu chinachake chofunika kwambiri. M’malemba ena, Baibulo limaneneratu zimene zinthu zinazake zikuimira ndipo ifenso timakhulupirira zimenezo. M’bale Splane ananena kuti: “Koma ngati Baibulo silikunena zimene zinazake zikuimira, ifenso sitikuyenera kunenapo kanthu.” Izi zikusonyeza kuti tikamawerenga Baibulo, tisamagwirizanitse nkhani imene tikuwerengayo ndi mfundo zimene tikungoziganizira. Komanso ngati powerenga Baibulo tikutha nthawi yaitali kuti tipeze kugwirizana kapena kusiyana kwa nkhani imene tikuwerengayo ndi zochitika za masiku ano, sitingaone mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zimene tikuwerengazo komanso zimene tikuphunzirapo. Izi zingachitikire aliyense, kaya amene akuyembekezera kupita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansili.​—Aroma 15:4. *

“Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?”

M’bale Lett ndi amene anakamba nkhaniyi ndipo inasintha zimene tinkakhulupirira pa fanizo la Yesu lokhudza anamwali 10. (Mateyu 25:1-13) Panopa tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mkwati akuimira Yesu ndipo anamwali akuimira otsatira a Yesu okhulupirika omwe ndi odzozedwa. (Luka 5:34, 35; 2 Akorinto 11:2) Fanizoli limanena za masiku otsiriza omwe adzafike pachimake nthawi ya chisautso chachikulu. Yesu atanena za anamwali opusa 5, sankatanthauza kuti otsatira ake odzozedwa ambiri adzakhala osakhulupirika ndipo adzalowedwa m’malo ndi ena. Koma amenewa anali mawu amphamvu owachenjeza. Popeza anamwali 5 anali ochenjera ndipo 5 anali opusa, izi zinasonyeza kuti wodzozedwa aliyense akhoza kusankha kukhala maso ndiponso wokonzeka kapena kukhala wosakhulupirika.

Mogwirizana ndi mfundo yakuti tisamathere nthawi yaitali kuganizira zinthu zimene sizinalembedwe tikamawerenga Baibulo, sichingakhalenso chinthu chanzeru kuganizira zimene mfundo iliyonse ya m’fanizoli ikuimira masiku ano. M’malo mwake, tingachite bwino kuganizira zimene tikuphunzira m’fanizoli. Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” tonsefe tili ndi udindo wowalitsa kuunika kwathu komanso ‘kukhalabe maso.’ (Yohane 10:16; Maliko 13:37; Mateyu 5:16) Palibe munthu amene angatichitire zimenezi. Aliyense akufunika ‘kusankha moyo’ ndipo kuti zimenezi zitheke ayenera kukhalabe paubwenzi wolimba ndi Yehova komanso kumamutumikira mwakhama.​—Deuteronomo 30:19.

“Fanizo la Matalente.”

Nkhani imeneyi inakambidwa ndi M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira. Iye anafotokoza tanthauzo latsopano la fanizo la matalente. (Mateyu 25:14-30) Panopa tikukhulupirira kuti mbuye wotchulidwa m’fanizoli, (kapena kuti Yesu) adzapatsa mphotho akapolo ake (otsatira a Yesu okhulupirika a padziko lapansi omwe ndi odzozedwa) m’tsogolomu akadzabwera n’kuwatenga kupita nawo kumwamba. Pamene ankanena zimene zidzachitikire “kapolo woipa ndi waulesi,” Yesu sankalosera kuti otsatira ake odzozedwa ambiri adzakhala osakhulupirika. Koma amawachenjeza n’cholinga choti apitirize kuchita khama komanso kupewa mtima ndi zochita za kapolo woipa.

Kodi ndi zinthu ziti zimene tingaphunzire m’fanizoli? Mbuye wa m’fanizoli anapatsa akapolo ake chinthu chamtengo wapatali. Mofanana ndi mbuyeyu, Yesu anapatsa otsatira ake ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu, ndipo amaona kuti ntchitoyi ndi yamtengo wapatali. Iye amafuna kuti tonse tizichita khama pogwira ntchitoyi, malinga ndi mmene zinthu zilili pamoyo wathu. M’bale Morris anayamikira onse amene anapezeka pamwambowu chifukwa cha khama lawo pa ntchito za Ufumu.

“Kodi Ndi Ndani Amene Adzaukire Anthu a Mulungu Posachedwapa?”

Uwu unali mutu wochititsa chidwi wa nkhani yomaliza pamwambowu yomwe inakambidwa ndi M’bale Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira. M’nkhaniyi, M’bale Jackson anafotokoza za kuukira anthu a Mulungu kwa Gogi wa ku Magogi.​—Ezekieli 38:14-23.

Kwa zaka zambiri, tinkakhulupirira kuti Gogi ndi dzina limene Satana Mdyerekezi anapatsidwa atathamangitsidwa kumwamba. Komabe M’bale Jackson anafotokoza kuti zimenezi zimabweretsa mafunso ambiri. Mwachitsanzo, pofotokoza za kuwonongedwa kwa Gogi, Yehova analosera kuti Gogiyo adzaperekedwa “kwa mbalame zodya nyama, mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zakutchire kuti mukhale chakudya chawo.” (Ezekieli 39:4) Yehova analoseranso kuti “Gogi pamodzi ndi khamu lake lonse” adzaikidwa m’manda padziko lapansi. (Ezekieli 39:11) Ndiye zingatheke bwanji kuti “mbalame zamitundumitundu ndi zilombo zakutchire” zidye Satana yemwe ndi mzimu? Nanga zingatheke bwanji kuti aikidwe m’manda padzikoli? Baibulo limanena kuti Satana adzatsekeredwa m’phompho kwa zaka 1,000 osati adzadyedwa kapena kuikidwa m’manda. (Chivumbulutso 20:1, 2) Komanso zaka 1,000 zikadzatha, Satana adzamasulidwa ndipo “adzatuluka kukasocheretsa mitundu ya anthu kumakona onse anayi a dziko lapansi. Mitunduyo ndiyo Gogi ndi Magogi,” (Chivumbulutso 20:7, 8) Ndiyeno ngati Gogi ndi Satana, kodi angadzisocheretse yekha?

M’bale Jackson anafotokoza kuti Gogi wa ku Magogi amene Ezekieli analosera sakuimira Satana, koma mgwirizano wa mitundu ya anthu amene adzaukire anthu a Mulungu m’tsogolo muno. N’zosakayikitsa kuti kuukira kwa Gogi ndi chimodzimodzi ndi kuukira kwa “mfumu ya kumpoto” komanso kuukira kwa “mafumu a dziko lapansi.”​—Danieli 11:40, 44, 45; Chivumbulutso 17:12-14; 19:19.

Kodi “mfumu ya kumpoto” ikuimira ndani? Sitinganeneretu, koma chikhulupiriro chathu chimalimba tikamaona Yehova akutithandiza pang’onopang’ono kumvetsa zinthu zimene zidzachitike mtsogolo makamaka pamene zinthuzo zatsala pang’ono kuchitika. Mfundo yakuti anthu a Mulungu adzaukiridwa siyenera kutichititsa mantha chifukwa tikudziwa kuti Gogi wa ku Magogi akadzatiukira, sadzapambana ndipo adzawonongedwa koma anthu a Mulungu adzapulumuka. *

Kumaliza.

M’bale Sanderson analengeza za kutulutsidwa kwa kabaibulo kakang’ono kakuti, Baibulo la Dziko Latsopano. Ananenanso kuti pakukonzedwa Baibulo lomvetsera limene lidzakhale ndi mawu a anthu osiyanasiyana akuwerenga mawu a anthu otchulidwa m’Baibulo. Baibulo longomvetserali lizidzaikidwa pang’onopang’ono pawebusaiti ya jw.org ndipo tidzayamba ndi buku la Mateyu.

M’bale Sanderson analengezanso kuti lemba la chaka cha 2015 lidzakhala Salimo 106:1. Lembali limati: “Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.” Iye analimbikitsa anthu onse kuti tsiku lililonse aziona zinthu zimene Yehova wawachitira n’kumamuthokoza.

Nyimbo yomaliza inali yakuti, “Inu Ndinu Yehova” yomwe ndi nyimbo yachitatu pa nyimbo zathu zatsopano. Abale onse 7 a m’Bungwe Lolamulira anapita kutsogolo n’kukaimba limodzi ndi gulu loimba la pabeteli. Anthu onse amene anali pamwambowu anaimba nawo nyimbo yokomayi. Nyimboyi inali yogwirizana kwambiri ndi mwambo wosaiwalikawu.

^ ndime 22 Nkhaniyi komanso zina ziwiri zinachokera m’nkhani zimene zidzatuluke mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2015.

^ ndime 30 Nkhaniyi inachokera m’nkhani imene idzatuluke mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 2015.