Pitani ku nkhani yake

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Chipangano Chakale?

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Chipangano Chakale?

Inde. A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti mabuku onse a m’Baibulo “anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Timoteyo 3:16) Izi zikutanthauza kuti mabuku onse amene anthu amawatchula kuti Chipangano Chakale ndi Chipangano Chatsopano ndi ochokera kwa Mulungu. Nthawi zambiri a Mboni za Yehova amatchula magawo awiri a m’Baibulowa kuti Malemba Achiheberi ndi Malemba Achigiriki. Izi zimathandiza kuti anthu ena asamaganize kuti mbali zina za m’Baibulo zinatha ntchito.

N’chifukwa chiyani Akhristu amafunikira Chipangano Chakale ndi Chatsopano?

Mulungu anauza mtumwi Paulo kulemba kuti: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.” (Aroma 15:4) Choncho nkhani zimene zili m’Malemba Achiheberi ndi zothandiza kwambiri kwa ife. M’malemba amenewa mulinso mbiri yakale yofunika kwambiri komanso malangizo othandiza.

  • Muli mbiri yakale yothandiza kwambiri. M’Malemba Achiheberi muli nkhani zokhudza mmene Mulungu analengera zinthu komanso zimene zinachitika kuti anthu achimwe. Pakanapanda nkhani zimenezi sitikanadziwa mayankho a mafunso ofunika kwambiri ngati akuti: Kodi tinachokera kuti? N’chifukwa chiyani anthufe timafa? (Genesis 2:​7, 17) Komanso m’Malemba Achiheberi muli nkhani zosonyeza mmene Yehova Mulungu ankachitira zinthu ndi anthu. Anthu amenewa ankakumana ndi zinthu zofanana ndi zimene timakumana nazo.​—Yakobo 5:17.

  • Muli malangizo othandiza kwambiri. M’mabuku a m’Baibulo a Miyambo ndi Mlaliki, omwe ali m’gulu la Malemba Achiheberi, muli malangizo othandiza kwambiri pamoyo wathu. Mwachitsanzo, m’mabukuwa muli malangizo othandiza kuti anthu azikhala ndi banja losangalala (Miyambo 15:17), othandiza kuti asamachite ulesi pa ntchito ndiponso kuti asamagwire ntchitoyo modzipanikiza (Miyambo 10:4; Mlaliki 4:6), komanso muli malangizo othandiza achinyamata kuti akhale ndi moyo wosangalala (Mlaliki 11:9–12:1).

Tingaphunzirenso zinthu zofunika kwambiri m’Chilamulo cha Mose, chomwe chimapezeka mu Tora (mabuku 5 oyambirira m’Baibulo). N’zoona kuti Akhristu satsatira Chilamulo. Komabe m’Chilamulocho muli mfundo zimene zingatithandize kuti tizikhala ndi moyo wosangalala.​—Levitiko 19:18; Deuteronomo 6:​5-7.