Pitani ku nkhani yake

Kodi Mose Ndi Amene Analemba Baibulo?

Kodi Mose Ndi Amene Analemba Baibulo?

Yankho la m’Baibulo

 Mulungu anagwiritsira ntchito Mose polemba mabuku asanu oyambirira a m’Baibulo. Mabuku ake ndi: Genesis, Ekisodo, Levitiko, Numeri ndiponso Deuteronomo. Zikuonekanso kuti Mose ndi amene analemba buku la Yobu ndi Salimo 90. Koma Mose anali m’modzi mwa anthu 40 amene Mulungu anawagwiritsira ntchito polemba Baibulo.