Nyimbo za Broadcasting

Nyimbo zosangalatsa zosonyeza kuyamikira chuma chathu chauzimu.

Moyo wabwino kwambiri

Timasangalala kwambiri tikamathandiza komanso kulimbikitsa ena.

Sindidzasiya

Muzidalira Yehova ndipo musasiye kumutumikira.

Ndasangalala Kuti Sindinagonje

N’chiyani chingathandize achinyamata kuti asatengere zochita za anzawo kusukulu?

Kungomwetulira

Kumwetulira kungatithandize muutumiki komanso pa moyo wathu.

Yehova Wakulandira

Mzimu woyera wa Mulungu ungakuthandizeni kuti mubwerere kwa iye.

Kusangalala ndi Misonkhano

Tikapita ku msonkhano, timasangalala ndi mgwirizano komanso chikondi chomwe abale padziko lonse ali nacho.

Ganizira Nthawiyo

Tikuyembekezera nthawi imene zinthu zonse zidzakhale zabwino.

Tiyendebe

Tipitirizebe kuyenda ndi gulu la Yehova lomwe likupita patsogolo

Madalitso Ophunzira Chinenero China

Kodi mungapeze madalitso otani chifukwa chophunzira chilankhulo china?

Musathamange

Utumiki wathu komanso zinthu zina pamoyo wathu kawirikawiri zimayenda bwino tikamachita zinthu mosapupuluma.

“Khalani Ochereza”

Kodi mungasonyeze kuchereza m’njira ziti?

Tikuthokoza

Yehova amatithandiza ndi mzimu wake woyera, kupirira mavuto ochuluka amene timakumana nawo. Zimenezi zimatichititsa kumuimbira nyimbo zomuthokoza.

Anzanga Apamtima

Kodi mungasankhe bwanji anzanu apamtima?

Zimene Timasankha

Ndi nzeru kumaganizira mmene zosankha zathu zingakhudzire utumiki wathu komanso anthu ena.

Tizikhululukirana

Tiziyesetsa kutsanzira Yehova n’kumakhululukira ena.

Dziko Latsopano Lili Pafupi

Kuyembekezera mwachidwi Paradaiso amene akubwerayu kungatithandize kuti tipirire.

Muziphunzira Kuti Mukhale Olimba

Achinyamata akhoza kukhala olimba mwauzimu ngati atamaphunzira Mawu a Mulungu paokha.

Mawu Anu Adzakhala Mpaka Kalekale

Tiyenera kutamanda Yehova chifukwa choti wasunga Mawu ake kuti anthu aziwagwiritsa ntchito

Zidzatiyendera Tikamapemphera

Kodi tingatani tikakumana ndi mavuto?

Yehova Amandithandiza Kukonza Tsogolo Langa

Tsiku ndi tsiku tizisankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova.

Ndimasunga Malamulo Anu

Zolankhula ndi zochita zathu zizisonyeza kuti timakonda Yehova.

Ndidzadzukanso

Tsanzirani munthu yemwe poyamba anali wakhama potumikira Yehova ndipo akupezanso mphamvu n’kubwerera atakumbukira chikondi chimene mpingo unkamusonyeza.

Ntchito Zanu N’zodabwitsa

Kusangalala ndi mwayi wogwira ntchito ndi Yehova!

Mwana Wanga Wamkazi Wapadera

Pamene zaka zikudutsa, bambo akuona mwana wake wamkazi akukula ndi kuyamba kuona choonadi kuti ndichakechake.

Tisachedwe

Monga atumiki a Yehova, kuwonjezera zochita mu utumiki wathu m’njira iliyonse kungatibweretsere chimwemwe chochuluka.

Yang’ane

Gwiritsani ntchito bwino nthawi yocheza ndi abale ndi alongo.

Chilengedwe Chanu Chimandidabwitsa

Ntchito za manja a Yehova zimatidabwitsa ndipo zimatichititsa kumuimbira.

Zinthu Zofunika

Tiyenera kumapeza nthawi yochitira zinthu zofunika kwambiri—kupemphera, kuphunzira, ndi kudzipereka kwa Mulungu.

Wokondedwa Wanga

Kudalira Yehova Mulungu kudzathandiza kuti banja lanu likhale lolimba!

Malo Amene Adzachititsa Kuti Mulemekezedwe

Ndife osangalala kupereka kwa Yehova malo amene adzachititsa kuti dzina lake lalikulu lilemekezedwe.

Ndikukhulupirireni

Kuphunzira mawu a Mulungu ndi kuganizira zimene tikuphunzirazo kungatithandize kupirira mavuto amene tikukumana nawo pa moyo.

Ndikusintha

Kodi mukufunitsitsa kusintha mmene mumachitira zinthu pa utumiki wanu?

Sangandisiye

Yehova Mulungu wathu sangatisiye!

Kukonda Abale

Palibe gulu lina lililonse padzikoli limene lingafanane ndi Mboni za Yehova pa nkhani yothandizana.

Tisaope

Pamene zinthu zikuvuta pamoyo wathu, tizikumbukira kuti sitili tokha.

Kufufuza

Omwe akufunitsitsa kudziwa Mulungu angafunike kuchita khama pomwe akufufuza za iye.

Mabwenzi Enieni

Kodi tingapeze kuti mabwenzi enieni?

Undidalire

Pamavuto ndi pamtendere, tingadalire mabwenzi enieni.

Yehova Watithandiza Kukhala Amodzi

Ngakhale kuti tili mu dziko loipali, koma tili ndi abale athu okonda mtendere komanso ogwirizana.

Ndithandizeni Ndikhale Wolimba Mtima

Yehova angatithandize kuti tipirire molimba mtima mayesero alionse amene tingakumane nawo.

Ndidzakupatsani Zonse Zomwe Ndingathe

Yehova ndi woyeneradi kumutumikira ndi mtima wathu wonse.

Tsiku Lililonse Lili N’zodetsa Nkhawa Zake

Tikhoza kupeza mtendere ndi chimwemwe ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto.

Ukhale Wolimba Mtima Ndipo Uchite Zinthu Mwamphamvu

Nyimbo yabwino kwambiri yotithandiza kupirira.

Tiziyamikira Chilengedwe cha Mulungu

Muzipeza nthawi yoganizira mozama zinthu zimene Yehova analenga ndipo muzimuthokoza m’pemphero.

Ndife Banja Limodzi

Kuli konse komwe tili, ndife a m’banja la Yehova.

“Menya Nkhondo Yabwino Yosunga Chikhulupiriro”

Tikhoza kukhalabe okhulupirika kwa Yehova ngakhale pomwe tikukumana ndi mavuto.

Yehova Amatithandiza Nthawi Zonse

Yehova amafunitsitsa kutithandiza.

Dziko Latsopano Lomwe Likubwera

Zimene timayerekezera kuona m’maganizo mwathu zikhoza kutichititsa kuona kuti zimene tikuyembekezera ndi zenizeni. Nyimboyi ikutithandiza kuti tiziika maganizo athu onse pa dziko latsopano.

Ndadzipereka Kwa Inu

Chifukwa cha chikondi cha Yehova, timadzipereka mpaka kubatizidwa.

Chikondi Sichitha

Chikondi cha Yehova sichitha. Chimatipatsa chimwemwe ndi kutitonthoza.

Mutulire Yehova

Mukakhala ndi nkhawa, pitirizani kudalira Yehova kuti akupatseni mphamvu komanso akutonthozeni.

Ngati Mwana

Kodi tingakhale bwanji ngati mwana posonyeza chikondi?

Tsimikizani

Tikhoza kutsimikiza mtima kuti Yehova amatikonda, ngakhale pomwe tikukumana ndi mayesero.

Ndikhululuke

Kodi wina wakukhumudwitsani? Kodi mukuvutika kuziiwala? Onani zimene mungachite kuti mukhululuke.

Thamanga

Muzisankha zochita mwanzeru kuti mupambane pampikisano wokalandira moyo.

Sitisiya

Kumanga chikhulupiriro cholimba kumadalira zipangizo zomangira zabwino.

Ndiwe Wekha

Muzisangalala ndi mphatso ya banja imene Yehova anapereka.

Muziteteza Maganizo Anu

Yehova angakuthandizeni kuti muwine nkhondo yolimbana ndi maganizo ofooketsa.

“Kondwerani Nthawi Zonse”

Nyimbo yachisangalalo ikhoza kutikumbutsa zifukwa zambiri zokhalira osangalala.

Ndife Gulu Logwirizana

Timakhalabe gulu limodzi logwirizana, ngakhale pomwe tikukumana ndi zinthu zoyesa chikhulupiriro chathu komanso mavuto.

Gwiritsani Ntchito Mphamvu Zanu Potumikira Yehova

Gwiritsani ntchito mphamvu zanu potumikira Yehova. Simudzanong’oneza bondo!

Chimwemwe Chosatha

Yehova ndi amene amatipatsa chimwemwe ndipo sadzasiya.

Muone

Muzisangalala ndi chiyembekezo chokhudza dziko latsopano.

Muzipeza Mpata Wolambira

Kuchita zambiri potumikira Yehova n’kofunika kwambiri pamoyo wathu.

Ndi Maso a Chikhulupiriro

Ganizirani tsogolo losangalatsa limene Mulungu wakonzera anthu.

Tili M’banja la Yehova

Padakali anthu ena m’dzikoli amene akusakasakabe choonadi. Vidiyoyi ikuthandizani kuona zimene mungachite kuti mupitirize kuthandiza anthu amene ali ngati nkhosawa.

Pamodzi, Timalimba Mtima

Ndi thandizo la Yehova komanso ubale wathu wapadziko lonse tikhoza kupilira mayesero aliwonse.

Ndingapite Kwa Ndani?

Tsanzirani mtumiki wa Yehova wokhulupirika amene akuyesetsa kumvera mawu a Yesu kwa moyo wake wonse.

Yehova Ali Nane

Ndi thandizo la Yehova sitingaope chilichonse.

Tigwirizanenso

Siyani kuganizira zimene ena akulakwirani ndipo muyambirenso kugwirizana

Uziphunzirapo Kanthu Ukalakwitsa

Ukaphunzirapo kanthu pa zimene walakwitsa, udzakhala wolimba kuposa kale.

Moyo Wosatha

Tingakhale ndi moyo wosangalala ndi watanthauzo panopa komanso mtsogolo.

Kudzakhala Mtendere (Nyimbo ya Msonkhano ya 2022)

M’malo momangoganizira za mavuto omwe tikukumana nawo, tiziganiziranso za mtendere umene M’lungu watilonjeza.

Ndimuyandikire

Yehova amachita chidwi ndi anthu amene akufunitsitsa kumuyandikira ndipo satengera zimene anthuwo ankachita m’mbuyomu.

“Sadzachedwa” (Nyimbo ya Msonkhano wa 2023)

Muzitsanzira anthu okhulupirika pamene mukuyembekezera Yehova.

“Timakobidi Tiwiri”

Yehova amayamikira zopereka zanu. Zambiri kaya zochepa.

Amatidziwa Bwino

Yehova amadziwa bwino aliyense payekha ndipo amamvetsa zomwe zili mumtima mwathu.

Tidzamuimbira

Timasangalala ndi mtendere chifukwa chotumikira Yehova.

Tisafooke

Muzidalira Yehova ndi kupitirizabe kulalikira ngakhale pomwe mukuchita mantha.

Ndilimbitse Chikhulupiriro Changa

Limbitsani chikhulupiriro chanu kuti muthane ndi kukaikira.

“M’dziko Labwino”

Kuganizira kwambiri za chiyembekezo chathu kumatithandiza kupirira ngakhale mavuto aakulu.

“Uthenga Wabwino” (Nyimbo ya Msonkhano wa 2024)

Kuyambira kale mpaka pano, anthu akhala akulalikira za uthenga wabwino mosangalala. Ntchitoyi ndi yaikulu kwambiri. Yesu ndi amene amaitsogolera ndipo angelo amathandiza nawo pa ntchitoyi.