Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo za M’Baibulo Zomwe Zingakuthandizeni Ngati Mwachotsedwa Ntchito

Mfundo za M’Baibulo Zomwe Zingakuthandizeni Ngati Mwachotsedwa Ntchito

 Munthu akachotsedwa ntchito akhoza kukumana ndi mavuto aakulu azachuma, kuvutika kusamalira banja lake komanso kuvutika maganizo. Ngati mukulimbana ndi vuto limeneli, mfundo za m’Baibulo zotsatirazi zingakuthandizeni.

  •   Muziuzako ena mmene mukumvera.

     Zimene Baibulo limanena: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.”—Miyambo 17:17.

     Munthu akachotsedwa ntchito, angamakhale wokhumudwa, wosokonezeka maganizo komanso angamadzione kuti ndi wolephera. Koma ukamauza achibale ndi anzako mmene ukumvera mumtima, angakuthandize kukhazikitsa mtima m’malo. Angakuthandizenso kudziwa zoyenera kuchita kuti upezenso ntchito ina.

  •   Muzipewa kuda nkhawa kwambiri.

     Zimene Baibulo limanena: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”—Mateyu 6:34.

     Baibulo limatilimbikitsa kukonzekera zomwe tikufuna kudzachita m’tsogolo. (Miyambo 21:5) Komabe, limatilimbikitsanso kuti tisamadere nkhawa kwambiri zam’tsogolo. Nthawi zambiri timadera nkhawa zinthu zomwe sizichitika n’komwe. Ndi bwino kuika maganizo athu pa zomwe tikuyenera kuchita lero.

     Baibulo lili ndi malangizo othandiza omwe mukhoza kuwagwiritsa ntchito kuti muthe kupirira ngati mukuvutika maganizo. Kuti mumve zambiri, werengani nkhani yakuti “Mungatani Kuti Muchepetse Nkhawa?

  •   Sinthani bajeti yanu.

     Zimene Baibulo limanena: ‘Ndaphunziranso . . . kukhala ndi zochuluka, ndi kukhala wosowa.’—Afilipi 4:12.”

     Sinthani zinthu zina mogwirizana ndi mmene zinthu zilili panopa. Zimenezi zikuphatikizapo mmene mumagwiritsira ntchito ndalama zanu kuti muzigula zinthu zogwirizana ndi kuchuluka kwa ndalama zomwe mumapeza. Muyeneranso kupewa kutenga ngongole zosafunikira.—Miyambo 22:7.

     Kuti mukwanitse kusintha zinthu zina mogwirizana ndi ndalama zomwe mukupeza panopo, werengani nkhani yakuti “Zimene Mungachite Ngati Mukupeza Ndalama Zochepa.”

  •   Muzigwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru.

     Zimene Baibulo limanena: “Pitirizani kuyenda mwanzeru . . . , ndipo muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Akolose 4:5.

     Ngakhale kuti pano simukupitanso kuntchito, tsiku lililonse muyenera kukhala ndi ndandanda yabwino yochitira zinthu. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muzichita zinthu mwadongosolo komanso kuti musamadzione ngati wolephera.

  •   Muzikhala wokonzeka kusintha.

     Zimene Baibulo limanena: “Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa.”—Miyambo 14:23.

     Muzikhala wokonzeka kugwira ntchito ina ngakhale itakhala yosiyana ndi yomwe munkagwira poyamba. Zimenezi zingaphatikizepo kugwira ntchito zooneka zonyozeka kapena zamalipiro ochepa poyerekeza ndi ntchito yanu yoyamba.

  •   Muzichita zinthu mwakhama.

     Zimene Baibulo limanena: “Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo, chifukwa sukudziwa pamene padzachite bwino.”—Mlaliki 11:6.

     Pitirizani kusakasaka ntchito ina. Muziuza anthu ena kuti mukufunafuna ntchito. Mungauze achibale, anzanu, omwe munkagwira nawo ntchito poyamba komanso anthu okhala nawo pafupi. Mutha kulankhula ndi maofesi omwe amapezera anthu wantchito, kufufuza munyuzi ndi m’mapepala omwe amatidwa m’malo osiyanasiyana kapenanso kufufuza pa intaneti. Ndi bwinonso kukasiya makalata ofunsira ntchito m’malo osiyanasiyana.