Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Kodi umphawi ungadzathedi padzikoli?

Kodi Mulungu Adzachita Zotani Kuti Anthu Asamadzavutikenso Ndi Umphawi?Mateyu 6:9, 10.

Chaka chilichonse, anthu mamiliyoni ambiri amafa ndi njala komanso matenda omwe amabwera chifukwa cha umphawi. Ngakhale kuti pali mayiko ena omwe ndi olemera, zikuoneka kuti anthu ambiri akuvutika ndi umphawi. Baibulo limanena kuti anthu akhala akuvutika ndi umphawi kuyambira kalekale.—Werengani Yohane 12:8.

Kuti umphawi udzathe, pakufunika boma lolamulira dziko lonse lapansi limene lizidzapatsa anthu zimene akufunika mosakondera. Boma limeneli lidzafunikanso kuthetsa nkhondo zomwe zimachititsa kuti anthu ambiri akhale mu umphawi. Mulungu watilonjeza kuti adzabweretsa boma lotereli.—Werengani Danieli 2:44.

Kodi ndani adzathetse umphawi?

Mulungu anasankha Yesu kuti adzalamulire dzikoli. (Salimo 2:4-8) Yesu akadzakhala mfumu, adzathandiza anthu osauka omwe amaponderezedwa komanso kuzunzidwa.—Werengani Salimo 72:8, 12-14.

Baibulo linaneneratu kuti popeza Yesu ndi “Kalonga Wamtendere” adzakhazikitsa mtendere komanso chitetezo padziko lonse. Kenako aliyense adzakhala ndi nyumba yakeyake komanso chakudya chokwanira. Anthu adzakhalanso ndi mwayi wogwira ntchito yakumtima kwawo.—Werengani Yesaya 9:6, 7; 65:21-23.