Pitani ku nkhani yake

Kodi Mwambo wa Halowini Unayamba Bwanji?

Kodi Mwambo wa Halowini Unayamba Bwanji?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo silinena chilichonse chokhudza Halowini. Anthu ambiri m’mayiko ena amakondwerera holide ya Halowini pa 31 October chaka chilichonse. Komabe, mmene mwambowu unayambira komanso zomwe zimachitika pamwambowu zimasemphana ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa.

Zimene Zili Munkhaniyi

 Mbiri ya Halowini komanso zomwe zimachitika pamwambowu

  •   Mwambo wa Samhain: Mogwirizana ndi zomwe The World Book Encyclopedia imanena, Halowini inachokera kumwambo wachikunja wa Samhain “womwe unkachitidwa kalekale ndi anthu otchedwa a Celtic, pafupifupi zaka zoposa 2,000 zapitazo.” Buku linanso linanena kuti: “A Celtic ankakhulupirira kuti panthawiyi, anthu omwe anafa amakakumana ndi anthu amoyo. Choncho pamwambo wa Samhain, anthu amoyo amatha kuyenderana ndi anthu omwe anamwalira.”—Onani kamutu kakuti, “ N’chifukwa chiyani mwambowu umadziwika ndi dzina loti Halowini?

  •   Zovala, maswiti ndi mphatso zina: Mogwirizana ndi zomwe ena ananena, akuti pochita mwambowu, a Celtic ankavala zovala zomwe zinkawapangitsa kuoneka ngati mizukwa. Iwo ankachita zimenezi ndi cholinga choti mizimu yomwe inkangoyendayenda, “isokonezeke n’kuwasiya osawavulaza poganiza kuti ali m’gulu lawo.” Enanso ankapereka maswiti kwa mizimuyo kuti isawavulaze. a

     M’zaka za m’ma 500 C.E. kukafika mu 1500 C.E., atsogoleri a Tchalitchi cha Katolika anayamba kutengera miyambo yachikunja n’kuyamba kulimbikitsa Akhristu awo kuti azipita kunyumba za anthu atavala ngati mizukwa n’cholinga choti azikapempha mphatso.

  •   Mizukwa, mavampaya, nkhandwe komanso mfiti: Kwa zaka zambiri, anthu akhala akukhulupirira kuti zinthu zimenezi zimagwirizana ndi mizimu yoipa. Buku lina linanena kuti zinthuzi “ndi mizimu yamphamvu komanso yoopsa kwambiri” ndipo “zimagwirizana ndi imfa, anthu akufa kapena mantha omwe anthu amakhala nawo chifukwa choopa kufa.”—Halloween Trivia.

  •   Maungu a Halowini: Kalekale ku Britain, anthu “ankayenda khomo ndi khomo kukapempherera anthu omwe anamwalira ndipo akatero ankayembekezera kupatsidwa chakudya ngati malipiro.” Panthawiyo ankatenganso “makandulo omwe ankawaika m’zomera zina zokhala ngati mbatata zobulungira zomwe ankazigoba mkati. Makandulowo ankaimira moyo wa munthu amene watsekeredwa kupuligatoliyo.” (Halloween—From Pagan Ritual to Party Night) Mabuku ena amati makandulowo ankathandiza pofuna kuthamangitsa mizimu yoipa. M’zaka za m’ma 1800, ku North America anayamba kugwiritsa ntchito maungu m’malo mwa zomera zija chifukwa choti maungu analipo ambiri komanso anali osavuta kuwagoba.

 Kodi pali vuto lililonse ndi mmene Halowini inayambira?

 Inde. Ngakhale kuti anthu ena amaona kuti kuchita mwambo wa Halowini kulibe vuto lililonse, komabe zomwe zimachitika pamwambowu zimatsutsana kwambiri ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa. Mwambo wa Halowini unachokera ku zikhulupiriro zabodza zonena za akufa komanso mizimu yosaoneka kapena kuti ziwanda.

 Taonani mavesi otsatirawa omwe akusonyeza mmene Mulungu amaonera zikhulupiriro zogwirizana ndi mwambo wa Halowini:

  •   “Pakati panu pasapezeke munthu . . . aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, . . . kapena aliyense wofunsira kwa akufa.”—Deuteronomo 18:10-12.

     Tanthauzo lake: Mulungu samasangalala ndi aliyense amene amafuna kulankhulana ndi akufa kapena amene amayesa kupeza njira zilizonse zolankhulirana ndi anthu omwe anamwalira.

  •   “Akufa sadziwa chilichonse.”—Mlaliki 9:5.

     Tanthauzo lake: Popeza akufa sadziwa chilichonse, sangathe kulankhulana ndi anthu omwe ali moyo.

  •   “Sindifuna kuti inu muziyanjana ndi ziwanda. Simungamwe kapu ya Ambuye, mukamweranso kapu ya ziwanda.”—1 Akorinto 10:20, 21, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

     Tanthauzo lake: Onse omwe amafuna kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ayenera kupewa kuchita zinthu ndi ziwanda mwanjira iliyonse.

  •   “Musasunthike polimbana ndi zochita zachinyengo za Mdyerekezi, chifukwa sitikulimbana ndi anthu . . . koma ndi . . . makamu a mizimu yoipa.”—Aefeso 6:11, 12.

     Tanthauzo lake: Akhristu ayenera kupewa kuchita zinthu zogwirizana ndi mizimu yoipa ndipo sayenera kuchita chilichonse chosonyeza kuti akusangalala nayo.

a Werengani buku lakuti, Halloween: An American Holiday, an American History, tsamba 4.