Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | YOSEFE

“Kodi Mulungu Sindiye Amamasulira Maloto?”

“Kodi Mulungu Sindiye Amamasulira Maloto?”

TSIKU lina Yosefe, yemwe anali ku Iguputo, ankayenda mkati mwa ndende, thukuta lili kamukamu. Pa tsikuli kunali dzuwa loswa mtengo moti mkati mwa ndendemo munkatentha kwambiri. Yosefe anali atakhala m’ndendeyi kwa nthawi yaitali ndipo ankaidziwa bwino moti kunkangokhala ngati kwawo. Akaidi ena onse ankamulemekeza kwambiri. Koma ngakhale zinali choncho, nayenso anali mkaidi.

Yosefe ayenera kuti ankakumbukira zomwe zinkachitika kwawo pa nthawi yomwe anali ndi ufulu wopita kulikonse kumene akufuna. Kwawo kunali ku Heburoni ndipo ankaweta nkhosa za bambo ake, m’mapiri. Ali ndi zaka 17 bambo ake, a Yakobo, anamutuma kuti akaone azichimwene ake omwe ankadyetsa nkhosa kudera linalake, kutali ndi kwawo. Komabe azichimwene akewo ankamuchitira nsanje ndipo ankafuna kumupha. Kenako anangomugulitsa ngati kapolo kwa amalonda. Amalondawo anapita naye ku Iguputo n’kumugulitsa kwa Potifara yemwe anali nduna ya panyumba ya Farao. Yosefe anayamba kugwira ntchito m’nyumba ya Potifara ndipo Potifarayo ankamukonda komanso kumukhulupirira kwambiri. Koma kenako mkazi wa Potifara anamunamizira kuti amafuna kum’gwiririra. Zimenezi ndi zomwe zinachititsa kuti aponyedwe m’ndende. *Genesis chaputala 37 ndi 39.

Pa nthawiyi n’kuti Yosefe ali ndi zaka 28 ndipo panali patatha zaka zoposa 10 ali kapolo komanso mkaidi. Poyamba ankaganiza kuti mavuto ake sapita patali. Koma tsopano anayamba kudzifunsa kuti, ‘Koma ine ndidzatuluka m’ndende muno? Nanga kodi ndidzawaonanso bambo anga ndi mng’ono wanga Benjamini? Ndikhala kundende kuno mpaka liti?

Kodi inunso munayamba mwamva ngati mmene Yosefe ankamveramu? Zoipa zina zimene zimatichitikira, zimakhala zoti tili ana sitinkaganiza n’komwe kuti zingadzatichitikire. Komanso nthawi zina zimaoneka ngati palibe chiyembekezo choti mavuto omwe tikukumana nawo angathe. Nthawi zinanso angakhale ovuta kuwapirira. Choncho tiyeni tione zimene tikuphunzira kwa Yosefe, yemwe anali wokhulupirika.

“YEHOVA ANAPITIRIZABE KUKHALA NDI YOSEFE”

Yosefe ankadziwa kuti Mulungu wake, Yehova, sanamutaye ndipo zimenezi zinkamuthandiza kuti azipirira. Ngakhale kuti anali m’ndende komanso kudziko lachilendo, Yehova ankamudalitsa. Baibulo limati: “Yehova anapitirizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha. Ndipo anachititsa mkulu wa ndende kum’konda Yosefe.” (Genesis 39:21-23) Mulungu anapitiriza kudalitsa Yosefe chifukwa anali wakhama. Ayenera kuti ankalimba mtima poona kuti Yehova anali naye.

Mwina Yosefe ankadzifunsa kuti, ‘Kodi cholinga cha Yehova n’choti ndikhale m’ndende muno mpaka kalekale?’ Iye sankadziwa yankho la funsoli, komabe anapitiriza kupemphera kwa Mulungu kuti amukumbukire. Nthawi zambiri Mulungu amayankha mapemphero a atumiki ake m’njira yomwe iwo sakuiganizira n’komwe. Zimenezi n’zimene zinachitikiranso Yosefe. Tsiku lina, pandendepo panabwera anthu awiri ndipo nkhani ya kubwera kwawoko inali m’kamwam’kamwa. Anthuwa anali ndi udindo wapamwamba kunyumba kwa Farao. Wina anali mkulu wa ophika mikate ndipo winayo anali mkulu wa operekera chikho.Genesis 40:1-3.

Ndiyeno mkulu wa asilikali olondera mfumu anapatsa Yosefe udindo woti aziyang’anira anthuwo. * Tsiku lina, anthu awiriwa analota maloto odabwitsa kwambiri. Kutacha, ankaoneka ankhawa posadziwa tanthauzo la malotowo. Yosefe atawaona, anazindikira kuti akuda nkhawa ndi zinazake ndipo anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani nkhope zanu zili zachisoni lero?” (Genesis 40:3-7) Popeza Yosefe anali munthu wokoma mtima, n’kutheka kuti anthuwa anaona kuti angathe kumasuka n’kumuuza chomwe chikuwadetsa nkhawa. Yosefe sanadziwe kuti zimene akambirane ndi anthuwa chikhala chiyambi cha kusintha kwa moyo wake. Choncho tingachite bwino kutengera chitsanzo chake. Mwina tingadzifunse kuti: ‘Kodi ineyo ndimalankhula komanso kuchita zinthu zosonyeza kuti ndimadera nkhawa ena?’

Yosefe ankalemekeza akaidi anzake ndipo ankawachitira zinthu mokoma mtima

Anthuwa anafotokozera Yosefe kuti ali ndi chisoni chifukwa cha maloto odabwitsa omwe analota komanso chifukwa choti ankaona kuti palibe amene angamasulire malotowo. Anthu a ku Iguputo ankakhulupirira kwambiri maloto ndipo odziwa kumasulira maloto ankapatsidwa ulemu kwabasi. Koma anthu awiriwa sankadziwa kuti maloto awo anali ochokera kwa Yehova, Mulungu wa Yosefe. Komabe Yosefe anadziwa zimenezi. Choncho anati: “Kodi Mulungu sindiye amamasulira maloto? Tandifotokozerani malotowo.” (Genesis 40:8) Zimene Yosefe ananenazi n’zofunika kwambiri kwa tonsefe ngati tikufuna kumvetsa bwino zimene Baibulo limaphunzitsa. Tiyenera kukhala odzichepetsa podziwa kuti Mulungu ndi amene angatithandize kulimvetsa. Tiyeneranso kupewa kumangomasulira za m’mutu mwathu pofuna kuti anthu azititama kuti timadziwa Baibulo.1 Atesalonika 2:13; Yakobo 4:6.

Woperekera chikho uja ndi amene anayamba kufotokozera Yosefe maloto ake. Ananena kuti analota mtengo wa mpesa wokhala ndi nthambi zitatu zomwe zinabereka mphesa. Kenako mphesa zija zinapsa ndipo iye anazifinyira m’chikho n’kuchipereka kwa Farao. Nthawi yomweyo, Yehova anathandiza Yosefe kudziwa tanthauzo la malotowa. Yosefe anauza woperekera chikhoyo kuti: “Nthambi zitatuzo zikuimira masiku atatu. Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa. Adzakubwezera ndithu pa ntchito yako yakale.” Nkhope ya woperekera chikhoyo inachita kuonekeratu kuti wasangalala kumva zimenezi. Kenako Yosefe anamuuza kuti: “Chonde, udzandikomere mtima ponditchula kwa Farao.” Anamufotokozeranso kuti anapezeka ku Iguputo chifukwa choti anabedwa kwawo ndipo anaikidwa m’ndende ngakhale kuti sanalakwe chilichonse.Genesis 40:9-15.

Wophika mikate uja ataona kuti Yosefe wamasulira zabwino, nayenso anauza Yosefe kuti amuuze tanthauzo la maloto omwe analota. Anati analota atasenza nsengwa zitatu za mikate ndipo mbalame zinkadya mikateyo. Yehova anathandizanso Yosefe kudziwa tanthauzo la malotowa. Koma tanthauzo la malotowa silinali labwino. Yosefe anauza wophika mikateyo kuti: “Kumasulira kwake ndi uku: Nsengwa zitatuzo zikuimira masiku atatu. Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa n’kukudula mutu. Adzakupachika pamtengo, ndipo mbalame zidzadya nyama yako ndithu.” (Genesis 40:16-19) Apatu Yosefe ananena uthenga wochokera kwa Mulungu, wabwino komanso wachiweruzo. Anachita zimenezi mopanda mantha ndipo izi n’zimenenso atumiki a Mulungu amachita.Yesaya 61:2.

Patatha masiku atatu, zimene Yosefe ananena zinachitikadi. Farao anakonza phwando lokumbukira kubadwa kwake. Anthu osalambira Mulungu ndi amene ankachita phwando lokumbukira tsiku la kubadwa. Pa tsikuli, Farao anapereka chiweruzo kwa antchito ake awiri aja. Mkulu wa ophika mikate uja anaphedwadi ndipo mkulu wa operekera chikho anabwezeretsedwa pa udindo wake. Koma n’zomvetsa chisoni kuti woperekera chikhoyu sanakumbukirenso za Yosefe.Genesis 40:20-23.

‘YEMWE ANENE NDI MULUNGU OSATI INE’

Zaka ziwiri zinadutsa ndipo izi ziyenera kuti zinali zowawa kwambiri kwa Yosefe. (Genesis 41:1) Yehova atamuthandiza kudziwa tanthauzo la maloto a anthu awiri aja, Yosefe ayenera kuti anaganiza kuti nthawi yoti atuluke m’ndende yatsala pang’ono. N’kutheka kuti kukacha, ankaganiza kuti ‘mwina ndituluka lero.’ Koma ayi ndithu anadabwa kuona kuti masiku akupita koma palibe chikuchitika. Zaka ziwiri zimenezi ziyenera kuti zinali nthawi yaitali kwambiri kwa Yosefe. Komabe m’malo momangokhalira kudandaula, Yosefe anapitirizabe kukhulupirira Yehova komanso kumudalira kwambiri. Zimenezi zinachititsa kuti chikhulupiriro chake chilimbe.Yakobo 1:4.

Aliyense ayenera kuyesetsa kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba makamaka masiku ano, pomwe zinthu zafika poipa kwambiri. Kuti tipirire mavuto tiyenera kukhala olimba mtima komanso odekha. Tiyeneranso kukhala ndi mtendere wa mumtima umene Yehova amapereka. Nafenso Yehova angatithandize kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba komanso kuti tisamangoganizira za mavuto athu.Aroma 12:12; 15:13.

Woperekera chikho uja anaiwala Yosefe koma Yehova sanamuiwale. Tsiku lina Yehova analotetsa Farao maloto awiri. Poyamba analota ng’ombe 7 zokongola ndiponso zonenepa zikutuluka mumtsinje wa Nailo. Kenako munatulukanso ng’ombe zina 7 zonyansa komanso zowonda. Ndiyeno ng’ombe zowondazo zinayamba kumeza ng’ombe zonenepa zija. Kenako Farao analota ngala 7 za tirigu, zazikulu komanso zokhwima bwino, zikutuluka paphesi limodzi. Koma kenako anaonanso ngala zina 7. Ngala zachiwirizi zinali zonyala komanso zowauka ndi mphepo ndipo kenako zinayamba kumeza ngala zabwino zija. Kutacha, Farao anayamba kuvutika maganizo posadziwa tanthauzo la malotowa. Choncho anaitanitsa anthu onse anzeru komanso amatsenga kuti amuuze tanthauzo la malotowo, koma onse analephera. (Genesis 41:1-8) Sitikudziwa ngati anthuwa anasoweratu chonena kapena ngati ankamasulira zosiyana. Zimenezi zinakhumudwitsa kwambiri Farao chifukwa ankafunitsitsa kudziwa tanthauzo la malotowo.

Pa nthawiyi ndi pamene woperekera chikho uja anakumbukira Yosefe. Anakumbukiranso kuti sanachite zimene Yosefe anamupempha zija ndipo anadziimba mlandu chifukwa cha zimenezi. Choncho, anauza Farao kuti zaka ziwiri m’mbuyomo ali kundende, kunali mnyamata wina yemwe anamasulira maloto molondola. Atangomva zimenezi, Farao anatumiza anthu kuti akatenge Yosefe.Genesis 41:9-13.

Kodi mukuganiza kuti Yosefe anamva bwanji anthuwa atafika kudzamutenga? Nthawi yomweyo anasintha zovala komanso anameta tsitsi ndi ndevu zake. N’kutheka kuti anameta mpala chifukwa ndi mmene anthu a ku Iguputo ankametera. Ayenera kuti anapempheranso kwa Yehova kuti amuthandize kukalankhula molimba mtima ndi Farao. Kenako anapita kunyumba yachifumu ya Farao. Baibulo limati: “Ndiyeno Farao anauza Yosefe kuti: ‘Ine ndalota maloto, ndipo palibe munthu amene wakwanitsa kuwamasulira. Koma ndamva kuti iweyo ukamva maloto umatha kumasulira.’” Yosefe anamuyankha kuti: “Yemwe anene uthenga wokhudza moyo wa inu Farao ndi Mulungu osati ine.” (Genesis 41:14-16) Apanso Yosefe anasonyeza kuti anali wodzichepetsa komanso ankakhulupirira Mulungu.

Yosefe anauza Farao kuti amene amasulire maloto ake ndi Mulungu osati iyeyo

Yehova amasangalala ndi anthu odzichepetsa komanso okhulupirika. N’chifukwa chake anathandiza Yosefe kudziwa tanthauzo la maloto a Farao. Koma sanathandize anthu anzeru komanso amatsenga aja. Yosefe ananena kuti maloto a Farao tanthauzo lake linali limodzi ndipo Yehova anamulotetsa kawiri pofuna kusonyeza kuti tanthauzo la malotowo ndi ‘lotsimikizirika.’ Ng’ombe zonenepa komanso ngala za tirigu zooneka bwino, zinkaimira zaka 7 zomwe mu Iguputo mudzakhale chakudya cha mwanaalirenji. Pomwe ng’ombe zowonda komanso ngala zosaoneka bwino zinkaimira zaka 7 za njala zomwe zidzabwere pambuyo pa zaka za chakudya chambirizo. Njalayi idzachititsa kuti zisadziwikenso kuti m’dzikomo munali chakudya chambiri.Genesis 41:25-32.

Farao anazindikira kuti Yosefe wamasuliradi molondola. Ndiye kodi pamenepa akanatani? Yosefe anafotokozera Farao zomwe angachite kuti pa nthawi ya njalayi asadzasowe mtengo wogwira. Anamuuza kuti apeze munthu “wozindikira ndi wanzeru” kuti aziyang’anira ntchito yosonkhanitsa zakudya munkhokwe pa zaka 7 za chakudya chambiri. Chakudyachi chinali choti chidzagwiritsidwe ntchito pa nthawi ya njala. (Genesis 41:33-36) Yosefe ankadziwa kuti angathe kugwira ntchitoyi. Koma popeza anali wodzichepetsa komanso wachikhulupiriro, sanauze Farao kuti asankhe iyeyo. Munthu amene amakhulupirira Mulungu, amakhala wodzichepetsa ndipo samadziona kuti amachita bwino zinthu kuposa ena. Amakhala wodekha ndipo amadalira Yehova.

“KODI PANGAPEZEKENSO MUNTHU WINA WONGA UYU?”

Farao ndi antchito ake onse anaona kuti Yosefe wanena zanzeru. Farao anadziwanso kuti Yehova ndi amene wathandiza Yosefe kuti anene zimenezi. Choncho anauza ogwira ntchito kunyumba yake yachifumu kuti: “Kodi pangapezekenso munthu wina wonga uyu, wokhala ndi mzimu wa Mulungu?” Kenako anauza Yosefe kuti: “Popeza kuti Mulungu wakudziwitsa zonsezi, palibenso munthu wina wozindikira ndi wanzeru ngati iwe. Iweyo ukhala woyang’anira nyumba yanga, ndipo anthu anga onse azimvera iweyo. Ine ndikhala wokuposa pa ufumu wokha.”Genesis 41:38-41.

Farao anachitadi zomwe ananenazi. Kenako anapatsa Yosefe malaya amtengo wapatali, tcheni chagolide komanso mphete yake yachifumu. Anamupatsanso galeta lachifumu kuti azitha kuyendera kulikonse m’dzikolo pogwira ntchito yake. (Genesis 41:42-44) Zinthutu zinasintha mwadzidzidzi pa moyo wa Yosefe. Pa tsikuli, anadzuka ali mkaidi koma anagona ali wachiwiri kwa mfumu. Apatu n’zoonekeratu kuti Mulungu anadalitsa Yosefe chifukwa choti anali wokhulupirika. Yehova ankaona zinthu zonse zopanda chilungamo zomwe zinkachitikira Yosefe. Ndipo anazithetsa pa nthawi yoyenera komanso m’njira yabwino. Yehova anathandiza Yosefe pa nthawi yoyenera koma anaganiziranso zomwe angachite kuti adzapulumutse Aisiraeli pa nthawi ya njala. M’nkhani ina yomwe idzatuluke mu Nsanja ya Olonda kutsogoloku, tidzaona mmene Yehova anachitira zimenezi.

Ngati mukukumana ndi mavuto ndipo akuoneka ngati sadzatha, musataye mtima. Kumbukirani zomwe zinachitikira Yosefe. Yosefe anadalitsidwa chifukwa anali wokoma mtima, wodzichepetsa, wopirira komanso ankakhulupirira kwambiri Mulungu.

^ ndime 4 Onani nkhani zakuti, “Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo” mu Nsanja ya Olonda ya August 1 ndi ya November 1, 2014.

^ ndime 10 Anthu akale a ku Iguputo ankakonda kwambiri mikate komanso makeke. Ankaphika mikate komanso makeke a mitundu yosiyanasiyana yoposa 90. Choncho mkulu wa ophika mikateyu anali munthu wotchuka kwambiri. Komanso mkulu wa operekera chikhoyu ankayang’anira anthu ogwira ntchito panyumba ya mfumu. Anthuwa ankaonetsetsa kuti vinyo kapena mowa umene unkaperekedwa kwa Farao unali wabwino kwambiri. Ankaonetsetsanso kuti zinthuzi sizinathiridwe poizoni ndi anthu ofuna kupha mfumu, chifukwa ziwembu zoterezo zinkachitikachitika. Nthawi zambiri mkulu wa operekera chikho ankakhalanso mlangizi wa mfumu.