Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO | YOSEFE

“Ndingachitirenji Choipa Chachikulu Chonchi N’kuchimwira Mulungu?”

“Ndingachitirenji Choipa Chachikulu Chonchi N’kuchimwira Mulungu?”

GULU la amalonda lomwe linagula Yosefe linali litatsala pang’ono kufika ku Iguputo ndipo linkadutsa m’mbali mwa mtsinje wa Nailo. Yerekezani kuti mukuona anthuwa akuyenda motsogozana limodzi ndi ngamila zawo ndipo akumva kulira kwa mbalame za m’madzi. Mbalame zina zikuuluka chifukwa chodzidzimutsidwa ndi phokoso la amalondawo. Njira imene anthuwa anadutsa inali yopita kutauni ina ya ku Iguputo. Pa nthawiyi Yosefe anayamba kuona kuti wafika m’dziko lachilendo. Iye anaona kuti nyengo ya kuderali inali yotentha komanso ankamva kafungo ka maluwa ndi zomera za m’madzi. Zimenezi zinapangitsa kuti ayambe kukumbukira kwawo ku Heburoni, komwe nyengo yake inali yosiyana kwambiri ndi ku Iguputo.

Ndiyeno yerekezani kuti mukumva phokoso la anyani akulira m’mitengo ikuluikulu. Pa ulendowu, gulu la amalondali linkakumana ndi anthu osiyanasiyana. Koma Yosefe sankamva chinenero chimene anthuwa ankalankhula. Choncho ayenera kuti akazindikira tanthauzo la mawu enaake ankawasunga kuti aziwakumbukira chifukwa ankadziwa kuti basi sadzapitanso kwawo.

Mavuto amene Yosefe ankakumana nawowa anali oposa msinkhu wake chifukwa pa nthawiyi n’kuti ali ndi zaka 17 kapena 18 zokha. Mavuto onsewa anayamba chifukwa choti abale ake ankamuchitira nsanje popeza bambo awo ankamukonda kwambiri. Choncho iwo ankafuna kumupha koma kenako anangomugulitsa. (Genesis 37:2, 5, 18-28) Amalondawa anayenda ulendowu kwa milungu ingapo ndipo tsopano anali atatsala pang’ono kufika pamalo ogulitsira malonda. Onse chimwemwe chinali chitadzaza tsaya chifukwa ankaona kuti apeza ndalama zambiri akagulitsa Yosefe komanso katundu wina amene anatenga. Kodi n’chiyani chinathandiza Yosefe kuti alimbe mtima pa nthawi yovutayi? Nanga chitsanzo chake chingatithandize bwanji kuti tizikhalabe ndi chikhulupiriro tikakumana ndi mavuto?

“YEHOVA ANAKHALABE NDI YOSEFE”

Baibulo limanena kuti: “Tsopano Yosefe uja, Aisimaeli anapita naye ku Iguputo, ndipo kumeneko anakam’gulitsa kwa Potifara. Potifara anali Mwiguputo, yemwe anali nduna ya panyumba ya Farao, komanso mkulu wa asilikali olondera mfumu.” (Genesis 39:1) Lembali likutithandiza kuganizira mmene Yosefe ankamvera mumtima mwake chifukwa likuti anagulitsidwanso kachiwiri. Ankangodziona ngati katundu wachabechabe woti anthu akhoza kumugulitsa nthawi iliyonse imene afuna. Taganizirani mmene ankamvera pamene Potifara anamutenga n’kumapita naye kunyumba kwake kudutsa m’njira yomwe munali anthu pikitipikiti. Ndipotu m’mbali mwa njirayi munali masitolo ambirimbiri.

Atafika kunyumba ya Potifara, zimene Yosefe anaona zinali zachilendo zokhazokha. Iye anali asanaonepo nyumba yotero chibadwireni. Kuyambira ali mwana, ankakhala m’mahema ndipo ankangokhalira kusamuka limodzi ndi nkhosa zawo. Popeza Potifara anali wolemera, anali ndi chinyumba chachikulu kwambiri komanso chokongola. Akatswiri ofukula zinthu zakale amanena kuti anthu a ku Iguputo ankakhala ndi minda ya maluwa yokongola kwambiri. M’mbali mwa mindayi ankadzalamo mitengo komanso mkati mwake ankakumbamo madamu omwe ankadzalamo zomera zina za m’madzi. Nyumba zina ankazimanga pakati pa minda ya maluwa ndipo izi zinkapangitsa kuti m’nyumbamo muzilowa kamphepo kayaziyazi. Nyumbazi zinkakhala ndi mawindo ambiri, zipinda zogona zambiri komanso chipinda chodyera chachikulu. Ankamanganso nyumba zogona antchito.

 Kodi zimenezi zinagometsa Yosefe moti anaiwala kwawo? Ayi. Ndipotu zinangomupangitsa kuti azikumbukira kwambiri kwawo. Anthu a ku Iguputo anali achilendo kwa iye chifukwa cha chinenero chawo, mmene ankavalira komanso chipembedzo chawo. Ankalambira milungu yonyenga yambirimbiri, ankakhulupirira mizimu, ankachita zamatsenga komanso ankakhulupirira kuti munthu akamwalira amakakhala ndi moyo kwinakwake. Koma pali chinthu chimodzi chimene chinathandiza Yosefe kuti asamaone ngati ali yekhayekha. Baibulo limanena kuti: “Yehova anakhalabe ndi Yosefe.” (Genesis 39:2) N’kutheka kuti Yosefe ankapemphera kwa Yehova n’kumuuza zakukhosi kwake chifukwa Baibulo limati: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye.” (Salimo 145:18) Kodi Yosefe ankachitanso chiyani chomwe chinamuthandiza kuti azikondabe Mulungu wake?

Yosefe anapewa kumangoganizira za mavuto amene ankakumana nawo ndipo ankagwira ndi mtima wonse ntchito yomwe anapatsidwa. Zimenezi zinapangitsa kuti Yehova amudalitse ndipo abwana ake anayamba kumukonda kwambiri. Potifara anaona kuti Yehova ankadalitsa kwambiri Yosefe. Ndipo n’zosakayikitsa kuti zimenezi zinapangitsa kuti zinthu ziziyenda bwino panyumba ya Potifara. Pamapeto pake Potifara anayamba kukhulupirira kwambiri Yosefe moti anasiya chilichonse m’manja mwake.—Genesis 39:3-6.

Yosefe ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa achinyamata amene amatumikira Mulungu chifukwa nawonso amakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Akakhala kusukulu, nthawi zina amaona kuti ali okha chifukwa anzawo amachita zinthu zosiyana ndi zimene iwowo amakhulupirira. Mwachitsanzo, anthu ambiri amapanga zamizimu komanso amaona kuti moyo ulibe cholinga chenicheni. Ngati nanunso mukukumana ndi mavuto ngati amenewa, dziwani kuti Yehova sanasinthe. (Yakobo 1:17) Iye amadalitsa anthu okhulupirika komanso amene amachita zinthu mwakhama. Inunso mukamachita zimenezi, Mulungu adzakudalitsani kwambiri.

Baibulo limanena kuti Yosefe anapitiriza kukula ndipo anali “wokongola m’maonekedwe ndi wa thupi loumbika bwino.” Komatu zimenezi zinamubweretsera mavuto chifukwa munthu akakhala wokongola, nthawi zambiri anthu amamusilira.

Mkazi wa Potifara anayamba kusirira Yosefe

“IYE SANAMVERE”

Yosefe ankaona kuti kukhulupirika ndi khalidwe lofunika kwambiri koma mkazi wa Potifara sankaona choncho. Posonyeza umboni wa zimenezi, Baibulo limanena kuti: “Mkazi wa mbuyake anayamba kuyang’ana Yosefe momusirira, moti anali kumuuza kuti: ‘Ugone nane.’” (Genesis 39:7) Kodi Yosefe anakopeka ndi mkazi wolambira milungu yonyengayu? Baibulo silisonyeza kuti Yosefe analibe chilakolako cha kugonana chomwe chimakhala champhamvu munthu akakhala wachinyamata. Ndipotu mkazi wa Potifara ayenera kuti anali wokongola komanso wolemekezeka chifukwa mwamuna wake anali nduna ya panyumba ya Farao ndipo anali wolemera kwambiri. Kodi Yosefe anaganiza kuti palibe  vuto kugona ndi mkazi wa Potifara bola ngati mwamuna wake atapanda kudziwa? Kodi anakopeka ndi zimene mkaziyu akanamupatsa akanagona naye?

Kunena zoona, sitingadziwe zinthu zonse zimene Yosefe ankaganiza pa nthawiyi. Komabe tingathe kudziwa maganizo ake pa nkhaniyi poona zimene anayankha mkazi wa Potifara. Iye anati: “Chifukwa cha ine, mbuye wanga sadera nkhawa za chilichonse m’nyumba muno, ndipo chilichonse chimene iye ali nacho wachipereka m’manja mwanga. M’nyumba muno mulibe woyang’anira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi n’kuchimwira Mulungu?” (Genesis 39:8, 9) Yerekezani kuti mukumuona Yosefe akulankhula mawu amenewa motsimikiza komanso molimba mtima. Zinkamunyansa kwambiri akaganizira zinthu zoipa zimene mkaziyu ankamukakamiza kuti achite. N’chifukwa chiyani zinkamunyansa?

Kumbukirani kuti Yosefe ananena kuti mbuye wake ankamudalira. Potifara anasiya chilichonse cha m’nyumba yake m’manja mwa Yosefe, kupatulapo mkazi wake. Yosefe akanagona ndi mkazi wa mbuye wake zikanapangitsa kuti mbuye wakeyo asiye kumudalira. Koma chifukwa chachikulu chimene anakanira kugona ndi mkaziyu chinali chakuti sankafuna kuchimwira Mulungu wake, Yehova. Makolo ake anamuphunzitsa mmene Mulungu amaonera ukwati komanso kukhala wokhulupirika m’banja. Pamene Yehova ankayambitsa ukwati, anaperekanso malangizo a mmene banjalo liyenera kukhalira. Mwamuna ndi mkazi wake anayenera kukhala “thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Anthu amene sanatsatire malangizo amenewa anakhumudwitsa Mulungu. Mwachitsanzo, iye anatsala pang’ono kulanga anthu amene ankafuna kugonana ndi mkazi wa Abulahamu komanso mkazi wa Isaki. Azimayi onsewa anali agogo ake a Yosefe. (Genesis 20:1-3; 26:7-11) Yosefe anamvetsa bwino zimene makolo ake anamuphunzitsazi ndipo ankayesetsa kuzitsatira pa moyo wake.

Koma mkazi wa Potifara sanasangalale ndi zimene Yosefe anamuyankha chifukwa anaona kuti Yosefe yemwe anali kapolo wake, akumukana mochititsa manyazi. Komanso Yosefe anamuuza kuti zimene ankamukakamiza kuti achitezi chinali “choipa chachikulu.” Ngakhale zinali chonchi, iye anapitirizabe kukakamiza Yosefe kuti agone naye. N’kutheka kuti chifukwa cha kunyada komanso kudziona kuti ndi wokongola, ankaganiza kuti atapitiriza kumunyengerera, Yosefe akhoza kusintha maganizo. Zimene anachitazi n’zofanana ndi zimene Satana anachita pa nthawi imene ankayesa Yesu. Satana atalephera kugonjetsa Yesu, sanasiyire pomwepo. Baibulo limati, “anamusiya kufikira nthawi ina yabwino.” (Luka 4:13) Zimenezi zikusonyeza kuti atumiki a Yehova ayenera kutsimikiza mtima kuti asamagonje poyesedwa. Ndi mmenenso Yosefe anachitira. Sanagonje ngakhale kuti ankayesedwa tsiku ndi tsiku. Baibulo limanena kuti, “Iye sanamvere” zoti agone ndi mkazi wa Potifarayo. (Genesis 39:10) Komatu mkazi wa Potifara sanasiye kum’kopa Yosefe.

Pofuna kukwaniritsa zofuna zake, anasankha nthawi yabwino. Anasankha nthawi imene antchito onse anali atatuluka m’nyumba. Anadziwa kuti pa nthawiyi Yosefe alowa m’nyumbamo kuti agwire ntchito yake. Yosefe analowadi m’nyumbamo ndipo mkazi wa Potifara anaona kuti ndi nthawi yoti akwaniritse zofuna zake. Choncho anagwira malaya a Yosefe, n’kumuuza kuti: “Ugone nane basi!” Yosefe anakana nthawi yomweyo. Anayesetsa kuti athawe koma mkaziyo anagwira malaya ake mwamphamvu. Yosefe anangovula malaya akewo n’kuthawa ndipo malayawo anatsala m’manja mwa mkaziyo.—Genesis 39:11, 12.

Zimenezi zikutikumbutsa zimene mtumwi Paulo analemba. Iye anati: “Thawani dama.” (1 Akorinto 6:18) Yosefe ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa Akhristu onse oona. Nthawi zina timakhala kapena kugwira ntchito ndi anthu amene satsatira malamulo a Mulungu. Komabe zimenezi siziyenera kutipangitsa kuchita makhalidwe oipa. Tiyenera kukana kuchita zinthu zoipa ngakhale kuti zimenezi zingapangitse kuti tivutike mwa njira inayake.

Mwachitsanzo, Yosefe anakumana ndi mavuto ambiri atakana kugona ndi mkazi wa Potifara. Mkaziyu anaganiza zomukhaulitsa moti Yosefe atathawa, iye anayamba kukuwa n’cholinga choti antchito ena alowe m’nyumbamo. Antchitowo atalowa, anawauza kuti Yosefe amafuna kum’gwiririra koma atakuwa, Yosefeyo wathawa. Mkazi wa Potifara anasunga malaya a Yosefe n’cholinga choti mwamuna wake akabwera udzakhale umboni woti amafuna kum’gwiririra. Potifara atabwera, mkaziyu anamuuza nkhani ya bodzayi. Anaimbanso mlandu mwamuna wakeyo ponena kuti analakwitsa pobweretsa Yosefe kuti azigwira ntchito m’nyumba mwawo. Kodi Potifara anatani atauzidwa zimenezi? Baibulo limati, “mkwiyo wake unayaka” ndipo analamula kuti Yosefe aikidwe m’ndende.—Genesis 39:13-20.

“ANASAUTSA MAPAZI AKE NDI MATANGADZA”

Sitidziwa zambiri za mmene ndende za akaidi za ku Iguputo zinalili pa nthawiyo. Akatswiri ofukula zinthu  zakale anapeza malo angati amenewa. Zikuoneka kuti ndendezo zinali ndi chitetezo chokhwima komanso zinkakhala ndi zipinda zamdima. Yosefe anafotokoza kuti ndende imene anaikidwamo inali ngati ‘dzenje,’ zomwe zikusonyeza kuti munthu akapitako ankangoona kuti kwake kwatha. (Genesis 40:15, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Buku la Masalimo limasonyeza kuti Yosefe ankakhala mozunzika kwambiri m’ndendeyi. Limati: “Anasautsa mapazi ake ndi matangadza, anam’manga ndi maunyolo.” (Salimo 105:17, 18) Nthawi zina akaidi a ku Iguputo ankawamanga nyakula ndipo ena ankawamangirira chitsulo m’khosi. Yosefe zinkamupweteka poona kuti akuzunzidwa popanda chifukwa.

Ndipo sikuti Yosefe anangokhala m’ndendemu kanthawi kochepa. Baibulo limasonyeza kuti anakhalamo kwa zaka zambiri. * Iye sankaganiza n’komwe zoti adzatulukanso m’ndendeyi. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti asataye mtima?

Baibulo limati: “Yehova anapitirizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha.” (Genesis 39:21) Zinthu monga matangadza, makoma a ndende komanso malo amdima sizingachititse kuti Yehova asiye kukonda atumiki ake. (Aroma 8:38, 39) N’zosakayikitsa kuti pa nthawi imene Yosefe anali m’ndende ankapemphera kwa Atate wake wakumwamba n’kumamuuza nkhawa zake. Zimenezi zinamuthandiza kuti akhale ndi mtendere wa m’maganizo umene “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse” amapereka. (2 Akorinto 1:3, 4; Afilipi 4:6, 7) Kodi Yehova ankathandizanso bwanji Yosefe? Baibulo limanena kuti Yehova anachititsa “mkulu wa ndende kum’konda Yosefe.”

Akaidi ankapatsidwa ntchito yoti azigwira ndipo Yosefe ankagwira mwakhama ntchito imene anapatsidwa. Zimenezi zinapangitsa kuti Yehova apitirize kumudalitsa. Popeza Yehova ankadalitsa Yosefe, zinapangitsa kuti woyang’anira ndende azimudalira ndi kumulemekeza ngati mmene Potifara ankachitira muja. Baibulo limati: “Choncho, mkulu wa ndendeyo anaika Yosefe kukhala woyang’anira akaidi onse m’ndendemo, ndi chilichonse chimene chinali kuchitika mmenemo. Mkulu wa ndendeyo sanali kuyang’aniranso chilichonse chimene chinali m’manja mwake. Zinali choncho chifukwa Yehova anali ndi Yosefe, ndipo chilichonse chimene iye anali kuchita Yehova anali kuchidalitsa.” (Genesis 39:22, 23) Yosefe ankasangalala kwambiri chifukwa chodziwa kuti Yehova akumudalitsa.

Zinthu zikhoza kusintha kwambiri pa moyo wathu ndipo mwinanso tikhoza kuchitidwa zinthu zopanda chilungamo. Zoterezi zikachitika, kuganizira chikhulupiriro cha Yosefe kungatithandize kwambiri. Tikamapemphera kwa Yehova nthawi zonse, tikamamvera malamulo ake komanso tikamapitiriza kuchita zinthu zabwino, iye adzatidalitsa. M’nkhani zotsatira zokhudza Yosefe zimene zidzatuluke m’tsogolomu, tidzaona njira zina zimene Yehova anamudalitsira.

Ali m’ndende, Yosefe ankagwira ntchito mwakhama ndipo Yehova anamudalitsa

^ ndime 23 Baibulo limasonyeza kuti Yosefe anali ndi zaka 17 kapena 18 pamene anayamba kutumikira panyumba ya Potifara ndipo anakhalako kwa zaka zingapo. Zimenezi zikusonyeza kuti mmene ankapita kundende n’kuti ali ndi zaka zoposa 20. Baibulo limasonyeza kuti anatuluka kundende ali ndi zaka 30.—Genesis 37:2; 39:6; 41:46.