Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Ankafuna Kuti Ndione Ndekha Kuti Zoona Ndi Ziti”

“Ankafuna Kuti Ndione Ndekha Kuti Zoona Ndi Ziti”
  • CHAKA CHOBADWA: 1982

  • DZIKO: DOMINICAN REPUBLIC

  • POYAMBA: NDINALI M’CHIPEMBEDZO CHA MORMON

KALE LANGA:

Ndinabadwira ku Santo Domingo, m’dziko la Dominican Republic, m’banja la ana anayi ndipo ndine womaliza. Makolo anga anali ophunzira kwambiri ndipo ankafuna anafe tikule bwino. Zaka zinayi ndisanabadwe, makolo anga anakumana ndi amishonale a tchalitchi cha Mormon. Atachita chidwi ndi mmene amishonalewo ankaonekera, anaganiza zoyamba tchalitchi chimenechi ndipo banja lathu linali loyamba kulowa tchalitchichi kuderali.

Pamene ndinkakula ndinkasangalala ndi zimene tinkachita tikapita kutchalitchi. Ndinkasangalalanso chifukwa choti tchalitchichi chinkalimbikitsa mabanja kukhala ndi moyo wosangalala komanso makhalidwe abwino. Ndinkanyadira chifukwa chokhala m’chipembedzo cha Mormon ndipo ndinkafunitsitsa kudzakhala mmishonale.

Ndili ndi zaka 18, banja lathu linasamukira ku America kuti ndikapitirize maphunziro anga akuyunivesite. Patatha chaka chimodzi, amayi anga aang’ono ndi amuna awo, omwe ndi a Mboni za Yehova, anabwera ku Florida kudzationa. Iwo anatiitanira ku msonkhano wawo. Kumsonkhanoko, ndinachita chidwi kwambiri kuona kuti anthu ambiri ankalemba manotsi ndipo wokamba nkhani akatchula vesi, iwonso ankawerenga vesilo m’Baibulo lawo. Choncho nanenso ndinapempha pepala ndi cholembera kuti ndizilemba manotsi.

Pambuyo pa msonkhanowo mayi anga aang’ono ndi amuna awo aja anandiuza kuti popeza ndinkafuna kudzakhala mmishonale, angandithandize kuti ndiphunzire Baibulo. Ndinaona kuti anali maganizo abwino chifukwa pa nthawiyi, sindinkalidziwa bwino Baibulo koma ndinkangodziwa zimene Buku la Mormon limanena.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Tikamaphunzira Baibulo pa foni, amayi anga aang’ono ndi amuna awo aja ankandilimbikitsa kuti ndiziona ngati zimene ndinkakhulupirira zikugwirizana ndi zomwe ndinkaphunzira m’Baibulo. Iwo ankachita zimenezi chifukwa ankafuna kuti ndione ndekha kuti zoona ndi ziti.

 Panali zambiri zimene ndinkakhulupirira zokhudza chipembedzo cha Mormon, koma sindinkadziwa bwino ngati zinalidi zochokera m’Baibulo. Mayi anga aang’ono aja ananditumizira Galamukani! ya November 8, 1995, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, yomwe inafotokoza za zikhulupiriro za chipembedzo cha Mormon. Ndinadabwa kwambiri chifukwa zina mwa zikhulupirirozi sindinkazidziwa. Zimenezi zinachititsa kuti ndikafufuze pa Intaneti, pa webusaiti ya chipembedzochi kuti ndione ngati zimene Galamukani! imeneyi inanena zinali zoona. Ndinapeza kuti zinalidi zoona, ndipo umboni winanso ndinaupeza nditapita kumalo osungirako zinthu zakale za chipembedzo cha Mormon ku Utah.

Poyamba ndinkaganiza ngati zimene Buku la Mormon limanena n’zogwirizana ndi Baibulo. Koma nditayamba kuphunzira Baibulo mosamala, ndinaona kuti n’zosiyana. Mwachitsanzo, pa Ezekieli 18:4, Baibulo limanena kuti moyo umafa. Koma m’Buku la Mormon, pa Alma 42:9, pamati: “Moyo sungafe.”

Kuwonjezera pa kuphunzitsa zinthu zosemphana ndi zimene Baibulo limanena, chipembedzochi chinkatiphunzitsanso kuti Mulungu amakonda dziko lathu kuposa mayiko ena. Mwachitsanzo, anthu achipembedzo cha Mormon amakhulupirira kuti munda wa Edeni unali mumzinda wa Jackson County ku Missouri, ku America. Ndiponso atsogoleri a tchalitchichi ankaphunzitsa kuti Mulungu adzalamulira dziko lapansi pogwiritsa ntchito boma la America.

Ndinkadabwa kuti zimenezi zingatheke bwanji. Tsiku lina ndikulankhula pa foni ndi munthu wina wachipembedzo chathu, yemwe ankaphunzira zaumishonale, ndinam’funsa ngati iyeyo angamenyane ndi anthu achipembedzo cha Mormon anzake, zitakhala kuti dziko lawo ndi lake lili pa nkhondo. Ndinadabwa atandiyankha kuti akhoza kuchita zimenezi. Ndinafufuza kuti ndidziwe zambiri za zikhulupiriro za tchalitchi chathu komanso ndinafunsa atsogoleri achipembedzochi za zikhulupirirozi. Iwo anandiyankha kuti pa nthawiyo zinali zosatheka kumvetsa mayankho a mafunso amenewa, koma ndidzawamvetsa bwino m’tsogolo.

Nditakhumudwa ndi zimene anandiyankhazi, ndinayamba kuganizira zifukwa zimene ndinkafunira kudzakhala mmishonale. Ndinaona kuti chifukwa china chinali choti ndinkafuna kuthandiza anthu. Komanso ndinkaona kuti n’kadzakhala mmishonale, anthu azidzandilemekeza. Koma Mulungu sindinkamudziwa bwinobwino. Ngakhale kuti m’mbuyomo ndinkawerenga Baibulo, sindinkalilemekeza ngati Mawu a Mulungu. Ndiponso sindinkadziwa kuti Mulungu analengeranji dziko lapansili komanso anthu.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kunandithandiza kudziwa zinthu monga dzina la Mulungu, zimene zimachitika munthu akamwalira komanso zomwe Yesu adzachite pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Kenako ndinayamba kulidziwa bwino Baibulo ndipo ndinayambanso kuuza ena zimene ndinkaphunzira. Poyamba ndinkadziwa kuti Mulungu aliko, koma tsopano ndinayamba kulankhula naye m’pemphero ndipo ndinkaona kuti ndili naye pa ubwenzi wabwino. Pa July 12, 2004 ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova ndipo patatha miyezi 6 ndinayamba kumatha nthawi yambiri ndikulalikira.

Kwa zaka zisanu, ndinatumikira kulikulu la Mboni za Yehova padziko lonse ku Brooklyn, mumzinda wa New York. Ndinkasangalala kwambiri kuthandiza nawo pa ntchito yopanga Mabaibulo ndiponso mabuku amene amathandiza anthu padziko lonse kuphunzira Baibulo. Panopa ndikupitirizabe kuthandiza anthu kuphunzira za Mulungu ndipo ntchito imeneyi imandithandiza kukhala wosangalala.