Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kutumikira Mulungu Kuli Ngati Mankhwala Ake

Kutumikira Mulungu Kuli Ngati Mankhwala Ake

Apainiya awiri atalowa m’nyumba ina ku Kenya, anadabwa kuona munthu wamng’ono kwambiri dzina lake Onesmus atagona pabedi. Kathupi kake kanali kakang’ono kwambiri ndipo anali ndi timikono tifupitifupi. Apainiyawo anakambirana naye lonjezo la Mulungu lakuti “munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo,” ndipo iye anangomwetulira.—Yes. 35:6.

Apainiyawo anamva kuti Onesmus, amene panopa ali ndi zaka zoposa 35, anabadwa ndi matenda a mafupa. Matendawa alibe mankhwala ndipo amachititsa kuti mafupa ake akhale osalimba moti sachedwa kusweka. Choncho Onesmus ankaona kuti pa moyo wake wonse azizunzika ndi ululu komanso aziyenda pa njinga ya anthu olumala.

Onesmus anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Koma mayi ake sanalole kuti azipita kumisonkhano poopa kuti akasweka mafupa ndipo ululu wake udzawonjezeka. Choncho abalewo ankangojambula nkhani zapamisonkhano n’kukamupatsa kuti azimvetsera kwawoko. Ataphunzira kwa miyezi 5, Onesmus anaganiza zoti apitebe kumisonkhano.

Kodi ululu wake unawonjezeka chifukwa choti anapita kumisonkhano? Ayi. Onesmus anati: “Ndikakhala pamisonkhano, ululu wanga unkachepa.” Iye ankaona kuti zinthu zosangalatsa zimene ankaphunzira zinkachepetsa ululu wake. Mayi ake aja ataona kuti mwana wawo wayamba kusintha anasangalala kwambiri moti anavomeranso kuphunzira Baibulo. Iwo ankakonda kunena kuti: “Kutumikira Mulungu kuli ngati mankhwala a mwana wanga.”

Pasanapite nthawi yaitali, Onesmus anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Kenako anabatizidwa ndipo panopa ndi mtumiki wothandiza. Miyendo yake komanso mkono umodzi sizigwira ntchito koma ankafunitsitsa kuchita zonse zimene akanatha potumikira Yehova. Iye ankafuna kuchita upainiya wothandiza koma ankaopa kulembetsa chifukwa chodziwa kuti padzafunika munthu wina woti azimuyendetsa panjinga yakeyo nthawi zonse. Atauza Akhristu anzake zimene zinkamudetsa nkhawazi, anamulonjeza kuti amuthandiza. Iwo anamuthandizadi kuti achite upainiyawo.

Kenako anayamba kulakalaka upainiya wokhazikika koma nkhawa yake inali yomwe ija. Tsiku lina analimbikitsidwa kwambiri atawerenga lemba la tsiku. Lembalo linali la Salimo 34:8 limene limati: “Talawani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino.” Ataganizira kwambiri lembali, iye anasankha zoyamba upainiya wokhazikika. Panopa amalalikira masiku 4 pa mlungu ndipo amaphunzira Baibulo ndi anthu ambiri omwe akukonda kwambiri choonadi. Mu 2010, Onesmus analowa Sukulu ya Utumiki Waupainiya. Iye anasangalala kwambiri kuona kuti mlangizi mmodzi anali m’bale amene anamulalikira poyamba uja.

Panopa makolo a Onesmus anamwalira koma abale ndi alongo amamusamalira bwinobwino. Iye akuona kuti akudalitsidwa kwambiri ndipo akuyembekezera nthawi imene aliyense sadzanena kuti: “Ndikudwala.”—Yes. 33:24.