Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azimvetsera Mapemphero Anu?

Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azimvetsera Mapemphero Anu?

Yehova Mulungu ndi “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Tikhoza kulankhula naye kulikonse, nthawi iliyonse, mokweza kapenanso chamumtima. Yehova amafuna kuti tizimutchula kuti “Atate” ndipo iye ndi Atate wabwino kwambiri kuposa wina aliyense. (Mateyu 6:9) Popeza Yehova ndi wachikondi, amatiphunzitsa zimene tingachite kuti iye azimvetsera mapemphero athu.

TIZIPEMPHERA KWA YEHOVA MULUNGU MU DZINA LA YESU

“Ngati mupempha chilichonse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.”​—Yohane 16:23.

Mawu a Yesuwa akusonyeza kuti Yehova amafuna kuti tizipemphera kwa iye mu dzina la Yesu Khristu, osati kudzera m’mafano, mwa anthu oyera mtima, angelo kapena makolo athu amene anamwalira. Tikamapemphera kwa Mulungu kudzera mu dzina la Yesu, timasonyeza kuti timazindikira udindo wofunika kwambiri wa Yesuyo. Iye ananena kuti: “Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.”​—Yohane 14:6.

TIZILANKHULA KUCHOKERA MUMTIMA

“Mukhuthulireni za mumtima mwanu.”​—Salimo 62:8.

Tikamapemphera kwa Yehova tiyenera kulankhula ngati mmene tingalankhulire ndi bambo wathu wachikondi. M’malo mowerenga pemphero lathu kuchokera m’buku kapena kungobwereza zimene taloweza, tiyenera kulankhula naye mwaulemu komanso mochokera mumtima.

TIZIPEMPHERA MOGWIRIZANA NDI ZIMENE MULUNGU AMAFUNA

“Chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”​—1 Yohane 5:14.

M’Baibulo, Yehova amatiuza zimene adzatichitire komanso zimene amafuna kuti tizimuchitira iyeyo. Kuti mapemphero athu azikhala ovomerezeka kwa Mulungu, tiyenera kupemphera “mogwirizana ndi chifuniro chake.” Kuti tichite zimenezi, tiyenera kuphunzira Baibulo n’cholinga choti timudziwe bwino. Tikamachita zimenezi, mapemphero athu adzamusangalatsa.

KODI TIKHOZA KUPEMPHERERA ZINTHU ZOTANI?

Tingapemphe Kuti Atipatse Zimene Timafunikira. Tikhoza kupempha Mulungu kuti azitithandiza kupeza zofunika pa moyo monga chakudya, zovala ndi malo okhala. Tikhozanso kupemphera kuti atipatse nzeru zoti tisankhe bwino zochita kapena mphamvu zoti tipirire mavuto. Tingapempherenso kuti atithandize kukhala ndi chikhulupiriro, atikhululukire kapena atithandize pa mavuto athu.​—Luka 11:3, 4, 13; Yakobo 1:5, 17.

Tizipempherera Anthu Ena. Makolo achikondi amasangalala ana awo akamakondana. Nayenso Yehova amafuna kuti ana ake apadziko lapansi azikondana. Tingachite bwino kupempherera mwamuna kapena mkazi wathu, ana athu, achibale athu komanso anzathu. Yakobo analemba kuti: ‘Muzipemphererana.’​—Yakobo 5:16.

Tiziyamikira. Ponena za Mlengi wathu, Baibulo limanena kuti: “Anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chimwemwe.” (Machitidwe 14:17) Tikamaganizira zinthu zonse zimene Mulungu watichitira, timafunitsitsa kumuthokoza m’pemphero. Timasonyezanso kuti timayamikira zimene Mulungu wachita tikamamvera malamulo ake.​—Akolose 3:15.

TIZIKHALA OLEZA MTIMA N’KUMAPITIRIZA KUPEMPHERA

Nthawi zina, tingakhumudwe chifukwa choti mapemphero athu ochokera mumtima sanayankhidwe mwamsanga. Zikatero, kodi tiziganiza kuti Mulungu alibe nafe chidwi? Ayi ndithu. Taganizirani zitsanzo zotsatirazi zomwe zimasonyeza kuti tiyenera kupitiriza kupemphera.

Steve, yemwe tamutchula munkhani yoyamba uja, ananena kuti: “Pemphero ndi limene landithandiza kuti ndisataye mtima.” Kodi n’chiyani chinamuthandiza kusintha? Iye anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anazindikira kufunika kopemphera mosalekeza ndipo anati: “Ndimapemphera kwa Mulungu n’kumamuthokoza chifukwa cha mmene anzanga akhala akundithandizira mwachikondi. Panopa ndine wosangalala kwambiri kuposa kale.”

Nanga bwanji za Jenny yemwe ankaganiza kuti si woyenera kuti Mulungu azimvetsera mapemphero ake? Iye anati: “Pa nthawi imene ndinkamva kwambiri kuti ndinali wachabechabe, ndinapempha Mulungu kuti andithandize kumvetsa chifukwa chake ndinkamva choncho.” Kodi zimenezi zinamuthandiza bwanji? Jenny ananena kuti: “Kulankhula ndi Mulungu kwandithandiza kuona zinthu moyenera n’kuzindikira kuti ngakhale kuti mtima wanga ukunditsutsa, Mulungu sakuchita zimenezi. Kwandithandizanso kuti ndisataye mtima koma ndipitirize kuchita zimene ndingakwanitse.” Ananenanso kuti: “Pemphero landithandiza kuona kuti Yehova ndi Mulungu wachikondi, Atate wanga komanso Mnzanga weniweni ndipo nthawi zonse azindithandiza ndikamayesetsa kuchita zimene amafuna.”

Isabel ananena kuti akaona mwana wake Gerard akusangalala ndi moyo ngakhale kuti ndi wolumala amazindikira kuti Mulungu anayankha mapemphero ake kudzera mwa iye

Chitsanzo china pa nkhaniyi ndi Isabel. Pamene anali woyembekezera, madokotala anamuuza kuti mwana wake adzabadwa ali wolumala. Iye anakhumudwa kwambiri. Ndiye anthu ena anamuuza kuti achotse mimbayo. Iye anati: “Ndinamva ngati ndifa chifukwa cha kumva kupweteka kwambiri mumtima.” Ndiye kodi anatani? Iye anati: “Ndinkangokhalira kupemphera kwa Mulungu kuti azindithandiza.” Patapita nthawi, anabereka mwana wamwamuna dzina lake Gerard ndipo analidi wolumala. Kodi Isabel akuona kuti Mulungu anayankha mapemphero ake? Inde. Kodi n’chifukwa chiyani amaona chonchi? Isabel anati: “Ndikaona mwana wanga, yemwe panopa ali ndi zaka 14, akusangala ndi moyo ngakhale kuti ndi wolumala, ndimazindikira kuti Yehova anayankha mapemphero anga kudzera mwa iye. Ndikutero chifukwa ndikuona kuti mwanayo ndi dalitso lalikulu kwambiri limene Yehova Mulungu wandipatsa.”

Mawu ochokera pansi pa mtima ngati amenewa amatikumbutsa za mawu a wolemba masalimo wina akuti: “Mudzamva kuchonderera kwa anthu ofatsa, inu Yehova. Mudzakonzekeretsa mitima yawo. Mudzatchera khutu lanu.” (Salimo 10:17) Izitu ndi zifukwa zomveka zotichititsa kupitiriza kupemphera.

M’Baibulo muli mapemphero ambiri a Yesu. Pemphero lodziwika kwambiri ndi limene anaphunzitsa otsatira ake. Kodi tikuphunzira chiyani pa pemphero limeneli?