Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Kangaude Wam’nyumba Amachita Zogometsa Kwambiri

Kangaude Wam’nyumba Amachita Zogometsa Kwambiri

KANGAUNDE amene amapezeka m’nyumba, amamanga kanyumba kake ka ulusi umene umatha kumata kwambiri khoma. Koma pakakhala kuti ndi pansi, ulusiwu sumata kwambiri, ndipo izi zimapangitsa kuti tizilombo todutsa tizikodwa ndi ulusi umenewu. Kodi kangaudeyu amatha bwanji kutulutsa ulusi womwe umamata kwambiri pakhoma koma sumata kwambiri pansi?

Kanyumba kapakhoma ka kangaude

Taganizirani izi: Kangaudeyu amamanga kanyumba kake kaulusi pakhoma, kudenga kapena malo ena otere, ndipo ulusi wake umakhala womata kwambiri moti tizilombo touluka sitingawononge ulusiwu. Akatswiri ena ofufuza zinthu a pa yunivesite ya Akron, mumzinda wa Ohio ku America, anapeza kuti kanyumba ka kangaude kapakhoma kamakhala kosiyana ndi kanyumba kapansi. Kanyumba kapansi ka kangaude sikakhala ndi ulusi wambiri ndipo zimenezi zimapangitsa kuti asamavutike kuchotsa tizichilombo tomwe tagwidwa pa ulusiwo.

Kanyumba kapansi ka kangaude

Akatswiri a pa yunivesiteyi, omwe anapeza zodabwitsa zimene kangaudeyu amachita, “ayamba kufufuza njira zimene angapangire guluu womata kwambiri ngati mmene umachitira ulusi wa kangaude wam’nyumba.” Akatswiriwa akuganiza kuti zimenezi zithandiza kuti apange guluu amene angadzamugwiritse ntchito ngati mabandeji komanso pothandizira anthu amene athyoka mafupa.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti kangaudeyu azitha kutulutsa ulusi womata kwambiri pakhoma komanso wosamata kwambiri pansi, kapena pali winawake amene anamulenga?