Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Muzichita Zinthu Moleza Mtima?

Kodi Mungatani Kuti Muzichita Zinthu Moleza Mtima?

MWINA nkhani zapitazi zakuthandizani kudziwa kuti munthu woleza mtima amakhala ndi thanzi labwino, amasankha zinthu mwanzeru komanso amakhala ndi anthu abwino ocheza nawo. Ndiyeno kodi mungatani kuti muzichita zinthu moleza mtima? Taonani zina zimene mungachite.

Fufuzani chimene chimachititsa

Kodi pali anthu amene amakuchititsani kuti musamaleze mtima? Nthawi zina anthu amenewa angakhale mwamuna kapena mkazi wanu, ana anu ndiponso makolo anu. N’kuthekanso kuti simumaleza mtima mukamadikirira winawake kapena mukachedwa. Komanso mungalephere kuleza mtima ngati mwatopa, muli ndi njala, tulo kapena nkhawa.

Kodi kufufuza zimene zimachititsa kuti musamaleze mtima kungakuthandizeni bwanji? Mfumu Solomo inalemba kuti: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.” (Miyambo 22:3) Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, munthu akadziwa zimene zimamuchititsa kuti asamaleze mtima akhoza kuzipewa mosavuta. Poyamba angafunike kumachita khama kwambiri kuti azileza mtima koma m’kupita kwa nthawi amazolowera kuchita zinthu modekha.

Chepetsani zimene mumachita

Pulofesa wina, dzina lake Noreen Herzfeld, wa payunivesite ya Saint John’s, ku Minnesota m’dziko la United States, anati: “Munthu akamagwira ntchito zambirimbiri pa nthawi imodzi ubongo wake umalephera kugwira bwino ntchito. Kenako munthuyo amalephera kupanga zinthu bwinobwino, zimene zimachititsa kuti azichita ulesi, azichita zinthu mosaleza mtima, azilephera kuganiza mwanzeru komanso kuthana ndi mavuto.”

Zingakuvuteninso kuleza mtima ngati muli ndi zinthu zambirimbiri zoti muchite. Dr. Jennifer Hartstein, yemwe tamutchula mu nkhani zapita zija ananenanso kuti: “Nthawi zambiri munthu saleza mtima akakhala kuti wapanikizika.”

Akulu akale anati, “kuona maso a nkhono n’kudekha.” Choncho ngati mukufuna kumasangalala ndi moyo, muzichita zinthu modekha. Muzikhala ndi anzanu apamtima ochepa oti mukhoza kupeza nthawi yocheza nawo, kusiyana n’kukhala ndi anzanu ambirimbiri amene muzingoonana nawo mwa apo ndi apo. Muzigawa nthawi yochitira zinthu zosiyanasiyana ndipo muziyamba kuchita zinthu zofunika kwambiri. Muzionetsetsa kuti zipangizo zamakono zisamakudyereni nthawi komanso muzipewa kuchita zinthu zosafunika kwenikweni.

Kuti musamadzichulukitsire zochita muyenera kuonanso zimene mumachita tsiku lililonse. Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachepetse kapena kungozisiyiratu? Baibulo limati: “Chilichonse chili ndi nthawi yake . . . , nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.” (Mlaliki 3:1, 6) Mwinatu ino ingakhale nthawi yabwino yoti musiye zinthu zina zimene zimangokutayitsani nthawi. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzichita zinthu modekha.

Muziona zinthu moyenera

Choyamba, dziwani kuti sikuti nthawi zonse zinthu zimachitika mofulumira ngati mmene inuyo mukufunira. Munthu woleza mtima amadziwa kuti sangapangitse kuti zinthu zonse zizichitika pa nthawi yomwe iyeyo akufuna.

Chachiwiri muzikumbukira kuti nthawi zina zinthu zimangochitika mosayembekezereka. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano, amphamvu sapambana pankhondo, anzeru sapeza chakudya, omvetsa zinthu nawonso sapeza chuma, ndipo ngakhale odziwa zinthu sakondedwa, chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo. Pakuti munthu nayenso sadziwa nthawi yake.”—Mlaliki 9:11, 12.

Choncho, m’malo mochita zinthu mosaleza mtima chifukwa cha zinthu zimene simungazisinthe, muzichita zinthu zimene mumadziwa kuti mungathe kuzichita. Mwachitsanzo, m’malo mokwiya kuti minibasi ikuchedwa kudzaza, mungachite bwino kupeza zochita zina pa nthawi imene mukudikirayo. Mwina mungamalembe zimene mukufuna kuchita m’tsogolo kapena kuwerenga zinazake.

Mfundo yofunika kuikumbukira ndi yakuti palibe chifukwa chodandaulira ndi zinthu zimene simungathe kuzisintha. N’chifukwa chake Baibulo limafunsa kuti: “Ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pang’ono pokha mwa kuda nkhawa?”—Luka 12:25.

Mukhale pa ubwenzi ndi Mulungu

Anthu ambiri amene amakhulupirira Baibulo azindikira kuti kutsatira mfundo zake kumawathandiza kuti azikhala oleza mtima. Baibulo limasonyeza kuti munthu amene ali pa ubwenzi ndi Mulungu amasonyeza makhalidwe monga kuleza mtima, chikondi, chimwemwe, mtendere, kudekha komanso kudziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Komanso limanena kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” (Afilipi 4:6, 7) Choncho mukamaphunzira Baibulo mungadziwe zimene mungachite kuti muchepetse nkhawa komanso kuti muzichita zinthu moleza mtima.