Onani zimene zilipo

Kodi Mulungu Amasintha Maganizo Ake?

Kodi Mulungu Amasintha Maganizo Ake?

Yankho la m’Baibo

 Inde. Iye amasintha maganizo ake akaona kuti anthu asintha khalidwe lawo. Mwacitsanzo, Mulungu atauza Aisiraeli kuti adzawalanga, anakambanso kuti: “Mwina adzamvela ndipo aliyense wa iwo adzabwelela kucoka panjila yake yoipa. Pamenepo ndidzasintha maganizo anga pa tsoka limene ndikufuna kuwagwetsela cifukwa ca zocita zawo zoipa.”—Yeremiya 26:3.

 Omasulila Mabaibo ambili anamasulila lembali monga kuti Mulungu “angalape” pa tsoka limene anali kufuna kupeleka kwa Aisiraeli, zimene zikanaonetsa kuti Mulungu analakwitsa. Komabe, mawu Aciheberi coyambilila a palembali, angatanthauze “kusintha maganizo kapena zimene ufuna kucita.” Pulofesa wina anati: “Munthu akasintha khalidwe lake, zimapangitsa kuti Mulungu asinthe cilango cimene anali kufuna kum’patsa.”

 Olo kuti Mulungu angasinthe maganizo ake, sizitanthauza kuti n’zimene ayenela kucita nthawi zonse. Onani nkhani zina za m’Baibo zoonetsa kuti Mulungu sanasinthe maganizo ake:

  •   Mulungu sanalole kuti Balaki amupangitse kusintha maganizo Ake pa nthawi imene Balakiyo anali kufuna kuti Mulungu atembelele mtundu wa Aisiraeli.—Numeri 23:18-20.

  •   Sauli, Mfumu ya Aisiraeli atayamba kucita zoipa, Mulungu sanasinthe maganizo ake atanena kuti amukana monga mfumu ya Aisiraeli.—1 Samueli 15:28, 29.

  •   Mulungu adzakwanilitsa lonjezo lake lakuti Mwana wake adzakhala wansembe mpaka kale-kale. Iye sadzasintha maganizo ake pa nkhaniyi.—Salimo 110:4.

Kodi si paja Baibo imati Mulungu sasintha?

 Inde, ndipo imati Mulungu anati: ‘Ine ndine Yehova, sindisintha.’ (Malaki 3:6) Komanso, Baibo imati Mulungu “sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.” (Yakobo 1:17) Komabe, izi sizikutsutsana na zimene Baibo imakamba zakuti Mulungu amasintha maganizo ake. , Mulungu sasintha m’lingalilo lakuti mfundo zake zacikondi komanso cilungamo sizisintha. (Deuteronomo 32:4; 1 Yohane 4:8) Komabe, angapatse anthu malangizo osiyana-siyana pa nthawi zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, Mulungu anapatsa Mfumu Davide malangizo osiyana a mmene angamenyele nkhondo ziŵili zotsatizana. Koma malangizo onsewo anathandiza.—2 Samueli 5:18-25.

Kodi Mulungu amadziimba mlandu cifukwa analenga anthu?

 Ayi, koma amamva cisoni cifukwa anthu ambili amakana kumumvela. Pokamba za mmene Mulungu anamvela Cigumula ca m’nthawi ya Nowa cisanacitike, Baibo imati: “Yehova anamva cisoni kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinam’pweteka kwambili mumtima.” (Genesis 6:6) Palembali, mawu akuti “anamva cisoni,” anacokela ku mawu Aciheberi amene angatanthauzenso “kusintha maganizo.” Conco, Mulungu anasintha maganizo ake n’kuwononga anthu ambili amene analiko Cigumula cisanacitike cifukwa cakuti anthuwo anali oipa. (Genesis 6:5, 11) Ngakhale kuti anakhumudwa kwambili cifukwa anthu ambili anasankha kucita zoipa, iye sanasinthe maganizo ake okhudza anthu onse. N’cifukwa cake anapulumutsa Nowa na banja lake pa nthawi ya Cigumula kuti anthu asatheletu padziko lapansi.—Genesis 8:21; 2 Petulo 2:5, 9.