Onani zimene zilipo

N’cifukwa Ciani Mboni za Yehova Zimalalikila Anthu Amene Ali Kale ndi Cipembedzo Cao?

N’cifukwa Ciani Mboni za Yehova Zimalalikila Anthu Amene Ali Kale ndi Cipembedzo Cao?

Taona kuti anthu ambili amene ali kale ndi cipembedzo amakondwela tikamakambilana nao nkhani za m’Baibulo. Ngakhale zili conco, timalemekeza ufulu umene munthu ali nao wotsatila zimene amakhulupilila. Ndipo sitikakamiza anthu kuti amvetsele uthenga wathu.

Pokambilana nkhani za cipembedzo ndi munthu wina, timatsatila malangizo a m’Baibulo akuti tizicita zimenezo ndi “mtima wofatsa ndiponso mwaulemu kwambili.” (1 Petulo 3:15) Ndipo timadziŵa kuti ena angakane uthenga wathu. (Mateyu 10:14) Komabe, sitimadziŵa mmene anthu angayankhile pokhapo titakambilana nao. Timadziŵanso kuti zinthu paumoyo wa anthu zimasintha.

Mwacitsanzo, munthu angatangwanike kwambili cakuti sitingathe kulankhula naye, koma ulendo wotsatila angasangalale kukambitsilana naye. Ndiponso, anthu angakumane ndi mavuto amene angawacititse kuti akhale ndi cidwi cofuna kumvetsela uthenga wa m’Baibulo. Conco, timalimbikila kulankhula ndi anthu nthawi zambili.