Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

AspctStyle/stock.adobe.com

KAMPENI YOITANILA ANTHU KU CIKUMBUTSO

Yesu Adzathetsa Nkhondo

Yesu Adzathetsa Nkhondo

 Pamene Yesu anali padziko lapansi, anaonetsa cikondi cacikulu pa anthu moti anapeleka moyo wake monga nsembe cifukwa ca iwo. (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Posacedwa, iye adzaonetsanso cikondi cake pa anthu poseŵenzetsa mphamvu zake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kuti athetse “nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.”​—Salimo 46:9.

 Onani zimene Yesu adzacita malinga n’zimene Baibo imakamba:

  •   “Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, komanso wonyozeka ndi aliyense amene alibe womuthandiza. Adzamvela cisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzawapulumutsa kuti asapondelezedwe komanso kucitilidwa zaciwawa.”​—Salimo 72:12-14.

 Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila zimene Yesu anaticitila komanso zimene adzaticitila m’tsogolo? Pa Luka 22:19, Yesu anauza ophunzila ake kuti azikumbukila imfa yake. Ndiye cifukwa cake Mboni za Yehova zimasonkhana pamodzi caka ciliconse pa tsiku limene anafa. Tikukuitanilani kuti mudzacite nafe Mwambo Wokumbukila imfa ya Yesu pa Sondo, pa March 24, 2024.

Pezani Kocitila Cikumbutso