Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

alfa27/stock.adobe.com

KAMPENI YOITANILA ANTHU KU CIKUMBUTSO

Yesu Adzacotsapo Anthu Osamvela Malamulo

Yesu Adzacotsapo Anthu Osamvela Malamulo

 Yesu adziŵa mmene cimamvekela munthu akamavutika cifukwa ca kusamvela malamulo na kupanda cilungamo kwa anthu ena. Iye anaimbidwapo mlandu wabodza, kumenyedwa, kuweluzidwa mopanda cilungamo, komanso kufa imfa yowawa. Ngakhale kuti anali wosalakwa, iye anali wokonzeka kupeleka “moyo wake dipo kuti awombole anthu ambili.” (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Tsopano pokhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, iye adzabweletsa cilungamo padziko lonse lapansi, ndipo adzathetselatu zopanda cilungamo zonse.—Yesaya 42:3.

 Baibo imafotokoza mmene dziko lapansi lidzakhalila Yesu akadzacitapo kanthu. Imati:

  •   “Oipa sadzakhalaponso. Udzayangʼana pamene ankakhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Salimo 37:10, 11.

 Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila zimene Yesu anaticitila komanso zimene adzaticitila m’tsogolo? Pa Luka 22:19, Yesu anauza ophunzila ake kuti azikumbukila imfa yake. Ndiye cifukwa cake Mboni za Yehova zimasonkhana pamodzi caka ciliconse pa tsiku limene anafa. Tikukuitanilani kuti mudzacite nafe Mwambo Wokumbukila Imfa ya Yesu pa Sondo, pa March 24, 2024.

Pezani Kocitila Cikumbutso