Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Coonadi Cikali Cofunika Masiku Ano?

Kodi Coonadi Cikali Cofunika Masiku Ano?

 Kodi mumaona kuti n’covuta kusiyanitsa coonadi komanso mabodza? M’malo mokhulupilila coonadi, anthu masiku ano amakhulupilila zinthu potengela mmene akumvela kapena mmene amaonela zinthu. Kuzungulila dziko lonse, anthu ambili samakhulupilila kuti kuli coonadi.

 Maganizo amenewo ni osadabwitsa. Pafupi-fupi zaka 2,000 zapitazo, Bwanamkubwa Waciroma dzina lake Pontiyo Pilato anaonetsa kuti anali na maganizo olakwika pa nkhani yokamba zoona. Iye anafunsa Yesu kuti: “Coonadi n’ciyani?” (Yohane 18:38) Ngakhale kuti Pilato sanayembekeze kuti Yesu amuyankhe, funso lake linali lofunika. Baibo imapeleka yankho imene ingakukhutilitseni, ndipo ingakuthandizeni kudziŵa coonadi m’dzikoli lodzala na mabodza.

Kodi coonadi cilikodi?

 Inde. Baibo imaseŵenzetsa mawu akuti “coonadi” pokamba za zinthu zenizeni komanso za makhalidwe abwino. Imaphunzitsa kuti Yehova a Mulungu ndiye Gwelo la coonadi ceniceni. Imati iye ni “Mulungu wacoonadi.” (Salimo 31:5) Baibo ili na coonadi ponena za Mulungu, ndipo imayelekezela coonadi cimeneco na nyale, cifukwa cingakutsogoleleni m’dziko lino la msokonezo—Salimo 43:3; Yohane 17:17.

Kodi coonadi mungacipeze bwanji?

 Mulungu safuna kuti tilandile coonadi ca m’Baibo m’cimbuli-mbuli. Ndiye cifukwa cake amatilimbikitsa kuifufuza Baibo poseŵenzetsa luntha lathu la kuganiza, osati kungotengeka cabe na mmene tikumvela. (Aroma 12:1) Iye amafuna kuti timudziŵe komanso tim’konde na ‘maganizo athu onse.’ Ndiponso amatilangiza kuti tizitsimikizila kuti zimene tikuphunzila m’Baibo ni coonadi.—Mateyu 22:37, 38; Machitidwe 17:11.

Kodi kunama kunayamba bwanji?

 Baibo imati mdani wa Mulungu, Satana Mdyelekezi, ndiye anayambitsa kunama. Imati iye ni “tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Iye anauza anthu oyambilila mabodza ponena za Mulungu. (Genesis 3:1-6, 13, 17-19; 5:5) Kucokela pa nthawiyo, Satana wakhala akukamba mabodza komanso kubisa coonadi ponena za Mulungu.—Chivumbulutso 12:9.

N’cifukwa ciyani kunama n’kofala masiku ano?

 M’nthawi yathu ino, imene Baibo imati ni “masiku otsiliza,” Satana akusoceletsa anthu ambili kuposa kale lonse. Anthu amanama pofuna kusoceletsa anzawo kapena kuwadyela masuku pa mutu. (2 Timoteyo 3:1, 13) Masiku ano kunama n’kofala ngakhale m’zipembedzo zambili. Monga Baibo inakambilatu za nthawi yathu ino, anthu amadzipezela “aphunzitsi kuti amve zowakomela m’khutu,” ndipo amasankha kusiya “kumvetsela coonadi.”—2 Timoteyo 4:3, 4.

N’cifukwa ciyani coonadi n’cofunika?

 Coonadi cimapangitsa kuti anthu azikhulupililana. Anthu sangakhale pa ubwenzi wolimba ngati sakhulupililana. Baibo imakamba kuti Mulungu amafuna tizimulambila m’coonadi. Imati: “Onse omulambila ayenela kumulambila motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi.” (Yohane 4:24) Kuti mudziŵe mmene coonadi ca m’Baibo cingakuthandizileni kudziŵa mabodza a zipembedzo na kusalola mabodza amenewo kukulamulilani, ŵelengani nkhani za m’magazini yakuti “Mabodza Amene Amalepheletsa Anthu Kukonda Mulungu.”

N’cifukwa ciyani Mulungu akufuna kuti nidziŵe coonadi?

 Mulungu amafuna kuti mukapulumuke. Kuti zimenezi zitheke mufunika kuphunzila coonadi cokhudza iye. (1 Timoteyo 2:4) Mukaphunzila miyeso ya Mulungu ya cabwino na coipa, mudzakhala naye pa ubwenzi wolimba. (Salimo 15:1, 2) Pofuna kuthandiza anthu kuti adziŵe coonadi, Mulungu anatumiza Yesu pa dziko lapansi. Mulungu amafuna kuti tizimvela zimene Yesu anaphunzitsa.—Mateyu 17:5; Yohane 18:37.

Kodi Mulungu adzakuthetsadi kunama?

 Inde. Mulungu amanyansidwa akaona anthu ena akudyela masuku pa mutu anzawo pogwilitsa nchito bodza. Iye analonjeza kuti adzawononga anthu amene amakonda kunama. (Salimo 5:6) Mulungu akadzacita zimenezi, adzakwanilitsanso lonjezo lake lakuti: “Mlomo wa coonadi ndi umene udzakhazikike kwamuyaya.”—Miyambo 12:19.

a Yehova ndilo dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yakuti “Kodi Yehova N’ndani?”