Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Anadzipeleka Mofunitsitsa ku Russia

Anadzipeleka Mofunitsitsa ku Russia

Mu 1991, Mboni za Yehova ku Russia zinasangalala kwambili zitalandila cilolezo pambuyo pokhala pa ciletso kwa nthawi yaitali. Panthawiyo ndi ocepa cabe amene anadziŵa kuti ciŵelengelo ca Mboni masiku ano, cingaculuke kuposa pa 170,000. Ndipo ena mwa alaliki a Ufumu akhama amenewa ndi Mboni zocokela kumaiko ena zimene zinapita ku Russia kuti zikathandize pa nchito yokolola. (Mat. 9:37, 38) Tiyeni timve zimene io akufotokoza.

ABALE ANADZIPELEKA KUKATHANDIZA NDI KULIMBIKITSA MIPINGO

M’caka cimene ciletso ca ku Russia cinatha, Matthew wa ku Great Britain anali ndi zaka 28. Nkhani ya pa msonkhano wacigawo m’caka cimeneco, inafotokoza kuti mipingo ya kum’maŵa kwa Ulaya ikufunika thandizo. Mkambi anapeleka citsanzo ca mpingo wa mumzinda wa St. Petersburg ku Russia umene unali ndi mtumiki wothandiza mmodzi ndipo unalibe mkulu. Ngakhale n’telo, ofalitsa anali kucititsa maphunzilo a Baibulo ambilimbili. Matthew anati: “Nkhaniyo itatha, sindinaleke kuganiza za ku Russia. Conco ndinapeleka pemphelo lacindunji kwa Yehova kuti andithandize kukwanilitsa colinga canga cokatumikila kumeneko.” Iye anasunga ndalama ndi kugulitsa zinthu zina zimene anali nazo. Pambuyo pake anasamukila ku Russia mu 1992. Kodi zinthu zinamuyendela bwanji?

Matthew

Matthew anati: “Ndinavutika kuti ndiphunzile cinenelo ndipo zinali zovuta kukambilana ndi anthu nkhani za m’Baibulo.” Vuto lina linali lakuti anali kusoŵa malo alendi okhala kwa nthawi yaitali. Iye anapitiliza kuti: “Ndinali kukhalila kusamukasamuka cakuti sindingakumbukile nthawi zimene ndinauzidwa mwadzidzidzi kuti ndicoke m’nyumba.” Mosasamala kanthu za mavuto amenewa Matthew anati: “Kutumikila ku Russia cinali cosankha cabwino kwambili pa zosankha zonse zimene ndinapangapo.” Anapitiliza kuti: “Ndaphunzila kudalila kwambili Yehova ndipo wakhala akunditsogolela pa njila zanga zonse.” M’kupita kwa nthawi, Matthew anayamikilidwa kukhala mkulu komanso mpainiya wapadela ndipo tsopano akutumikila pa ofesi ya nthambi pafupi ndi mzinda wa St. Petersburg.

Mu 1999, mbale Hiroo anatsiliza maphunzilo a Sukulu Yophunzitsa Utumiki ku Japan ali ndi zaka 25 ndipo panthawiyi, mmodzi wa aphunzitsi ake anamulimbikitsa kukatumikila ku dziko lina. M’bale Hiroo atamva za kusoŵa kwakukulu m’dziko la Russia anayamba kuphunzila cinenelo ca Cirasha. Kuonjezela pa kuphunzila cinenelo anacitanso cinthu cina cimene cinamuthandiza. Iye anati: “Podziŵa kuti ku Russia ndi kozizila kwambili ndinayamba ndayesa kukhala m’dzikolo kwa miyezi 6 ndipo ndinapita mu November n’colinga cakuti ndione ngati ndingakwanitse.” Iye ataona kuti wakwanitsa kukhala, anabwelela kwao ku Japan kuti akakonzekele zodzakhalilatu m’dzikoli. Panthawiyi anakhala ndi umoyo wosalila zambili n’colinga cakuti asunge ndalama kuti akakhaliletu ku Russia.

Hiroo ndi Svetlana

Hiroo wakhala zaka 12 ku Russia tsopano ndipo watumikila m’mipingo yosiyanasiyana. Pampingo wina analipo yekha mkulu ndipo anali kusamalila ofalitsa oposa 100. Pampingo winanso iye ndi amene anali kukamba nkhani zambili za mu Msonkhano wa Nchito. Anali kucititsanso Sukulu ya Ulaliki, Phunzilo la Nsanja ya Mlonda ndi kutsogoza Maphunzilo 5 a Buku a Mpingo. Iye anali kucitanso maulendo aubusa ambilimbili. Akaganizila zocitika zimenezo Hiroo anati: Zinali zosangalatsa kwambili kuthandiza abale ndi alongo kukhala olimba mwa kuuzimu.” Kodi kutumikila ku malo kumene kukufunika anchito ambili kwamukhudza bwanji Hiroo? Iye anati: “Ndikalibe kubwela ku Russia ndinali mkulu ndiponso mpainiya koma tsopano ndikuona kuti ubwenzi wanga ndi Yehova walimba kwambili. Ndaphunzila kudalila kwambili Yehova m’mbali zonse za moyo wanga.” Hiroo anakwatila Svetlana mu 2005 ndipo onse akutumikila monga apainiya.

Michael ndi Olga ali ndi Marina ndi Matthew

Matthew wa zaka 34 ndi m’bale wake Michael wa zaka 28 akhala ku Canada. Iwo atapita ku Russia kukaceza, anacita cidwi kuona anthu okondwelela amene anapezeka pa misonkhano koma panali abale ocepa cabe amene anali kucititsa misonkhanoyo. Matthew anati: “Ku mpingo umene ndinapitako tinasonkhana 200 koma misonkhano yonse inatsogozedwa ndi mkulu mmodzi wa cikulile ndi mtumiki wothandiza mmodzi wacinyamata. Poona mmene zinthu zinalili ndinaganiza zokathandiza abalewo.” Conco mu 2002, iye anasamukila ku Russia.

Patapita zaka zinai, Michael anapita ku Russia ndipo anaona kuti abale anali kufunikabe. Iye monga mtumiki wothandiza, anapatsidwa nchito yosamalila maakaunti, mabuku ndi magawo. Anapemphedwanso kucita nchito ya kalembela wa mpingo, kukamba nkhani za anthu onse ndi kuthandiza kukonzekeletsa misonkhano ikuluikulu komanso kuthandiza kumanga Nyumba za Ufumu. Komabe, mipingo yambili ikali kufunika thandizo. Ngakhale kuti kusamalila maudindo ambili ndi nchito yovuta kwambili, Michael amene akutumikila monga mkulu tsopano akupitiliza kunena kuti: “Kuthandiza abale kwandicititsa kukhala wokhutila. Imeneyi ndi njila yabwino kwambili yogwilitsila nchito moyo wanga.”

Matthew anakwatila Marina ndipo Michael anakwatila Olga. Mabanjawa limodzi ndi anchito ena odzipeleka, anapitiliza kuthandiza mipingo kupita patsogolo.

ALONGO ACANGU AKUTHANDIZA PA NCHITO YOKOLOLA

Tatyana

Pamene Tatyana anali ndi zaka 16 mu 1994, apainiya apadela 6 ocokela ku Czech Republic, Poland ndi Slovakia anasamukila ku Ukraine kukatumikila mu mpingo wao. Iye amawakumbukila bwino kwambili ndipo anati: “Amenewo anali apainiya acangu, ofikilika, okoma mtima ndipo anali kulidziŵa bwino kwambili Baibulo.” Iye anaona mmene Yehova anawadalitsila kaamba ka mzimu wodzipeleka umene anali nao moti anakamba kuti, ‘Inenso ndifuna ndikacite zofanana ndi zimenezo.’

Atalimbikitsidwa ndi citsanzo ca apainiyawo, Tatyana akakhala pa holide anali kupita ndi ena ku magawo akutali a ku Ukraine ndi Belarus kumene Mboni sizinalalikileko. Iye anali kusangalala kwambili ndi ulaliki wotelowo cakuti anapanga zolinga zakuti aonjezele utumiki wake mwa kusamukila ku Russia. Mlongoyu anaganiza zopita ku dzikolo kuti akacezele mlongo wina amene nayenso anacokela kudziko lina. Tatyana anakhala kumeneko kwa nthawi yocepa ndi colinga cakuti apeze nchito imene idzamuthandize pocita upainiya. Ndiyeno mu 2000, iye anasamukila ku Russia. Kodi kucita zimenezi kunali kopepuka?

Tatyana anafotokoza kuti: “Popeza kuti ndinalibe nyumba yangayanga, ndinafunika kukhala m’nyumba ya lendi. Zimenezi zinali zovuta kwambili, cakuti nthawi zina ndinali kulakalaka kubwelela kwathu. Koma nthawi zonse Yehova anali kundithandiza kuzindikila kuti ndidzapindula kwambili ndikapitiliza kutumikila.” Tatyana tsopano akutumikila monga mmishonale ku Russia. Iye anamaliza ndi mau akuti: “Pa zaka zonse zimene ndatumikila kuno, ndasangalala kwambili ndipo ndapeza mabwenzi ambilimbili. Koposa zonse, cikhulupililo canga calimba kwambili.”

Masako

Masako wa ku Japan amene ali ndi zaka za m’ma 50, kwa nthawi yaitali anali kulakalaka utumiki waumishonale koma zinali kuoneka kuti ndi zosatheka kaamba ka vuto la thanzi lake. Ngakhale n’telo, pamene vuto lake linacepako, anaganiza zopita ku Russia kuti akathandize pa nchito yokolola. Ngakhale kuti zinali zovuta kupeza malo abwino okhala ndi nchito yamaziko, iye anali kuphunzitsa Cijapanizi ndi kugwila nchito yoyeletsa kuti azizithandizila pocita upainiya. Kodi n’ciani camuthandiza kupitiliza utumiki?

Masako watumikila ku Russia kwa zaka zoposa 14. Akaganizila zaka zimenezo, amanena kuti: “Mavuto amene ndakumana nao sangapambane cimwemwe cimene ndapeza. Kulalikila kumalo amene kukufunika ofalitsa Ufumu ambili kumacititsa munthu kukhala ndi umoyo wosangalatsa kwambili.” Anaonjezela kuti: “Kwa zaka zonsezi, Yehova wandipatsa cakudya, zovala ndi malo ogona. Kwa ine, zimenezi n’cozizwitsa.” Kuonjezela pa kutumikila kumalo osoŵa m’dziko la Russia, Masako anagwilanso nao nchito yokolola ku Kyrgyzstan. Iye amathandizilanso tumagulu twa cinenelo ca Cingelezi, Cichainizi ndi Ciwiga. Tsopano iye akutumikila monga mpainiya ku St. Petersburg.

MABANJA AKUTHANDIZA NDIPO ALANDILA MADALITSO

Inga ndi Mikhail

Cifukwa ca mavuto a zacuma, nthawi zambili mabanja amasamukila kudziko lina kuti akapezeko thandizo. Komabe pali mabanja ena amene amasamukila kudziko lina kaamba ka zinthu za kuuzimu mofanana ndi mmene Abrahamu ndi Sara anacitila. (Gen. 12:1-9) Mwacitsanzo, Mikhail ndi Inga, anasamukila ku Russia kucokela ku Ukraine mu 2003. Atangofika kumeneko anapeza anthu amene anali kufuna kuphunzila coonadi ca m’Baibulo.

Mikhail anakamba kuti: “Panthawi ina tinapita kukalalikila m’dela limene Mboni zikalibe kulalikilamo, tinapeza mwamuna wina wacikulile amene anatifunsa kuti, ‘Kodi ndinu alaliki?’ Ife titayankha kuti inde, anapitiliza kuti: ‘Ndinali kudziŵa kuti tsiku lina mudzafika pa nyumba panga. Cifukwa sizingatheke kuti mau a Yesu asakwanilitsidwe.’ Mwamunayo anagwila mau a Yesu a pa Mateyu 24:14.” Mikhail anapitiliza kuti: “ M’dela limenelo tinapezanso kagulu ka azimai ena pafupifupi 10 a chechi ca Baptist amene anali ndi njala ya coonadi. Iwo anali ndi buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha limene anali kugwilitsa nchito pophunzila Baibulo mlungu uliwonse. Kwa maola ambili tinayankha mafunso ao ndi kuimba nao nyimbo za Ufumu ndipo tinadyela limodzi cakudya ca madzulo. Cocitika cimeneci ndi cimodzi mwa zocitika zosangalatsa kwambili ndiponso cosaiŵalika.” Mikhail ndi Inga anavomeleza kuti kutumikila ku dela limene kukufunika ofalitsa Ufumu ambili kwawathandiza kuyandikila kwambili kwa Yehova, kukonda kwambili anthu ndi kukhala ndi moyo wokhutilitsa. Iwo tsopano akugwila nchito ya m’dela.

Oksana, Aleksey, ndi Yury

Mu 2007, m’bale Yury ndi mkazi wake Oksana, a zaka za m’ma 30 ndi mwana wao Aleksey amene ali ndi zaka 13 a kudziko la Ukraine, anapita kukaceza ku ofesi ya nthambi ya ku Russia. Kumeneko anaona mapu a magawo ena akuluakulu a m’dzikolo amene kulibe alaliki. Oksana anati “Titaona mapuyo tinazindikila kuti ku Russia kukufunikila alaliki a Ufumu kuposa ndi kale lonse. Zimenezi zinatipangitsa kutsimikiza mtima kuti tisamukile m’dzikoli.” N’ciani cina cinawathandiza? Mkazi wake anati: “Kuŵelenga nkhani za m’mabuku athu monga nkhani zakuti, ‘Kodi Mungakatumikile Kudziko Lina?’ Kwatithandiza kwambili. * Ofesi ya nthambi itatiuza malo amene tingapiteko, tinapita kumaloko kuti tikafune nyumba yokhalamo ndi nchito.” Mu 2008 anasamukila ku Russia.

Poyamba, kupeza nchito kunali kovuta. Vuto lina linali lakuti banjali linali kungokhalila kusamukasamuka. M’bale Yury anati: “Nthawi zambili tinali kupemphela kwa Yehova kuti atithandize kukhala olimba ndi kuti tipitileze kumudalila pogwila nchito yolalikila. Yehova anatisamalila kwambili pamene tinaika zinthu za Ufumu patsogolo. Ndipo utumiki umenewu walimbitsa banja lathu.” (Mat. 6:22, 33) Nanga utumiki umenewu wakhudza bwanji wacicepele Aleksey? Oksana anakamba kuti: “Utumiki umenewu wamuthandiza kwambili, cakuti anadzipeleka kwa Yehova ndi kubatizidwa ali ndi zaka 9. Cifukwa ca kuona kufunika kwa alaliki a Ufumu, Aleksey amacita upainiya wothandiza akakhala pa holide. Iye amakonda ulaliki ndipo ndi wakhama kwambili. Zimenezi zimatisangalatsa kwambili.” Yury ndi Oksana akucita upainiya wapadela.

“CIMENE NDIMADANDAULA”

Monga mmene ndemanga za abale ndi alongo ogwila nchito yokolola zaonetsela, kusamukila kudela lina n’colinga cofutukula utumiki wathu kumafuna kudalila kwambili Yehova. N’zoona kuti abale ndi alongo amene amasamukila kumadela kumene kukufunika alaliki a Ufumu ambili amakumana ndi mavuto. Komabe amakhala ndi cimwemwe cacikulu kwambili akamalalikila uthenga wa Ufumu kwa anthu amene amaulandila. Kodi inuyo mungakwanitse kukathandiza pa nchito yokolola mwa kusamukila kumalo amene kukufunika ofalitsa Ufumu ambili? Ngati mungasankhe kucita zimenezi, mungamve mmene Yury anamvelela atapanga cosankha cokatumikila kumalo amene kukufunika anchito ambili. Iye anati: “Cimene ndimadandaula naco n’cakuti ndinayamba utumikiwu mocedwa.”

^ par. 20 Onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 1999, masamba 23-27.