Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kufatsa​—Kumaonetsa Nzelu

Kufatsa​—Kumaonetsa Nzelu

Tsiku lina, Toñi amene amasamalila okalamba, anagogoda pakhomo ndipo mzimayi wa zaka za m’ma 50 anatsegula citseko. Mzimayiyo anayamba kunyoza Toñi na kumukalipila poona monga wafika mocedwa kudzasamalila amayi okalamba a mzimayiyo. Koma si zoona kuti Toñi anafika mocedwa ku nchito. Ngakhale n’conco, Toñi anapepesabe kwa mzimayiyo.

ULENDO winanso, mzimayiyo anakalipilanso Toñi. Kodi Toñi anacitanji? Iye anati: “Zinali zovuta kwambili. Panalibe cifukwa coninyozela na kunikalipila.” Koma Toñi anapepesanso na kuuza mzimayiyo kuti anali kumvetsa mavuto amene anali kukumana nawo.

Mukanakhala Toñi, kodi mukanacita ciani? Kodi mukanaonetsa kufatsa? Kapena kodi zikanakuvutani kulamulila mkwiyo wanu? Kukamba zoona, si copepuka kukhala wofatsa m’zocitika ngati zimenezi. Tikapanikizika kapena ena akatiputa, zimakhala zovuta kukhalabe wofatsa.

Komabe, Baibo imalimbikitsa Akhiristu kukhala ofatsa. Ndipo Mau a Mulungu amagwilizanitsa khalidwe limeneli ndi nzelu. Yakobo anafunsa kuti: “Kodi pakati panu pali aliyense wanzelu ndi womvetsa zinthu? Ameneyo ayenela kukhala ndi khalidwe labwino limene limasonyeza kuti amacita ciliconse mofatsa ndipo kufatsa kwake kumacokela mu nzelu.” (Yak. 3:13) Kodi kufatsa kumaonetsela motani nzelu yocokela kumwamba? Nanga tingakhale nalo bwanji khalidwe laumulungu limeneli?

MAPINDU A KUKHALA WOFATSA

Kufatsa kungabweze mkwiyo. “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mau opweteka amayambitsa mkwiyo.”Miy. 15:1.

Kuyankha mwaukali kumakulitsa vuto, cifukwa kumakhala ngati kukolezela moto. (Miy. 26:21) Koma kuyankha mofatsa nthawi zambili kumabweza mtima pansi. Kungafeŵetse mtima wa munthu wokwiya.

N’zimene zinatika kwa Toñi. Mzimayi uja ataona mayankhidwe ofatsa a Toñi, anagwetsa misozi. Anafotokozela Toñi kuti anali na mavuto ake komanso a m’banja. Toñi analalikila mzimayiyo ndi kuyamba kuphunzila naye Baibo. Zonsezi n’cifukwa ca khalidwe lake la kufatsa ndi la mtendele.

Kufatsa kungatipatse cimwemwe. “Odala ndi anthu amene ali ofatsa, cifukwa adzalandila dziko lapansi.”Mat. 5:5.

N’cifukwa ciani anthu ofatsa amakhala acimwemwe? Cifukwa cokhala ndi khalidwe la kufatsa, ambili amene kale anali aukali lelo ni acimwemwe. Anasintha umoyo wawo, ndipo akuyembekezela tsogolo labwino. (Akol. 3:12) Adolfo, woyang’anila dela wa ku Spain, akumbukila bwino mmene umoyo wake unalili asanaphunzile coonadi.

Adolfo anati: “Umoyo wanga unalibe colinga cililonse. Nthawi zambili, n’nali kukhala wolusa cakuti anzanga ena anali kuniopa cifukwa ca khalidwe laciwawa. Tsiku lina zinthu zinafika poipa. Pa ndeu, ananilasa ndi mpeni ka 6 cakuti n’nacuca magazi kutsala pang’ono kufa.”

Koma lomba, Adolfo amalimbikitsa ena kukhala ofatsa mwa mau na citsanzo cake cabwino. Ambili amakopeka na khalidwe lake labwino. Adolfo amati ni wokondwela kwambili ndi mmene wasinthila umoyo wake. Ndipo amayamikila Yehova cifukwa com’thandiza kukhala wofatsa.

Kufatsa kumakondweletsa Yehova. “Mwana wanga, khala wanzelu ndi kukondweletsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”Miy. 27:11.

Yehova amatonzedwa ndi mdani wake wamkulu, Mdyelekezi. Mulungu ali na cifukwa cabwino cokhalila wokwiya cifukwa ca citonzo cimeneco. Komabe, Baibo imachula Yehova kuti ni “wosakwiya msanga.” (Eks. 34:6) Pamene tiyesetsa kutengela khalidwe la Mulungu losakwiya msanga ndi kufatsa, timaonetsa nzelu, ndipo Yehova amakondwela kwambili.—Aef. 5:1.

M’dzikoli anthu ambili ni aukali. Timakumana ndi anthu “odzimva, odzikweza, onyoza, . . . onenela anzawo zoipa, osadziletsa, [ndi] oopsa.” (2 Tim. 3:2, 3) Koma zimenezi siziyenela kulepheletsa Mkhiristu kukhala wofatsa. Mau a Mulungu amatikumbutsa kuti ‘nzelu yocokela kumwamba ni yamtendele ndi yololela.’ (Yak. 3:17) Ngati tikhala amtendele ndi ololela, timaonetsa kuti tili na nzelu zaumulungu. Nzelu imeneyi idzatithandiza kuyankha mofatsa ngati wina watikalipitsa. Idzatithandizanso kukhala pa ubwenzi wathithithi na Yehova, Gwelo la nzelu zosatha.