Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mmene Mungapindulile na Cisamalilo ca Mulungu

Mmene Mungapindulile na Cisamalilo ca Mulungu

Mulungu analenga thupi lathu m’njila yakuti izikwanitsa kudzicilitsa lokha modabwitsa kwambili. Pamene thupi lathu lacekeka, kumyuka, kapena kulasiwa, “limayamba kudzikonza mocititsa cidwi, kupoletsa zilonda zikulu-zikulu komanso zing’ono-zing’ono.” (Johns Hopkins Medicine) Mwamsanga thupi limayamba kudzikonza kuti magazi asataike ambili, kukonza cilonda, na kulimbitsa minofu.

GANIZILANI IZI: Ngati Mlengi anakonza matupi athu kuti azipoletsa okha zilonda, kodi sitingakhale na cidalilo m’lonjezo lake lakuti adzakonzanso maganizo athu kuti tileke kudziimba mlandu? Wamasalimo analemba kuti, “Iye amacilitsa anthu osweka mtima, ndipo amamanga zilonda zawo zopweteka.” (Salimo 147:3) Koma ngati mumakhala na maganizo odziimba mlandu, kodi n’ciani cingakuthandizeni kukhala na cidalilo cakuti Yehova adzamanga zilonda zanu, pali pano komanso m’tsogolo?

ZIMENE BAIBO IMATIPHUNZITSA PA CIKONDI CA MULUNGU

Mulungu anatilonjeza kuti: “Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.” (Yesaya 41:10) Munthu amene amadziŵa kuti Yehova amasamala za iye, amakhala na mtendele wa m’maganizo komanso mphamvu zom’thandiza kupilila mavuto amene angakumane nawo. Ponena za mtendele wa m’maganizo umenewu, mtumwi Paulo anati ni “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” Iye anawonjezelanso kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:4-7, 9, 13.

Malemba amatithandiza kukhala na cikhulupililo m’malonjezo a Yehova okhudza tsogolo la anthu. Mwacitsanzo, Chivumbulutso 21:4, 5 (imene yagwidwa mau papeji yotsatila) imatiuza zimene adzacita, komanso cifukwa cake tingakhale na cidalilo cakuti adzacitadi zimenezo:

  • “Iye adzapukuta misozi yonse” m’maso mwa anthu. Yehova adzacotsapo mavuto na nkhawa zathu zonse, ngakhale zimene zingaoneke zocepa kwa ena.

  • “Wokhala pampando wacifumu” mu ulemelelo wa wakumwamba, Mfumu Yamphamvuzonse m’cilengedwe conse, adzaonetsa mphamvu na ulamulilo wake, mwa kucotsapo mavuto na kutipatsa zonse zofunikila.

  • Yehova amatitsimikizila kuti malonjezo ake ni “odalilika ndi oona.” Kutanthauza kuti malinga na mbili yake, Mulungu woona waonetsa kuti amakwanilitsa malonjezo ake.

“‘Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.’ Ndipo wokhala pampando wacifumu anati: ‘Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.’ Ananenanso kuti: ‘Lemba, pakuti mawu awa ndi odalilika ndi oona.’”—Chivumbulutso 21:4, 5.

Cilengedwe komanso Baibo, zimaonetsa makhalidwe a Atate wathu wakumwamba. Popanda mau, cilengedwe cimatilimbikitsa kudziŵa Mulungu kuti akhale Bwenzi lathu lapamtima. Koma Baibo imatiuza mwacindunji kuti, “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yakobo 4:8) Machitidwe 17:27 imakamba kuti: “Iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”

Mukapitiliza kuphunzila za Mulungu, mudzalimbitsa cidalilo canu mwa iye kuti “amakudelani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Kodi kukhala na cidalilo monga ici mwa Yehova kuli na mapindu otani?

Ganizilani cocitika ca Toru wa ku Japan. Iye analeledwa na amayi ake acikhristu, koma analoŵa m’gulu la zigaŵenga za ku Japan. Iye anafotokoza kuti, “N’nali kukhulupilila kuti Mulungu sanikonda, ndipo n’nali kuona kuti imfa za anansi anga maka-maka za amene n’nali kuwakonda kwambili, zinali kucitika kuti nilangidwe.” Toru anavomeleza kuti cifukwa ca imfa za anansi ake komanso maganizo akuti zinali cilango kwa iye, zinam’pangitsa kukhala “munthu wouma mtima ndi wopanda cifundo.” Ponena za colinga cake, iye anati, “N’nafika poganiza za kupha munthu wochuka kwambili kuposa ine n’colinga cakuti nidzipangile dzina ngakhale kuti zimenezi zikanacititsa kuti nife msanga.”

Koma pamene iye na mkazi wake, Hannah, anaphunzila Baibo, Toru anasintha kwambili umoyo wake. Anasinthanso mmene anali kuonela zinthu. Hannah anati, “N’nadzionela nekha mmene mwamuna wanga anali kusinthila.” Tsopano, Toru amakamba motsimikiza kuti: “Kuli Mulungu amene amasamaladi za aliyense wa ise payekha. Iye safuna kuti wina aliyense afe, ndipo ni wofunitsitsa kukhululukila amene alapa macimo awo mocokela pansi pamtima. Amamvetsela ku zinthu zimene sitingauze wina aliyense kupatulapo iye na zinthu zimene palibe amene angazimvetsetse. Posacedwa, Yehova adzacotsapo mavuto onse na zoŵaŵa. Ngakhale pali pano, iye amatithandiza m’njila zimene sitiyembekezela. Amatisamalila na kutithandiza pamene talefuka.”—Salimo 136:23.

Monga mmene cocitika ca Toru caonetsela, kudziwa kuti Mulungu angacotsepo mavuto onse, na kuti posacedwa adzapukuta misozi yonse, kumatipatsa ciyembekezo cotsimikizika. Kumatithandizanso kukhala na umoyo wabwino panthawi ino. Inde, ngakhale m’dziko lodzala na mavuto, mungapindule na cisamalilo cacikondi ca Mulungu.