Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nanga Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulila Dziko Lapansi?

Nanga Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulila Dziko Lapansi?

Ena mwa otsatila a Yesu okhulupilika anafuna kudziŵa kuti ni liti pamene Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila. Yesu anayankha funso lawo mwa kuŵauza kuti sadzadziŵa nthawi yeni-yeni pamene udzayamba kulamulila padziko lapansi. (Machitidwe 1:6, 7) Koma poyamba, iye anali ataŵauzilatu kuti otsatila ake akadzaona zocitika zina zikucitika zonse pa nthawi imodzi, ‘adzadziwe kuti Ufumu wa Mulungu wayandikila,’ ndipo nthawi yakuti uyambe kulamulila dziko yafika. —Luka 21:31.

KODI N’ZOCITIKA ZITI ZIMENE YESU ANAKAMBILATU KUTI ZIDZACITIKA?

Yesu anati: “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzacitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala milili ndi njala.” (Luka 21:10, 11) Zocitika zonsezi pamodzi zimapanga cizindikilo cosakaikitsa. Ndipo kucitika pa nthawi imodzi kwa zinthu zimenezi kumaonetsa kuti “Ufumu wa Mulungu wayandikila.” Kodi zinthu zimenezi zikucitikadi pa nthawi imodzi, komanso kuonekela padziko lonse? Tiyeni tione umboni wake.

1. NKHONDO

Mu 1914, nkhondo yaikulu inabuka imene siinacitikepo m’mbili yonse ya anthu! Akatswili ambili yakale amakamba kuti caka ca 1914 cinali posinthila mbili ya anthu, cifukwa m’pamene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inabuka. Kwa nthawi yoyamba pa nkhondoyi, anthu anaseŵenzetsa pamlingo waukulu kwambili zida zankhondo monga akasinja, mabomba oponyewa na ndeke zankhondo, mfuti zowombela zipolopolo mopitiliza, mphepo yapoizoni, na zida zina zakupha. Pambuyo pake panabukanso nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, imene inabweletsa mabomba anyukiliya, monga zida zatsopano. Kucokela mu 1914 anthu akhala akucita nkhondo m’malo osiyana-siyana, ndipo nkhondo zimenezi zimapha anthu ambili.

2. ZIVOMEZI

Buku lakuti Britannica Academic linati: “Caka ciliconse kumacitika zivomezi pafupi-fupi 100 zimene zimawononga kwambili.” Komanso, malipoti a bungwe la United States Geological Survey anati: “Malinga n’zimene tapeza kwa nthawi yaitali (kucokela ca m’ma 1900) timayembekezela zivomezi zikulu-zikulu pafupi-fupi 16 caka ciliconse.” Ena angakambe kuti kuculuka kwa zivomezi kumeneku, n’cifukwa cabe cakuti masiku ano pali njila zamakono zodziŵila zivomezi zimene zimacitika kusiyana na kale. Koma mfundo ni yakuti zivomezi zazikulu padziko lonse zimabweletsa mavuto aakulu kwambili komanso imfa, kuposa kale lonse.

3. NJALA

Padziko lonse, njala imabwela cifukwa ca nkhondo, katangale, kugwa kwa cuma, kusayendetsa bwino zaulimi, kapena kusakonzekela nyengo zoipa. “Lipoti la 2018” la bungwe la World Food Programme limati: “Padziko lonse lapansi, anthu 821 miliyoni amavutika na njala ndipo anthu 124 miliyoni pa anthu amenewo alibiletu cakudya.” Caka ciliconse ana pafupi-fupi 3.1 miliyoni amafa cifukwa ca kupeleŵela kwa cakudya m’thupi. Pa ciŵelengelo ca ana onse amene anafa padziko lonse mu 2011, 45 pelesenti anafa cifukwa ca njala.

4. MATENDA KOMANSO MILILI

Buku lofalitsidwa na bungwe la World Health Organization limati: “M’zaka zino za m’ma 2000, taona milili ikulu-ikulu. Matenda akale monga kolela, matenda oyambukila komanso cikasu (yellow fever) ayambanso, ndiponso kwabuka matenda ena atsopano monga mlili wa fuluwenza, Ebola, na malungo ochedwa Zika. Kwabwelanso matenda opangitsa munthu kuvutika kupuma ochedwa SARS komanso MERS.” Ngakhale kuti asayansi na madokotala aphunzila zambili za matenda, iwo sakwanitsa kupeza mankhwala ocilitsa matenda onse.

5. NCHITO YOLALIKILA PADZIKO LONSE

Yesu anachulanso mbali ina ya cizindikilo pamene anakambilatu kuti: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Pamene dzikoli likumana na mavuto oopsa, anthu opitilila 8 miliyoni ocokela ku mitundu yonse, akulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu m’maiko 240 mu vitundu vopitilila 1,000. Izi sizinacikepo m’mbili yonse ya anthu.

KODI CIZINDIKILO CIMENECI CITIKHUDZA BWANJI?

Zocitika zimene zimapanga cizindikilo cimene Yesu anapeleka zikucitika masiku ano. N’cifukwa ciani kudziŵa zimenezi n’kofunika? Cifukwa Yesu anati: “Mukadzaona zimenezi zikucitika, mudzadziwe kuti Ufumu wa Mulungu wayandikila.”—Luka 21:31.

Posacedwa, Ufumu umenewu udzaonetsetsa kuti cifunilo ca Mulungu cacitika padziko lapansi

Cizindikilo cimene Yesu anapeleka, komanso nthawi ya zocitika za m’Baibo, zimatithandiza kumvetsa bwino kuti Mulungu anakhazikitsa Ufumu wake kumwamba mu 1914. * Panthawiyo, anaika Mwana wake Yesu Khristu kukhala Mfumu. (Salimo 2:2, 4, 6-9) Posacedwa, Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulila padziko lapansi, ndipo udzacotsapo maulamulilo onse a anthu, na kupanga dzikoli kukhala paradaiso kuti anthu akakhalepo kwamuyaya.

Posacedwa, mawu a m’pemphelo lacitsanzo amene Yesu anaphunzitsa adzakwanilitsidwa, akuti: “Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba, cimodzimodzinso pansi pano.” (Mateyu 6:10) Koma kodi Ufumu umenewu wakhala ukucitanji kucokela pamene unayamba kulamulila mu 1914? Nanga tingayembekezele zotani Ufumu umenewu ukadzaloŵa m’malo maulamulilo a anthu?

^ ndime 17 Kuti mudziŵe zambili zokhudza caka ca 1914, onani buku lakuti, Zimene Baibulo ingatiphunzitse yolembedwa na Mboni za Yehova, zakumapeto 22.