Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

TENGELANI CIKHULUPILILO CAO | RABEKA

“Inde Ndipita”

“Inde Ndipita”

RABEKA anayamba kuona malo a miyala pamene anali pa ulendo. Patapita milungu yocepa, iye anayamba kuzoloŵela kukwela pa ngamila. Dziko la Harana kumene iye anabadwila, linali kutali kwambili kuloŵela kumpoto koma ca kum’mawa. Mwina iye sadzaonanso banja lake. Iye anali ndi mafunso ambili okhudza tsogolo lake, makamaka pamene anatsala pang’ono kufika.

Gulu la apaulendo linadutsa mzinda wa Kanani ndi nkhalango yoopsa ya m’dziko la Negebu. (Genesis 24:62) Rabeka ayenela kuti anaona nkhosa. Dziko limeneli linalibe conde cabwino colimapo, koma linali ndi malo abwino odyetselapo ziŵeto. Munthu wacikulile amene anali kutsogolela anali kulidziŵa bwino dzikoli. Iye anali wosangalala cifukwa ca nkhani yabwino imene anafuna kuuza mbuye wake, yakuti Rabeka adzakhala mkazi wa Isaki. Rabeka ayenela kuti anali ndi mafunso ambili okhudza mmene umoyo wake udzakhalila m’dzikolo. Kodi Isaki amene anali kudzakhala mwamuna wake anali munthu wotani, popeza anali asanaonanepo? Kodi Isaki adzamukonda Rabeka? Nanga, kodi Rabeka adzamukonda mwamunayo?

M’maiko ambili masiku ano, kusankhila munthu wokwatilana naye kumaoneka kwacilendo. Koma m’maiko ena, n’kofala kwambili. Mosasamala kanthu za mmene munakulila, mungavomeleze kuti Rabeka anali kupita kumalo amene sanali kudziŵa. Iye anali mkazi wolimba mtima ndiponso wacikhulupililo. Zinthu zikamasintha paumoyo wathu, timafunika kukhala ndi makhalidwe amenewa. Koma pali makhalidwe enanso okhumbilika ndi ocititsa cidwi, kuonjezela pa cikhulupililo cimene Rabeka anali naco.

“NDITUNGILANSO MADZI NGAMILA ZANU”

Kusintha kwa zinthu pa umoyo wa Rabeka kunayamba ndi zinthu zimene anazoloŵela kucita. Iye anakulila ku Harana, mumzinda wa Mesopotamiya. Makolo ake anali osiyana kwambili ndi anthu a ku Harana. Iwo sanali kulambila mulungu wa mwezi wochedwa Sini. Koma anali kulambila Mulungu wao, Yehova.—Genesis 24:50.

Rabeka anali mkazi wokongola, koma sanali waulesi, zimene zikanacititsa kukongola kwake kukhala kopanda phindu. Iye anali mkazi wauzimu, ndipo anali wamakhalidwe abwino. Banja lake linali lolemela cakuti linali ndi anchito, koma Rabeka sanaleledwe ngati mfumukazi. M’malomwake, anali kugwila nchito mwamphamvu. Mofanana ndi akazi ambili a m’nthawiyo, Rabeka anali ndi nchito zambili zogwila, monga kutunga madzi a banja lonse. M’madzulo mulimonse, iye anali kunyamula mtsuko paphewa lake ndi kupita ku citsime.—Genesis 24:11, 15, 16.

Tsiku lina madzulo atanyamula madzi mu mtsuko wake, mwamuna wina wacikulile anathamanga kudzakumana naye. Mwamunayo anati: “Conde ndipatse madzi a mumtsuko wako ndimweko pang’ono.” Iye anapempha madziwo mwaulemu ndi modzicepetsa. Rabeka anazindikila kuti mwamunayo wacokela kutali. Conco, mwamsanga anatula pansi mtsuko ndi kupatsa mwamunayo madzi kuti amwe. Iye anaona kuti mwamunayo alinso ndi ngamila 10 zimene zinali gone pafupi ndi comwelamo ziŵeto, cimene munalibe madzi. Cifukwa ca mmene mwamunayo anali kumuyang’anila, Rabeka anayesetsa kukhala woolowa manja mmene angathele. Conco, iye anati: “Nditungilanso madzi ngamila zanu mpaka zitamwa mokwanila.”—Genesis 24:17-19.

Onani kuti Rabeka sanangodzipeleka kupatsa cabe madzi ngamila 10, koma anaonetsetsa kuti ngamilazo zamwa madzi mokwanila. Ngamila imodzi ikakhala ndi ludzu kwambili, ingamwe madzi okwana malita 95. Ngati ngamila zonse 10 zinali ndi ludzu kwambili, ndiye kuti Rabeka anagwila nchito yotunga madzi kwa maola ambili. Zikuoneka kuti ngamila zimenezo zinali ndi ludzu kwambili. * Koma, kodi Rabeka anadziŵa kuti ngamilazo zinali ndi ludzu kwambili? Iyai. Iye anali wofunitsitsa kugwila nchito mwakhama kuti aonetse kuti waceleza mwamuna wacikulile amene anali wacilendo. Mwamunayo analandila thandizo lake. Ndiyeno, iye anali kuyang’anitsitsa Rabeka pamene anali kuthamangathamanga ndi mtsuko wa madzi kuti adzaze comwelamo ziŵeto.—Genesis 24:20, 21.

Rabeka anali kugwila nchito mwakhama ndipo anali woceleza

Citsanzo ca Rabeka n’colimbikitsa kwambili masiku ano. Tikukhala m’dziko limene muli anthu odzikonda kwambili. Malinga ndi zimene zinanenedwelatu, anthu ndi “odzikonda,” osafuna kuthandiza anzao. (2 Timoteyo 3:1-5) Akristu amene akufuna kuthetsa khalidweli, angacite bwino kuganizila citsanzo ca m’Baibulo ca mkazi wakaleyu, amene anali kuthamangathamanga ku citsime kukatunga madzi.

Rabeka anaona mmene mwamuna wacikulile anali kumuyang’anila. Kuyang’ana kwake sikuti kunali kolakwika, koma zinaonetsa kuti anadabwa, ndipo anakondwela ndi kudzipeleka kwa Rabeka. Rabeka atamaliza kutunga madzi, mwamunayo anam’patsa mphatso za mtengo wapatali. Ndiyeno mwamunayo anafunsa Rabeka kuti: “Kodi ndiwe mwana wa ndani? Conde ndiuze. Kodi kunyumba kwa bambo ako kuli malo oti tikhoza kugonako?” Atamuuza za banja lake, mwamunayo anakondwela kwambili. Mwacimwemwe mtsikanayo anati: “Cakudya ca ziŵeto tili naco cambili, komanso malo ogona alipo.” Kumeneko kunali kuceleza kumene iye anaonetsa mwamunayo ndi ena amene anali naye. Conco, Rabeka anathamangila kunyumba kwa mai ake kukawafotokozela zonse zimene zinacitika.—Genesis 24:22-28, 32.

Apa, n’zoonekelatu kuti Rabeka anaphunzitsidwa kukhala woceleza. Limeneli ndi khalidwe limene likuzimililika masiku ano. Ndipo ici ndi cifukwa cina cimene tiyenela kutengela citsanzo ca mkazi wokoma mtima ameneyu. Kukhulupilila Mulungu kuyenela kutilimbikitsa kukhala oceleza. Yehova ndi woceleza, amapatsa moolowa manja kwa onse ndipo amafuna kuti olambila ake azicita cimodzimodzi. Tikamaceleza anthu amene sangatibwezele zilizonse, timasangalala cifukwa timakondweletsa Atate wathu wakumwamba.—Mateyu 5:44-46; 1 Petulo 4:9.

“UKAM’TENGELE MWANA WANGA MKAZI”

Kodi mwamuna wacikulile amene anali pa citsime ndani? Anali mtumiki wa Abulahamu, m’bale wa agogo ake a Rabeka. Iye analandilidwa ndi Betuele, atate ake Rabeka. Dzina la mtumiki ameneyu ndi Eliezere. * Atamulandila, anamupatsa cakudya, koma iye anakana kudya mpaka atafotokoza cimene anabwelela. (Genesis 24:31-33) Ganizilani kuti mukumuona akulankhula mwacimwemwe, popeza kuti anali ataona cizindikilo camphamvu cakuti Mulungu wake, Yehova anam’dalitsa paulendo wake wofunika. N’cifukwa ciani tikutelo?

Ganizilani kuti mukuona Eliezere akufotokoza nkhani yonse kwa Betuele, bambo a Rabeka pamodzi ndi mlongosi wake Labani, ndipo io akumvetsela mwachelu. Iye akuwauza kuti Yehova anadalitsa kwambili Abulahamu ku Kanani, ndi kuti Abulahamu ndi Sara ali ndi mwana dzina lake Isaki amene anali kudzalandila coloŵa ca atate ake. Abulahamu anapatsa mtumiki wakeyu udindo waukulu wopita ku Harana, kwa acibale a Abulahamu kuti akatengele Isaki mkazi.—Genesis 24:34-38.

Abulahamu anacita pangano ndi Eliezere lakuti sadzatengela Isaki mkazi pakati pa akazi acikanani. N’cifukwa ciani? Cifukwa Akanani sanali kulemekeza ngakhale kulambila Yehova Mulungu. Abulahamu anali kudziŵa kuti Yehova adzaononga anthu amene anali kucita zinthu zoipa. Iye sanafune kuti mwana wake wokondedwa Isaki, akwatile mkazi pakati pa anthu a makhalidwe oipa amenewo. Anadziŵanso kuti mwana wake ndi amene anali kudzakwanilitsa malonjezo a Mulungu.—Genesis 15:16; 17:19; 24:2-4.

Eliezere anapitiliza kuuza amene anamulandila kuti, atafika pa citsime pafupi ndi Harana, anapemphela kwa Yehova Mulungu. Iye anapempha Yehova kuti amuthandize kusankha mkazi amene Isaki anafunika kukwatila. Nanga anacita bwanji zimenezi? Eliezere anapempha Mulungu kumutsimikizila kuti mkazi amene afuna kuti Isaki akakwatile akamupeze ku citsime. Akadzamupempha madzi akumwa, iye adzapatse Eliezere madzi ndi kumwetsa ngamila zake zonse. (Genesis 24:12-14) Kodi ndani anabwela ndi kucita ndendende zimenezo? Anali Rabeka. Ganizilani mmene Rabeka akanamvelela, akanamva nkhani imene Eliezere anafotokozela acibale ake.

Betuele ndi Labani anakondwela kwambili ndi nkhani ya Eliezere. Iwo anati: “Zimenezi zacokela kwa Yehova.” Malinga ndi mwambo, io anacita pangano la ukwati pakati pa Rabeka ndi Isaki. (Genesis 24:50-54) Kodi zimenezi zitanthauza kuti Rabeka analibe ufulu wokambapo pa nkhaniyi?

Kutatsala milungu yocepa kuti ayambe ulendo wake, Eliezere anafunsa Abulahamu za nkhaniyi kuti: “Bwanji ngati mkaziyo sakabwela nane?” Abulahamu anamuyankha kuti: “Udzamasuka ku lumbiloli.” (Genesis 24:39, 41) Banja la Betuele linali kulemekeza ufulu wa mtsikana. Eliezere anakondwela kwambili kuona kuti zinthu zonse zayenda bwino, cakuti tsiku lotsatila m’maŵa, anapempha kuti abwelele ku Kanani ndi Rabeka. Komabe, banjalo linafuna kuti Rabeka akhale nao kwa masiku ena 10. Pamapeto pake, nkhaniyo inatha motele: “Tiyeni timuitane mtsikanayo kuti timve zimene iyeyo anene.”—Genesis 24:57.

Tsopano Rabeka anafunika kupanga cosankha cacikulu pamoyo wake. Kodi iye adzakamba ciani? Kodi adzacondelela atate ake ndi mlongo wake kuti asamulole kupita kudziko lacilendo? Kapena, kodi adzaona kuti ndi mwai kutengako mbali pa zocitika zimene zinaonekelatu kuti zinali kutsogoleledwa ndi Yehova? Zimene anayankha zinaonetsa mmene anali kumvelela pa nkhani imene inali kudzasintha umoyo wake. Iye anati: “Inde ndipita.”—Genesis 24:58.

Iye anali ndi mtima wodzipeleka. Masiku ano, zimene timatsatila pankhani ya cikwati, zingakhale zosiyanako. Ngakhale n’telo, tingaphunzile zambili kwa Rabeka. Cinthu cimene cinali cofunika kwambili kwa iye ndi kuika patsogolo zofuna za Mulungu wake, Yehova, osati zofuna zake. Pankhani ya cikwati masiku ano, Mau a Mulungu amatipatsa malangizo othandiza. Amatiuza mmene tingasankhile munthu wokwatilana naye, ndi mmene tingakhalile mkazi kapena mwamuna wabwino. (2 Akorinto 6:14, 15; Aefeso 5:28-33) Conco, tingacite bwino kutengela citsanzo ca Rabeka kuti tizicita zinthu m’njila imene Mulungu afuna.

“KODI MUNTHU AKUBWELA APOYO . . . NDANI?”

Banja la Betuele linadalitsa Rabeka wokondedwa wao. Pambuyo pake, Rabeka, Debora, amene anali mlezi wake, ndi adzakazi ena anapitila pamodzi ndi Eliezere ndi anyamata ake. (Genesis 24:59-61; 35:8) Atayenda mtunda ndithu, dziko la Harana linayamba kubisika. Unali ulendo wautali pafupifupi makilomita 800, ndipo uyenela kuti unatenga milungu itatu. Ndipo ulendowu uyenela kuti unali wotopetsa. Rabeka anali kuzidziŵa ngamila, koma sitidziŵa ngati iye anali kudziŵa kukwela pa ngamila. Baibulo limakamba kuti banja lake linali ndi ziŵeto, koma sanali anthu amalonda oyenda ndi gulu la ngamila. (Genesis 29:10) Nthawi zambili, anthu amene amaphunzila kukwela pa ngamila amadandaula cifukwa ca mavuto amene amakumana nao, ngakhale paulendo waufupi.

Akamayenda, Rabeka anali kufunsa mafunso Eliezere, kuti adziŵe zambili zokhudza Isaki ndi banja lake. Ganizilani kuti mukuona mwamuna wacikulile akuuza Rabeka lonjezo la Yehova kwa bwenzi Lake, Abulahamu, pamene akuotha moto usiku. Kudzela mwa Abulahamu, Mulungu adzautsa mbeu imene idzabweletsa madalitso kwa anthu onse. Ganizilani cisangalalo cimene Rabeka anali naco mumtima, atazindikila kuti lonjezo la Yehova lidzakwanilitsidwa kudzela mwa Isaki, amene anali kudzakhala mwamuna wake, ndiponso mwa iye.—Genesis 22:15-18.

Rabeka anali wodzicepetsa, khalidwe lofunika kwambili

Pothela pake, tsiku limene tafotokoza kuciyambi kwa nkhani ino linafika. Pamene gulu la ngamila linali kudutsa m’dziko la Negebu, dzuŵa likuloŵa, Rabeka anaona mwamuna akuyenda m’chile. Mwamunayo anali kuoneka kuti ndi wokoma mtima. Nkhaniyo imati, “mwamsanga [Rabeka] anatsika pangamila,” sanayembekezele ngamila kugwada pansi. Atatelo anafunsa mtumiki kuti: “Kodi munthu akubwela apoyo kucokela m’chile kudzakumana nafe ndani?” Atauzidwa kuti ndi Isaki, iye anatenga nsalu yophimba kumutu n’kudziphimba nayo. (Genesis 24:62-65) N’cifukwa ciani anacita zimenezi? Zimene anacitazo zinali cizindikilo cakuti akulemekeza munthu amene anali kudzakhala mwamuna wake. Ulemu waconco, umaoneka wacikale masiku ano. Komabe, tonse amuna ndi akazi tingaphunzilepo kanthu pa kudzicepetsa kwa Rabeka. Ndani wa ife amene sangafune kukhala ndi khalidwe lofunika limeneli?

Isaki, mwamuna amene anali ndi zaka pafupifupi 40, anali akali kulila malilo a mai ake Sara, amene anali atamwalila zaka zitatu zapita. Conco, tingathe kuona kuti Isaki anali munthu wokoma mtima ndi wacifundo. Linali dalitso lalikulu kwa Isaki kukhala ndi mkazi wodziŵa nchito, woceleza, ndi wodzicepetsa. Nanga zinthu zinawayendela bwanji? Baibulo limati: “Iye anam’konda kwambili.”—Genesis 24:67; 26:8.

Ngakhale kuti Rabeka anakhalako zaka pafupifupi 3,900, n’zotheka kutengela citsanzo cake. Tingatengele kulimba mtima kwake, kugwila nchito kwake mwakhama, kuceleza alendo, ndi kudzicepetsa kwake. Tonsefe akulu ndi ana, amuna ndi akazi, a pabanja ndi amene sali pabanja, tingacite bwino kutsanzila cikhulupililo cake.

^ par. 10 Inali nthawi ya m’madzulo. Baibulo silionetsa utali wa nthawi imene Rabeka anakhala ku citsime. Silionetsanso kuti anthu a m’banja lake anali atagona pamene iye anamaliza nchitoyo, kapena kuti wina wa m’banja lake anamulondola cifukwa cocedwa kufika panyumba.

^ par. 15 Eliezere sanachulidwe dzina lake m’nkhani yonseyi, koma aoneka kuti ndiye mtumiki amene anatumidwa. Abulahamu anauza Eliezere kuti ndiye adzatenge coloŵa iye akadzafa. Conco, iye anali mtumiki wamkulu koposa komanso wodalilika wa Abulahamu. Umu ndi mmene mtumikiyu akufotokozedwela m’nkhani ino.—Genesis 15:2; 24: 2-4.