Onani zimene zilipo

Kodi Mavuto Adzathadi?

Kodi Mavuto Adzathadi?

Kodi mwayankha kuti . . .

  • inde?

  • iyai?

  • kaya?

ZIMENE BAIBO IMANENA

“Mulungu . . adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:3, 4, Baibulo la Dziko Latsopano.

UBWINO WOKHULUPILILA ZIMENEZI

Mudzavomeleza kuti si Mulungu amene amacititsa mavuto.—Yakobo 1:13.

Mudzasangalala kudziŵa kuti Mulungu amakhudzidwa tikakumana ndi mavuto.—Zekariya 2:8.

Mudzakhala ndi ciyembekezo cakuti mavuto onse adzatha.—Salimo 37:9-11.

KODI TINGAKHULUPILILEDI ZIMENE BAIBO IMANENA?

Inde, pa zifukwa ziŵili izi:

  • Mulungu amadana ndi mavuto ndi kupanda cilungamo. Ganizilani mmene Yehova Mulungu anamvelela pamene anthu ake akale anacitilidwa nkhanza. Baibo imakamba kuti iye anavutika mtima pamene adani ake anali ‘kukankha-kankha’ anthu ake.—Oweruza 2:18, Baibulo la Dziko Latsopano.

    Mulungu amadana kwambili ndi anthu amene amakonda kuvulaza anzao. Mwacitsanzo, Baibo imakamba kuti Mulungu amanyansidwa ndi “manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.”—Miyambo 6:16, 17.

  • Mulungu amadela nkhawa aliyense wa ife. Si munthu yekha amene amadziŵa “mlili wake ndi ululu wake,” koma Yehova nayenso amadziŵa zimenezo.—2 Mbiri 6:29, 30.

    Kupyolela mu Ufumu wake, Yehova posacedwapa adzacotsapo mavuto amene munthu aliyense ali nao. (Mateyu 6:9, 10) Koma pakali pano, iye amatonthoza anthu onse amene amam’funa-funa.—Machitidwe 17:27; 2 Akorinto 1:3, 4.

GANIZILANI FUNSO ILI

N’cifukwa ciani Mulungu amalola kuti tizivutika?

Baibo imayankha funso limeneli pa AROMA 5:12 ndi pa 2 PETULO 3:9.