Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

1

Kodi Nifuna Kukhala Munthu Wabwanji?

Kodi Nifuna Kukhala Munthu Wabwanji?

CIFUKWA CAKE UFUNIKA KUDZIŴA

Kudziŵa kuti ndiwe munthu wabwanji kudzakuthandiza kupanga zosankha zanzelu pamene ukumana na zovuta.

KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?

Yelekeza cocitika ici: Karen wangofika kumene ku phwando. Ndiyeno amvela liu lodziŵika kumbuyo kwake.

“Manje iwe wangoimilila cabe apo?”

Pamene Karen atembenuka aona kuti ni mnzake Jessica, na mabotolo aŵili kumanja otsegulilatu. Aona kuti ni moŵa. Jessica apatsila Karen botolo imodzi nomuuza kuti, “Iwe unakula manje, tiye tikondweleko pang’ono.”

Karen afuna kukana, koma Jessica ni mnzake. Ndipo Karen safuna kuoneka monga wogona, olo womvetsa ulesi. Maka-maka cifukwa Jessica ni mtsikana wabwino. Conco, Karen aganiza kuti ‘Ngati Jessica amamwa, ndiye kuti moŵa siwoipa. Ni moŵa cabe, si camba.’

Sembe iwe unali Karen, ukanacita ciani?

YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!

Kuti ucite cinthu canzelu pa nkhani monga iyi, uyenela kudziŵa kuti umafuna kukhala munthu wabwanji. Ukadziŵa zimenezi, udzakhala na mphamvu zolamulila umoyo wako, m’malo molola anzako kuyendetsa umoyo wako.—1 Akorinto 9:26, 27.

Nanga ungakhale nazo bwanji mphamvu zimenezo? Poyambila pabwino n’kuyankha mafunso otsatila:

1 NIMACITA BWINO M’MBALI ZITI?

Kudziŵa mbali zimene umacita bwino kudzakulitsa cidalilo cako.

CITSANZO CA M’BAIBO: Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati ndilibe luso la kulankhula, si kuti ndine wosadziŵanso zinthu.” (2 Akorinto 11:6) Cifukwa Paulo anali kudziŵa Malemba, anakhalabe wolimba pamene anthu anali kumutsutsa. Sanalole kuti zokamba zawo zimulefule.—2 Akorinto 10:10; 11:5.

UYENELA KUDZIFUFUZA. Pansi apa, lemba luso limene uli nalo.

Lomba fotokoza za khalidwe limodzi limene umacita bwino kwambili. (Monga, cifundo, kupatsa, kudalilika, kusunga nthawi, kapena khalidwe lina)

2 NANGA ZOFOOKA ZANGA NI ZITI?

Ngati ulola zofooka zako kulamulila umoyo wako, zikhoza kusintha umunthu wako wabwino.

CITSANZO CA M’BAIBO: Paulo anadziŵa bwino zofooka zake. Analemba kuti: “Mumtima mwanga ndimasangalala kwambili ndi cilamulo ca Mulungu, koma ndimaona cilamulo cina m’ziwalo zanga cikumenyana ndi cilamulo ca m’maganizo mwanga n’kundipanga kukhala kapolo wa cilamulo ca ucimo cimene cili m’ziwalo zanga.”—Aroma 7:22, 23.

UYENELA KUDZIFUFUZA. Ni zofooka ziti zimene uyenela kulamulila?

3 ZOLINGA ZANGA N’ZABWANJI?

Tifunse kuti: Kodi ungakwele motoka [taxi] na kuuza dilaiva kuti azingozunguluka malo amodzi mpaka mafuta asile? Kucita zimenezo kungakhale kupusa kwambili, komanso kuwononga ndalama.

Uphunzilapo ciani? Kuika zolinga kudzakuthandiza kuti usamangozunguluka mu umoyo popanda kopita. Umakhala na kopita ndipo umadziŵa bwino njila yokafikila kumeneko.

CITSANZO CA M’BAIBO: Paulo analemba kuti: “Sikuti ndikungothamanga osadziŵa kumene ndikuloŵela.” (1 Akorinto 9:26) Paulo sanali kungotsatila zocitika za mu umoyo. M’malo mwake, anali kudziikila zolinga na kuzikwanilitsa.—Afilipi 3: 12-14.

UYENELA KUDZIFUFUZA. Pansi apa, lemba zolinga zitatu zimene ungafune kuzikwanilitsa m’caka ca maŵa.

4 KODI UMAYENDELA MFUNDO ZITI?

Ukadziŵa bwino umunthu wako, umakhala monga mtengo wa mizu yolimba umene sungagwe olo kukhale cimphepo cabwanji

Ngati ulibe mfundo zimene umayendela, udzakhala munthu wopanda colinga. Udzakhala munthu wosintha-sintha monga bilimankhwe. Uzingotengela zocita za anzako—umboni wakuti sudziimila pawekha.

Koma ngati umacita zinthu motsatila mfundo zimene umakhulupilila, umakwanitsa kuima pawekha, mosasamala kanthu na zimene anzako amacita.

CITSANZO CA M’BAIBO: Pamene Danieli anali wacicepele, “anatsimikiza mumtima mwake” kuti azimvela malamulo a Mulungu, olo kuti makolo na abululu ŵake anali kutali kwambili. (Danieli 1:8) Mwa kucita izi, anakhulupilika pa mfundo zake. Conco, Danieli anali kutsatila mfundo zimene anali kukhulupilila.

UYENELA KUDZIFUFUZA. Umayendela mfundo ziti? Mwacitsanzo: Kodi umakhulupilila kuti Mulungu aliko? Ngati umakhulupilila, n’cifukwa ciani? Pali umboni wanji wokupangitsa kukhulupilla?

Kodi umakhulupilila kuti malangizo a Mulungu pa makhalidwe ni aphindu kwa iwe? N’cifukwa ciani?

Cothela tikufunse kuti, Kodi ungasankhe kukhala monga ciani? Tsamba lakugwa ku mtengo lotengeka-tengena na mphepo iliyonse, kapena monga mtengo wolimba umene sungagwe olo cimphepo ciwombe bwanji? Ukakhulupilika pa mfundo zako, udzakhala monga mtengo umenewo. Pamenepo, udzadziŵa kuti ndiwe munthu wabwanji.