Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

9

Kodi Niyenela Kukhulupilila za Cisanduliko—Evolution?

Kodi Niyenela Kukhulupilila za Cisanduliko—Evolution?

CIFUKWA CAKE UYENELA KUDZIŴA

Ngati ciphunzitso ca cisanduliko (evolution) n’coona, ndiye kuti moyo ulibe tanthauzo kweni-kweni. Koma ngati ciphunzitso cakuti zinthu zinacita kulengedwa ndiye coona, tikhoza kupeza mayankho okhutilitsa pa mafunso okhudza moyo na tsogolo lathu.

KUKHALA IWE UNGACITE BWANJI?

Ganizila cocitika ici: Alex wasokonezeka. Iye wakhala akukhulupilila mwa Mulungu, nakuti ndiye analenga zinthu. Koma lelo, atica ake a biology acita kukamba motsimikiza kuti za cisanduliko n’zoona, ndipo zili na maumboni otsimikizilidwa ndi akatswili a sayansi. Alex safuna kuoneka monga mbuli. Alingalila kuti, ‘Koma ngati asayansi apeza kuti za cisanduliko n’zoona, ndine ndani ine kuti niwatsutse?’

Kukhala Alex, kodi ukanavomeleza kuti za cisanduliko n’zoona, cabe cifukwa n’zimene mabuku a kusukulu amakamba?

YAMBA WAIMA NA KUGANIZA!

Kumbali zonse ziŵili, okhulupilila cisanduliko ndi okhulupilila za cilengedwe, ambili amangokhulupilila popanda zifukwa zeni-zeni.

  • Ena amakhulupilila za cilengedwe, cabe cifukwa n’zimene anaphunzila ku chechi.

  • Ena amakhulupilila za cisanduliko, cabe cifukwa n’zimene anawaphunzitsa kusukulu.

MAFUNSO 6 OFUNIKA KUYAGANIZILA

Baibo imakamba kuti: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheberi 3:4) Kodi n’zomveka, kapena iyayi?

Kukhulupilila kuti zamoyo sizinacite kulengedwa na Mlengi n’kosamveka. Kuli monga kukamba kuti nyumba iyi sinamangidwe na munthu aliyense, inadzimanga yekha

ZIMENE ENA AMAKAMBA: Ciliconse kumwamba na padziko lapansi cinabwelapo cifukwa ca kuphulika kwakukulubig bang.

1. Kodi n’ndani, kapena n’ciani cinacititsa kuphulika kumeneko?

2. Kodi zomveka ni ziti—zakuti zinthu zonse zinabwelapo zekha, kapena kuti pali wina amene anazipanga?

ZIMENE ENA AMAKAMBA: Anthu anacita kusandulika kucokela ku vinyama.

3. Ngati anthu anacita kusandulika kucokela ku vinyama—monga anyani—n’cifukwa ninji anthu ali na nzelu kwambili kuposa anyani?

4. N’cifukwa ciani ngakhale twamoyo tung’ono-ng’ono tuli na cipangidwe cocolowana kwambili?

ZIMENE ENA AMAKAMBA: Cisanduliko cili na umboni wotsimikizilika.

5. Kodi munthu amene akamba zimenezo anatsimikizila payekha za umboni umenewo?

6. Anthu ambili amakhulupilila za cisanduliko, cabe cifukwa anaphunzitsidwa kuti anthu onse anzelu amazikhulupilila, si conco?

“Julia anakamba kuti: “Ngati unali kuyenda mu sanga ndiye waona nyumba yabwino maningi, kodi ungaganize kuti: ‘Koma nyumba iyi ni yokongola! Ndiye kuti mitengo inagwa yokha, ndiyeno n’kuthyoka-thyoka na kujuŵika-juŵika yokha kukhala mapulanga. Kenako, n’kudzikhomelela-khomelela yokha na misomali, basi nyumba n’kupangika.’ Sungaganize conco, ndaŵa zimenezi n’zosamveka! Ndiye n’cifukwa ciani tingaganize kuti ni mmene zinthu zonse zinakhalilako?”

Gwen naye anati: “Tikambe kuti munthu wina akuuza kuti mu fakitale yopulintha mabuku mwacitika ngozi. Akuti cinacake caphulika, ndipo inki yamwazika-mwazika kuzipupa na kumalata nakupangika mau onse ali m’dikishonali yoposa makidishonale onse. Kodi ungakhulupilile zimenezo?”

N’CIFUKWA CIANI UYENELA KUKHULUPILILA MWA MULUNGU?

Baibo imalimbikitsa kuti ufunika kuseŵenzetsa ‘luso lako la kuganiza.’ (Aroma 12:1) Zimenezi zitanthauza kuti suyenela kukhulupilila Mulungu, cabe cifukwa ca:

  • MAGANIZO CABE (Basi nimangoona kuti payenela kukhala winawake wamphamvu kuposa ise ŵanthu)

  • KUTENGELA KWA ANTHU ENA (Nimakhala pakati pa anthu olambila Mulungu)

  • MAKOLO (Ni mmene makolo anga ananiphunzitsila—ndiwo ananisankhila)

M’malo mwake, ufunika kukhala na zifukwa zomveka kuposa zimenezi.

Teresa anafotokoza kuti: “Nikakhala m’kilasi ndipo atica akufotokoza mmene matupi athu amagwilila nchito, nimakhutila kuti zoona Mulungu aliko. Ciwalo ciliconse ca thupi yathu, olo kacepe bwanji, kana nchito yake. Ndipo nchito zambili zimenezi zimacitika ise osadziŵako ciliconse. Kukamba zoona, thupi ya munthu imagometsa maganizo!”

Nayenso Richard anakamba kuti: “Nikaona nyumba itali yosanja, sitima yapamadzi, kapena motoka, nimadzifunsa kuti, ‘Kodi anaipanga n’ndani?’ Pamafunika anthu anzelu kuti apange cinthu monga motoka. Zili conco cifukwa ngakhale tunsimbi twake tung’ono-tung’ono tufunika kuseŵenza bwino-bwino kuti motoka iziyenda bwino. Ndipo ngati motoka imafunika kukhala na woipanga, kuli bwanji ise ŵanthu!”

Anthony naye anati: “Pamene n’naphunzila zambili za sayansi, m’pamenenso n’naona kuti za cisanduliko zilibe maziko eni-eni. . . . N’naona kuti kukhulupilila za cisanduliko n’kovuta cifukwa zilibe umboni weni-weni, koma za Mlengi zili na maumboni otsimikizilika.”

GANIZILA IZI

Ngakhale kuti asayansi akhala akufufuza zinthu kwa zaka zambili-mbili, akalibe kugwilizana m’zonse pa ciphunzitso ca cisanduliko. Manje ganiza, ngati asayansi akangiwa kugwilizana pa ciphunzitso cawo ca cisanduliko—ndipo iwo ni akatswili—kodi ungalakwe kucikaikila ciphunzitso cimeneco?