Pitani ku nkhani yake

Mfundo Zachidule Zokhudza Baibulo

Mfundo Zachidule Zokhudza Baibulo

Kuyambira kale, Baibulo ndi buku lomwe lafalitsidwa padziko lonse kuposa buku lina lililonse ndipo anthu ambiri amalikonda. Koma mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi buku lotchukali limanena za chiyani?’

Kabuku kakuti Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani? kamafotokoza momveka bwino mfundo zachidule zokhudza Baibulo zomwe zingakuthandizeni kumvetsa mfundo yaikulu ya m’Baibulo. Kabukuka kakufotokoza mfundo zachidule zokhudza kulengedwa kwa zinthu kofotokozedwa m’buku la Genesis mpaka mfundo zosangalatsa zokhudza m’tsogolo zomwe zimapezeka m’buku la Chivumbulutso. M’kabukuka muli tchati chosonyeza nthawi imene zinthu zikuluzikulu zinachitika. Mulinso zithunzi zokongola komanso mafunso okuthandizani kuganiza mozama omwe mungakambirane ndi ena.

Werengani kabuku ka pa intaneti kakuti Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani?