Pitani ku nkhani yake

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Manja a Octopus Ndi Ogometsa Kwambiri

Manja a Octopus Ndi Ogometsa Kwambiri

 Akatswiri akufuna kupanga makina oti azithandiza madokotala akafuna kuchita munthu opaleshoni. Pogwiritsa ntchito makinawa, madokotala azidzatha kupanga opaleshoniyo pong’amba malo aang’ono kwambiri m’malo mong’amba malo aakulu. Makinawa adzakhala ndi tizipangizo tofewa, tomwe azidzatilowetsa pamalo omwe akufuna kupanga opaleshoniyo ndipo adzatipanga potengera mmene manja a octopus amagwirira ntchito.

 Taganizirani izi: Octopus ali ndi manja 8. Manjawa ndi ofewa kwambiri ndipo amatha kuwatambasula n’kugwira chinthu mwamphamvu kapenanso kuchifinya ngakhale chinthucho chitakhala pamalo opanikizika. Ngakhale manja ake ndi ofewa moti atha kupindikira kulikonse, octopus amathanso kulimbitsa tizigawo tosiyanasiyana ta dzanja lake, mogwirizana ndi mmene akufunira.

 Akatswiri ofufuza zinthu akuona kuti akhoza kutengera manja a nyamayi, popanga makina okhala ndi tizipangizo tofewa tokhala ngati manja, tomwe tingamathandize popanga maopaleshoni ovuta kwambiri. Ngati angakwanitse kupanga makinawa, madokotala sazidzavutika pothandiza odwala omwe akufunika opaleshoni yaikulu.

 Onerani kavidiyoka kuti muone mmene octopus amagwiritsira ntchito manja ake

 Panopa akatswiriwa apangapo kale makina okhala ndi tizipangizo togwira ntchito ngati manja a octopus ndipo akuwagwiritsa ntchito pa maopaleshoni ongoyeserera. Kadzanja kamodzi kakatali mamilimita 135, kakhoza kugwira kapena kunyamula kachiwalo kofewa ka m’thupi popanda kuyambitsa vuto lililonse. Ndipo kwinaku kadzanja kena kakhoza kumachita opaleshoni yomwe ikufunikayo. A Dr. Tommaso Ranzani, omwe ndi mmodzi wa akatswiri amene anapanga nawo makinawa ananena kuti: “Tikukhulupirira kuti tangoyambapo chabe, m’tsogolomu tikhala tikupanga makina ena otsogola kwambiri kuposa amenewa.”

Makina okhala ndi tizipangizo tofewa ngati manja a octopus, angakhale othandiza kwambiri popanga opaleshoni

 Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti octopus akhale ndi manja ogometsa chonchi? Kapena pali wina amene anawalenga?