Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Kanyama Kam’madzi Komwe Kamawala Pofuna Kudziteteza

Kanyama Kam’madzi Komwe Kamawala Pofuna Kudziteteza

P ALI kanyama kenakake kam’madzi kamene kamakonda kufufuza zakudya usiku. (Hawaiian Bobtail Squid) Kanyamaka kamawala osati n’cholinga choti kazioneka, koma pofuna kudziteteza. Kuwala kumene kamatulutsaku kukakumana ndi kuwala kwa mwezi ndi nyenyezi, zimapangitsa kuti kanyamaka kasinthe mtundu ndipo sikaoneka. Zimenezi zimatheka chifukwa cha mabakiteriya otulutsa kuwala omwe amakhala m’mimba mwa kanyamaka. Kugwirizana komwe kulipo pakati pa kanyamaka ndi mabakiteriyawa, kungatiphunzitse zambiri zomwe zingathandize kuti tikhale ndi thanzi labwino.

Taganizirani izi: Kanyamaka kamapezeka m’nyanja pafupi ndi zilumba za ku Hawaii. Kuwala kwa mwezi ndi nyenyezi kumapangitsa kuti kanyamaka kazionekera patali, ndipo izi zingapangitse kuti kagwidwe ndi nsomba komanso zinthu zina. Choncho kuti kadziteteze, kamatulutsa kuwala pamimba pake. Kuwalaku kumakhala kofanana ndi kuwala kwa mwezi ndi nyenyezi ndipo kumapangitsa kuti kanyamaka kasamaoneke. Zimene zimachitika n’zoti, mabakiteriya aja akamawala, amapangitsa kuti kanyamaka kazitulutsanso kuwala kwangati kwa mabakiteriyawo.

Mabakiteriyawa amathandizanso kuti kanyamaka kazigona komanso kudzuka pa nthawi yofanana. Akatswiri akuchita chidwi kwambiri ndi zimenezi chifukwa choti mabakiteriyawa amapezekanso m’thupi mwa anthu komanso nyama za m’gulu loyamwitsa. N’kutheka kuti mabakiteriya omwe amathandiza kugaya zakudya amathandizanso kuti thupi la anthu komanso nyama lizidziwa nthawi yogona ndi yodzuka. Koma mabakiteriyawa akasokonezedwa, zimabweretsa mavuto monga kunenepa kwambiri, kulephera kugona komanso matenda a nkhawa ndi a shuga. Choncho, akatswiri atafufuza bwino mgwirizano womwe uli pakati pa kanyamaka ndi mabakiteriya, angadziwe zambiri zomwe zingathandize kuti anthu azikhala ndi thanzi labwino.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti kanyamaka kaziwala pofuna kudziteteza, kapena pali winawake amene anakapanga?