Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Yesaya 40:31​—“Anthu Odalira Yehova Adzapezanso Mphamvu”

Yesaya 40:31​—“Anthu Odalira Yehova Adzapezanso Mphamvu”

 “Koma anthu odalira Yehova adzapezanso mphamvu. Iwo adzaulukira m’mwamba ngati ali ndi mapiko a chiwombankhanga. Adzathamanga koma osafooka. Adzayenda koma osatopa.”​—Yesaya 40:31, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.​—Yesaya 40:31, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Yesaya 40:31

 Yehova a Mulungu akutsimikizira anthu ake kuti adzawapatsa mphamvu zothetsera kapena kupirira vuto lililonse limene angakumane nalo.

 “Anthu Odalira Yehova Adzapezanso Mphamvu.”

Anthu amene amadalira, kapena kuti kukhulupirira kuti Mulungu amatha komanso akufunitsitsa kuthandiza anthu ake, sayenera kukayikira kuti iye adzawathandizadi. (Miyambo 3:5, 6) Njira imodzi imene Mulungu amathandizira anthu omulambira ndi kugwiritsa ntchito mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito.​—Luka 11:13.

 “Iwo adzaulukira m’mwamba ngati ali ndi mapiko a chiwombankhanga.” Mawu ophiphiritsawa akusonyeza mmene mphamvu ya Mulungu ingathandizire munthu. Chiwombankhanga chimadalira mpweya wotentha wopita m’mwamba kuti chiziuluka osakupiza mapiko ake. Chikapeza mpweyawo chimatambasula mapiko ake n’kumazungulirazungulira mkati mwake uku chikukwera m’mwamba. Chifukwa chopeza mpweya wotentha pafupipafupi chikamapita kumene chikufuna, chiwombankhanga chikhoza kuuluka kwa maola ambiri osagwiritsa ntchito mphamvu zake zambiri.

 “Adzathamanga koma osafooka.” Mavuto amene timakumana nawo angatifooketse komanso kutikhumudwitsa koma tingapirire ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu. Mphamvuzo zingatithandize kuchitabe zimene tiyenera kuchita ngakhale titakumana ndi mavuto aakulu. Mtumwi Paulo, yemwe anakumana ndi mavuto aakulu kwambiri, analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”​—Afilipi 4:13.

Nkhani yonse ya Yesaya 40:31

 Mulungu anachititsa kuti mneneri Yesaya alembe mawuwa m’zaka za m’ma 700 B.C.E. Lembali limanena za atumiki okhulupirika onse a Mulungu. Koma zikuoneka kuti Yehova ananena mawuwa kuti alimbikitse Ayuda omwe anadzatengedwa ku ukapolo ku Babulo kwa zaka 70. Pamene Ayuda ankabwerera kwawo kuchokera ku ukapolowo, anaona mawu a Mulunguwa akukwaniritsidwa. (Yesaya 40:1-3) Mulungu anawapatsa mphamvu kuti ayende ulendo wautali komanso wovuta b wochokera ku Babulo kupita ku Yerusalemu mu 537 B.C.E.​—Yesaya 40:29.

a Yehova ndi dzina la Mulungu.​—Salimo 83:18.

b Zikuoneka kuti njira imene Ayudawo anayenda inali yamtunda wa makilomita 1,600.