Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Mika 6:8—“Uziyenda Modzichepetsa Ndi Mulungu Wako”

Mika 6:8—“Uziyenda Modzichepetsa Ndi Mulungu Wako”

“Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino. Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.”—Mika 6:8, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.”—Mika 6:8, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Zimene Lemba la Mika 6:8 Limatanthauza

Mneneri Mika anafotokoza kuti kusangalatsa Yehova a Mulungu si kovuta kwambiri kwa anthufe. (1 Yohane 5:3) Vesili likufotokoza mfundo zitatu zofunika kwambiri zimene Mulungu amayembekezera kuti anthufe tizichita. Mfundo ziwiri zoyambirira zikufotokoza mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi anthu ena, pamene mfundo yachitatu ikukhudza ubwenzi umene tiyenera kukhala nawo ndi Mulungu.

“Uzichita chilungamo.” Mulungu amafuna kuti anthu amene amamulambira azichita zinthu mwachilungamo. Zimenezi zikutanthauza kuti tiziganiza ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mfundo za Mulungu zotithandiza kusiyanitsa chabwino ndi choipa. (Deuteronomo 32:4) Mwachitsanzo, anthu amene amatsatira mfundo za Mulungu amayesetsa kuchitira anthu onse zinthu moona mtima komanso mopanda tsankho, posatengera kumene akuchokera, mtundu wawo komanso kuti ndi olemera kapena osauka.—Levitiko 19:15; Yesaya 1:17; Aheberi 13:18.

“Ukhale wokoma mtima.” Palemba la Mika 6:8, mawu a Chiheberi akuti “ukhale wokoma mtima,” angamasuliridwenso kuti “uzikonda chikondi chokhulupirika.” Mu Chiheberi choyambirira mawu akuti “kukhulupirika” samangotanthauza kukhala wokhulupirika kwa anthu omwe timawakonda koma angatanthauzenso kuwachitira zinthu mokoma mtima komanso mwachifundo, kutanthauza kuti tiyenera kuwachitira zambiri. Mulungu amafuna kuti anthu omwe amafuna kumusangalatsa asamangosonyeza ena chifundo ndi kukoma mtima koma azikondanso makhalidwe amenewa. Zimenezi zikutanthauza kuti anthu amene amamulambira ayenera kumasangalala pothandiza ena, makamaka amene akufunikira kuthandizidwa. Kupatsa n’kumene kumatithandiza kukhala osangalala.—Machitidwe 20:35.

“Uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” M’Baibulo mawu akuti “kuyenda,” angatanthauze “kutsatira njira inayake yochitira zinthu.” Munthu amasonyeza kuti akuyenda ndi Mulungu akamachita zinthu zimene Mulungu amasangalala nazo. Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi Nowa. Iye “anayenda ndi Mulungu woona” chifukwa anali wolungama pamaso pa Mulungu ndipo “anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake.” (Genesis 6:9) Masiku ano anthufe ‘timayenda ndi Mulungu’ tikamachita zinthu mogwirizana ndi zimene tikuphunzira m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Kuti zimenezi zitheke, tifunika kukhala odzichepetsa n’kumakumbukira kuti patokha sitingakwanitse kuchita zinthu zonse, koma timadalira Mulungu kuti azitithandiza pa chilichonse.—Yohane 17:3; Machitidwe 17:28; Chivumbulutso 4:11.

Nkhani ya pa Mika 6:8

Mika anali mneneri wa ku Isiraeli kuyambira mu 777 mpaka 717 B.C.E. Pa nthawi imeneyo anthu ambiri ankakonda kupembedza mafano, kuchita zachinyengo ndiponso kupondereza anzawo. (Mika 1:7; 3:1-3, 9-11; 6:10-12) Aisiraeli ambiri ankanyalanyaza malamulo a Mulungu omwe anali m’Chilamulo chomwe Mulungu anapereka kudzera mwa Mose. Chilamulochi chinkatchedwa kuti Chilamulo cha Mose. Pa nthawi yofananayo anthu ambiri ankaganiza molakwika kuti Mulungu atha kuwakonda ngati akuchita miyambo inayake yokhudza chipembedzo kapenanso kungopereka nsembe.—Miyambo 21:3; Hoseya 6:6; Mika 6:6, 7.

Patapita zaka mahandiredi ambirimbiri Mika atanena mawu amenewa, Yesu ananenanso kuti Atate wake amasangalala ndi anthu omwe amasonyeza ena chikondi, chilungamo ndi chifundo, koma amadana ndi anthu amene amangodzionetsera kuti amalambira Mulungu. (Mateyu 9:13; 22:37-39; 23:23) Mawu a Yesuwa akutithandiza kudziwa zimene Mulungu amafuna kuti anthu amene amamulambira azichita masiku ano.

Onerani kavidiyoka kuti mukhale ndi chithunzi cha zomwe zili m’buku la Mika.

a Mu Chingelezi, dzina lakuti Yehova linamasuliridwa kuchokera ku zilembo 4 za Chiheberi zoimira dzina la Mulungu יהוה (YHWH). Zilembozi zimatchedwa kuti Tetragrammaton. Palembali, dzina limeneli analimasulira kuti “AMBUYE” mu Baibulo la New International Version. Kuti mudziwe zambiri zokhudza Yehova komanso chifukwa chake Mabaibulo ena sagwiritsa ntchito dzinali, onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?