Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Luka 1:37—“Chifukwa Zimene Mulungu Wanena Sizilephereka”

Luka 1:37—“Chifukwa Zimene Mulungu Wanena Sizilephereka”

 “Chifukwa zimene mulungu wanena sizilephereka.”—Luka 1:37, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Chifukwa kwa Mulungu palibe chosatheka.”—Luka 1:37, King James Version.

Tanthauzo la Luka 1:37

 Mulungu Wamphamvuyonse angathe kuchita zinthu zimene anthu amaona kuti n’zosatheka. Palibe chimene chingamulepheretse kukwaniritsa zimene wanena kapena kulonjeza.

 Mawu a chilankhulo choyambirira akuti “wanena” angatanthauze “mawu” kapena “zonena,” makamaka za Mulungu. Angatanthauzenso zotsatirapo za zinthu zimene Yehova a Mulungu wanena. Popeza kuti mawu onse amene Mulungu wanena amachitika, Lemba la Luka 1:37 lingatanthauziridwenso kuti: “Chifukwa zimene Mulungu walonjeza sizingalephereke” kapena “Kwa Mulungu, palibe chosatheka.” Matanthauzo onsewa akungonena za mfundo yoona imodzi yakuti: Palibe zimene Mulungu wanena kapena kulonjeza zimene sizingakwaniritsidwe chifukwa kwa iye, palibe chosatheka.—Yesaya 55:10, 11.

 Baibulo lonse lili ndi nkhani zambiri zokhudza zimene Mulungu analonjeza. Mwachitsanzo, kudzera mwa mngelo, Yehova analosera kuti Sara, mkazi wa Abulahamu adzatenga pakati ali wachikulire. Mulungu ananenanso kuti: “Kodi pali chosatheka ndi Yehova?” (Genesis 18:13, 14) Pambuyo poganizira mozama zinthu zimene Mulungu analenga, Yobu ananena kuti: “Palibe chilichonse chimene mukufuna kuchita chimene simungakwanitse.” (Yobu 42:2) Pa nthawi ina, otsatira a Yesu ankadzikayikira kuti sangakhale oyenera kupulumutsidwa ndi Mulungu koma Yesu anawakumbutsa kuti “zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.”—Mateyu 19:25, 26. b

Zimene Zili pa Luka 1:37

 Mngelo Gabirieli anauza namwali wa Chiyuda dzina lake Mariya mawu a pa Luka 1:37. Gabirieli anali atangouza mtsikanayu kuti adzabereka “Mwana wa Wamʼmwambamwamba” ndiponso kuti ‘adzamupatse dzina lakuti Yesu.’ Iye ndi amene adzakhale Mfumu ya Ufumu wa Mulungu womwe udzalamulire dzikolo mpaka muyaya.—Luka 1:26-33; Chivumbulutso 11:15.

 Mariya anadabwa kwambiri moti anafunsa kuti zimenezi zingatheke bwanji chifukwa anali wosakwatiwa komanso ‘asanagonepo ndi mwamuna.’ (Luka 1:34, 35) Gabirieli anamuyankha kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito mzimu woyera, womwe ndi mphamvu yake yogwira ntchito. Pa nthawiyi n’kuti Yesu ali kumwamba monga mwana wauzimu wa Mulungu. Ndiyeno Yehova anagwiritsa ntchito mzimu woyera posamutsa moyo wa Mwana wake kuchokera kumwamba n’kumuika m’mimba mwa Mariya. (Yohane 1:14; Afilipi 2:5-7) Choncho Maria anakhala woyembekezera modabwitsa. Pofuna kumuthandiza kuti azikhulupirira kwambiri mphamvu za Mulungu, mngelo anauza Mariya kuti wachibale wake Elizabeti nayenso sikale pamene anakhala woyembekezera “mu ukalamba wake.” Elizabeti ndi mwamuna wake Zekariya analibe mwana chifukwa chakuti Elizabeti anali wosabereka. (Luka 1:36) Mwana wawo anali Yohane M’batizi amene Yehova ananeneratu za utumiki wake.—Luka 1:10-16; 3:1-6.

 Kenako mngelo Gabirieli ananena mawu a pa Luka 1:37, mwina poganizira Mariya ndi Eilizabeti. Mawu omwewa amalimbikitsa atumiki a Yehova a masiku ano kuti zonse zimene analonjeza adzazikwaniritsa. Ndipo zimenezi zikuphatikizapo zimene analonjeza zoti adzachotsa maboma a anthu ndipo adzalowedwa m’malo ndi ulamuliro wa Mwana wake Yesu Khristu yemwe adzakhale Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba.​—Danieli 2:44; 7:13, 14.

 Onerani vidiyo yachiduleyi kuti muone zomwe zili m’buku la Luka.

a Yehova ndi dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Onani nkhani yapawebusaiti yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?