Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Aroma 12:2​—“Sandulikani mwa Kusintha Maganizo Anu”

Aroma 12:2​—“Sandulikani mwa Kusintha Maganizo Anu”

 “Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”​—Aroma 12:2, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino, koma musandulike mwa kukonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndikuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu​—chokondweretsa ndi changwiro.”​—Aroma 12:2, Chipangano Chatsopano Mu Chichewa Cha Lero.

Tanthauzo la Aroma 12:2

 Anthu amene amafuna kusangalatsa Mulungu samangofunika kupewa zinthu zoipa, koma amafunikanso kusintha makhalidwe awo. Mulungu sawakakamiza kuti asinthe, koma iwo amachita zimenezi chifukwa chakuti amamukonda ndipo amazindikira kuti iye ndi wokoma mtima ndiponso amafuna kuti zinthu zizitiyendera bwino.​—Yesaya 48:17.

 “Musamatengere nzeru za nthawi ino.” “Nzeru za nthawi ino,” zomwe ndi mfundo, makhalidwe komanso zochita za anthu am’dzikoli, sizigwirizana ndi mfundo kapena maganizo a a Mulungu. (1 Yohane 2:15-17) “Nzeru za nthawi ino” zimakhala kulikonse ndipo zimachititsa kuti anthu asinthe n’kuyamba kutengera makhalidwe a anzawo. Kuti munthu azilambira Mulungu movomerezeka, amayenera kupewa zochita za m’dzikoli. Akapanda kutero angayambe kukhala ndi makhalidwe oipa amene angamubweretsere mavuto komanso amene sasangalatsa Mulungu.​—Aefeso 2:1-3; 4:17-19.

 “Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” Munthu amafunikanso kuyesetsa kusintha mmene amaganizira komanso kumvera mumtima mwake. Tikhoza kuona kuti kusintha kumeneku ndi kwakukulu chifukwa mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti ‘kusandulika’ amanena za kusintha ngati kumene kumachitika kuti mbozi ikhale gulugufe. Anthu amene amalambira Mulungu amafunika kuvala “umunthu watsopano.”​—Aefeso 4:23, 24; Akolose 3:9, 10.

 “Muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.” Mulungu amafuna kuti anthu amene amamulambira azitsimikizira kuti zimene amakhulupirira n’zoona. Anthu amenewa amachita zimenezi akamaphunzira Mawu a Mulungu, kuwagwiritsa ntchito komanso akamaona ubwino wotsatira mfundo za Mulungu pa moyo wawo. Akamatero, amatsimikizira okha mumtima mwawo kuti njira za Mulungu ndi zabwino.​—Salimo 34:8.

Nkhani Yonse ya Aroma 12:2

 Chaputala 12 cha buku la Aroma, chimafotokoza zimene tiyenera kuchita kuti tizilambira Mulungu movomerezeka. Kulambira kumeneko kumakhudza mbali zonse za moyo wa munthu, ndipo kumafuna kuti munthu azigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza” m’malo momangokhulupirira zinthu m’chimbulimbuli kapena mongotengeka maganizo. (Aroma 12:1, 3) M’chaputalachi muli malangizo othandiza munthu kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo, okhudza mmene angamachitire zinthu ndi anthu ena komanso zimene angachite munthu wina akamulakwira.​—Aroma 12:9-21.