Pitani ku nkhani yake

Kodi Mariya Mmagadala Anali Ndani?

Kodi Mariya Mmagadala Anali Ndani?

Yankho la m’Baibulo

 Mariya Mmagadala anali wotsatira wokhulupirika wa Yesu Khristu. Dzina lake lakuti Mmagadala liyenera kuti linachokera ku dzina la mzinda wotchedwa Magadala (kapena mwina lakuti Magadani). Mzindawu unali pafupi ndi nyanja ya Galileya. N’kutheka kuti pa nthawi inayake, Mariya ankakhala mumzindawu.

 Mariya Mmagadala limodzi ndi azimayi ena angapo ankayenda ndi Yesu ndi ophunzira ake n’kumawathandiza kupeza zofunika pa moyo. (Luka 8:1-3) Iye anaona Yesu akuphedwa komanso anali pa gulu la anthu oyamba kumuona atangoukitsidwa.—Maliko 15:40; Yohane 20:11-18.

 Kodi Mariya Mmagadala anali hule?

 Baibulo silinena kuti Mariya Mmagadala anali hule. Zimene limanena zokhudza Mariya asanayambe kutsatira Yesu n’zakuti Yesuyo anamutulutsa ziwanda 7.—Luka 8:2.

 N’chifukwa chiyani anthu ena amaganiza kuti iye anali hule? Zaka mahandiredi angapo Mariya atamwalira, anthu ena ananena kuti iye anali munthu (yemwe ayenera kuti anali hule) amene dzina lake silinatchulidwe koma anasambitsa mapazi a Yesu ndi misozi yake n’kuwapukuta ndi tsitsi lake. (Luka 7:36-38) Koma palibe umboni uliwonse m’Baibulo woti munthuyo anali Mariya.

 Kodi Mariya Mmagadala anali “mtumwi wa atumwi”?

 Ayi. Tchalitchi cha Katolika chimatchula Mariya kuti “Mariya Mmagadala Woyera” komanso “mtumwi wa atumwi” chifukwa choti anali woyamba kuuza atumwi kuti Yesu anaukitsidwa. (Yohane 20:18) Koma mfundo imeneyi siitanthauza kuti Mariya anali mtumwi ndipo Baibulo silinena paliponse kuti iye anali mtumwi.—Luka 6:12-16.

 Baibulo linamaliza kulembedwa cha m’ma 98 C.E. Koma atsogoleri a matchalitchi sankamulemekeza kwambiri Mariya Mmagadala mpaka m’zaka za m’ma 500 C.E. Nkhani zina zimene zinalembedwa m’zaka za m’ma 100 ndi 200 C.E., zomwe sizinaphatikizidwe m’Baibulo, zimafotokoza kuti atumwi ena a Yesu ankachitira nsanje Mariya. Koma nkhani zimenezi ndi zabodza ndipo sizili m’Malemba.

 Kodi Mariya Mmagadala anali mkazi wa Yesu Khristu?

 Ayi. Baibulo limasonyeza kuti Yesu sanakwatire. a