Pitani ku nkhani yake

Kodi Ndingatani Kuti Ndizisankha Zochita Mwanzeru?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizisankha Zochita Mwanzeru?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo limatipatsa malangizo abwino omwe angatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru. Lingatithandize kuti ‘tipeze nzeru [komanso] luso lomvetsa zinthu.’ (Miyambo 4:5) Nthawi zina limatiuza zinthu zabwino zomwe tiyenera kusankha. Koma nthawi zina, limangotipatsa malangizo omwe angatithandize kuti tisankhe zinthu mwanzeru.

Zimene zili munkhaniyi

 Zomwe zingakuthandizeni kuti muzisankha zochita mwanzeru

  •   Musamapupulume posankha zochita. Baibulo limati: “Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” (Miyambo 14:15) Kusankha zinthu mopupuluma kungakuchititseni kuti mulephere kuganizira zinthu zofunika kwambiri. Muziganizira mofatsa musanasankhe zoyenera kuchita.​—1 Atesalonika 5:21.

  •   Musamasankhe zochita pongotengera mmene mukumvera mumtima. Baibulo limatichenjeza kuti tisamadalire kwambiri mtima wathu. (Miyambo 28:26; Yeremiya 17:9) Mwachitsanzo, zingakhale zovuta kuti tisankhe zochita mwanzeru ngati takwiya, tapanikizika maganizo, takhumudwa, tatopa kapenanso ngati tikufunitsitsa kwambiri chinthu chinachake.​—Miyambo 24:10; 29:22.

  •   Muzipemphera kuti Mulungu akupatseni nzeru. (Yakobo 1:5) Mulungu amasangalala kwambiri kuyankha mapemphero oterowo. Iye ndi Atate wachikondi ndipo amafunira ana ake zinthu zabwino. “Pakuti Yehova amapereka nzeru. Kudziwa zinthu ndi kuzindikira kumatuluka m’kamwa mwake.” a (Miyambo 2:6) Ndipo Yehova amatipatsa nzeru pogwiritsa ntchito Mawu ake omwe ndi Baibulo.​—2 Timoteyo 3:16, 17.

  •   Muzifufuza. Kuti musankhe zochita mwanzeru, muyenera kudziwa zolondola pa nkhani yomwe mukufuna kusankhayo. Ndipotu Baibulo limati: “Munthu wanzeru amamvetsera ndi kuphunzira malangizo owonjezereka.” (Miyambo 1:5) Kodi nzeru zothandiza ndi zodalirika tingazipeze kuti?

     Choyamba, muzifufuza kaye zomwe Baibulo limanena zokhudza nkhaniyo. Chifukwa choti Mlengi wathu amadziwa zinthu zomwe zingakhale zabwino kwa ife, anatipatsa Mawu ake momwe tingapezemo malangizo omwe angatithandize. (Salimo 25:12) Baibulo limatipatsa malangizo osapita m’mbali pa nkhani zina zomwe tikufuna kusankha. Nthawi zina malangizowa amaperekedwa ngati malamulo kapena mfundo zomwe tingayendere. (Yesaya 48:17, 18) Palinso nkhani zina zambiri zomwe Baibulo silifotokoza mwachindunji zomwe tingachite. Koma limakhala ndi mfundo zomwe zingatithandize kuti tisankhe zochita mwanzeru ngakhale kuti zomwe tingasankhezo zingakhale zosiyana ndi zomwe ena angasankhe. Kuti mupeze mavesi a nkhani yomwe mukufuna kudziwa, muzifufuza nkhanizi m’mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo ndipo mungapeze mabukuwa kwaulere pawebusaiti iyi. b

     Kuti mudziwe zoyenera kusankha pa nkhani zina, muyenera kufufuza ku malo kapena ku mabungwe odalirika. Mwachitsanzo, musanagule chinthu china chake makamaka chinthu chomwe ndi chofunika ndalama zambiri, muyenera kuwerenga bwino zomwe zinalembedwa pachinthucho ndi kudziwa bwino kampani yomwe inachipanga. Muyeneranso kudziwa bwino zomwe mungachite ngati chinthucho chitawonongeka kapenanso ngati mutafuna kuchibweza. Ndi bwinonso kutsimikizira ngati zomwe zalembedwa zokhudza chipangizocho, ndi zogwirizana ndi zomwe mukufuna.

     Baibulo limati: “Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima.” (Miyambo 15:22) Choncho musanasankhe zoti muchite, muzifunsa kaye anthu odalirika. Mwachitsanzo, musanasankhe zoti muchite pa thandizo la kuchipatala, mungachite bwino kufunsa kaye adokotala kuti akuuzeni mmene chithandizo chimene mukufunacho chimagwirira ntchito. (Mateyu 9:12) Nthawi zina mungachitenso bwino kufunsa anthu ena omwe anakumanapo ndi vuto ngati lanulo. Komabe, ndi bwino kukumbukira kuti inuyo (osati anthu amene mukuwafunsawo) ndi amene muyenera kusankha zoti muchite. Muyeneranso kukumbukira inuyo ndi amene mudzakumane ndi zotsatira za zimene mungasankhezo.​—Agalatiya 6:4, 5.

  •   Muziganizira bwino mbali zonse za nkhaniyo. Pa zomwe mwafufuzazo, lembani zomwe inuyo mungakonde. Lembaninso ubwino ndi kuipa kwa njira iliyonse imene mungasankhe. Muyeneranso kuganizira zimene zingachitike chifukwa cha zimene mwasankhazo. (Deuteronomo 32:29) Mwachitsanzo muyenera kuganizira mmene zimene mwasankhazo zingakukhudzireni komanso mmene zingakhudzire banja lanu ndi anthu ena. (Miyambo 22:3; Aroma 14:19) Ngati mutaganizira zimenezi mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo mukhoza kusankha zochita mwanzeru.

  •   Sankhani zoti muchite. Nthawi zina tikhoza kuzengereza kusankha zoti tichite chifukwa chokayikira. Koma kulephera kusankha zoti tichite kukhoza kutitayitsa mwayi kapena kutilowetsa m’mavuto ena. M’mawu ena tinganene kuti, kulephera kusankha zoti tichite, n’chimodzimodzi kusankha zinthu mopanda nzeru. Mwambi wina wa m’Baibulo wogwirizana ndi ntchito yaulimi umati: “Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.”​—Mlaliki 11:4, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

 Muzikumbukiranso kuti ngakhale mutasankha bwino zochita, pakhozabe kukhala zovuta zina. Ndipotu kawirikawiri, kuti zomwe tasankhazo zitheke, timafunika kuluza zinthu zina. Tikhozanso kukumana ndi zinthu zadzidzidzi. (Mlaliki 9:11) Choncho gwiritsa ntchito mfundo zomwe mwapeza kenako sankhani njira yomwe ingakuthandizeni kuti zomwe mwasankhazo zitheke.

 Kodi ndisinthe zomwe ndinasankha kale?

 Zinthu zina zomwe tinasankha zingafunike kuzisintha. Nthawi zina zinthu zikhoza kusintha pa moyo wathu kapena tikhoza kuona kuti zomwe tinasankha poyamba sizinayende mmene timayembekezera. Ngati ndi choncho, ndi bwino kuonanso bwino zomwe tinasankhazo kenako n’kusankhanso njira ina yomwe ingatithandize kupeza zomwe tikufuna.

 Komabe, pali zinthu zina zomwe tinasankha zomwe sitiyenera kuzisintha. (Salimo 15:4) Mwachitsanzo, Mulungu amafuna kuti anthu okwatirana azisungabe zomwe analonjezana. c (Malaki 2:16; Mateyu 19:6) Ngati m’banja muli mavuto, ndi bwino kuyesetsa kuthana ndi mavutowo m’malo mothetsa banjalo.

 Bwanji ngati ndinasankha molakwika ndipo sindingathenso kuzisintha?

 Tonsefe nthawi zina timasankha zinthu molakwika kapena mosaganiza bwino. (Yakobo 3:2) Zimenezi zikachitika tikhoza kukhumudwa kapenanso kudziimba mlandu ndipo palibe vuto ngati tikumva choncho. (Salimo 69:5) Dziwani kuti nthawi zina kukhumudwa chifukwa chosankha zinthu molakwika kungatithandize kuti tisadzabwerezenso zomwe tinalakwitsazo. (Miyambo 14:9) Komabe, Baibulo limatilimbikitsa kuti tisamakhumudwe mopitirira malire chifukwa zikhoza kutisokoneza kwambiri maganizo. (2 Akorinto 2:7) Baibulo limati:  d “Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo.” (Salimo 103:8-13) Choncho ndi bwino kuphunzirapo kanthu pa zomwe tinalakwitsa ngakhale kuti sitingathe kuzisintha. Kenako tiziyesetsa kuchita zomwe tingathe kuti zinthu ziyambenso kuyenda bwino.

a Yehova ndi dzina la Mulungu lopezeka m’Baibulo.​—Salimo 83:18.

b Mungathenso kufufuza pa jw.org polemba mawu ofanana ndi zomwe mukufuna kusankhazo. Pawebusaitiyi pamapezeka malangizo a m’Malemba pa nkhani zosiyanasiyana. Kuwonjezera pamenepa, mungathenso kufufuza mu “Kalozera wa Mawu a m’Baibulo” mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika.

c Ndi cholinga cha Mulungu kuti anthu okwatirana azikhala limodzi kwa ndi moyo wawo wonse. Iye amalola anthu okwatirana kuthetsa banja lawo ndi kukwatirananso ndi munthu wina pokhapokha ngati wina wachita chigololo. (Mateyu 19:9) Ngati mukulimbana ndi mavuto am’banja, Baibulo lingakuthandizeni kuthana ndi mavutowo mwanzeru komanso mwachikondi.

d Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti: “Kodi Baibulo Lingandithandize Kuti Ndisiye Kudziimba Mlandu?