Pitani ku nkhani yake

Kodi Akatswiri a Maphunziro Amakhulupirira Kuti Yesu Anakhalapodi?

Kodi Akatswiri a Maphunziro Amakhulupirira Kuti Yesu Anakhalapodi?

 Akatswiri a maphunziro ali ndi zifukwa zomveka zimene zimawachititsa kukhulupirira kuti Yesu anakhalapodi. Pofotokoza zimene ananena akatswiri a mbiri yakale a m’nthawi ya atumwi komanso a m’zaka za m’ma 100 C.E., zokhudza Yesu ndiponso Akhristu oyambirira, buku lina limene linatuluka mu 2002 linati: “Nkhani zimene akatswiri osiyanasiyana analemba zikusonyeza kuti kalelo, ngakhale anthu amene ankatsutsa Chikhristu sankakayikira zoti Yesu anakhalapodi. Koma chakumapeto kwa zaka za m’ma 1700 mpaka m’ma 1800 ndiponso chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, anthu ena anayamba kukayikira zoti Yesu anakhalapodi ngakhale kuti anthuwo analibe umboni womveka.”—Encyclopædia Britannica.

 Mu 2006, buku linanso lonena za Yesu linati: “Masiku ano, palibe katswiri aliyense wodziwika bwino amene angatsutse zoti Myuda wina dzina lake Yesu, mwana wa Yosefe, anakhalapodi. Koma akatswiri ambiri amanena kuti panopa anthu akudziwa zambiri zokhudza zinthu zimene Yesu anachita komanso zimene ankaphunzitsa.”—Jesus and Archaeology.

 Baibulo limasonyeza kuti Yesu anali munthu weniweni. M’Baibulo muli mayina a makolo ake komanso achibale ake. (Mateyu 1:1; 13:55) Limatiuzanso mayina a olamulira otchuka amene anakhalapo pa nthawi yofanana ndi Yesu. (Luka 3:1, 2) Zimenezi zimathandiza akatswiri ofufuza kuti atsimikizire kuti nkhani za m’Baibulo n’zolondola.