Pitani ku nkhani yake

Kodi Mawu Oti Puligatoliyo Amapezeka M’Baibulo?

Kodi Mawu Oti Puligatoliyo Amapezeka M’Baibulo?

Zimene Baibulo limanena

 Ayi. M’Baibulo simupezeka mawu akuti “puligatoliyo,” ndipo siliphunzitsa kuti mizimu ya anthu amene amwalira imakayeretsedwa ku puligatoliyo. a Taonani zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza uchimo ndi imfa zomwe ndi zotsutsana ndi chiphunzitso cha puligatoliyo.

  •   Kukhulupirira magazi a Yesu ndi kumene kumayeretsa munthu ku uchimo, osati kupita ku puligatoliyo. Baibulo limanena kuti “magazi a Yesu Mwana [wa Mulungu] akutiyeretsa ku uchimo wonse” komanso limati “Yesu Khristu . . . anatimasula ku machimo athu ndi magazi ake.” (1 Yohane 1:7; Chivumbulutso 1:5) Yesu anapereka “moyo wake dipo la anthu ambiri” kuti awawombole ku uchimo.—Mateyu 20:28, Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu.

  •   Anthu amene amwalira sadziwa chilichonse. “Pakuti amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Munthu amene wamwalira sangamve china chilichonse, choncho sizingatheke kuti ayeretsedwe ndi moto wa ku puligatoliyo.

  •   Munthu samalangidwa chifukwa cha machimo pambuyo poti wamwalira. Baibulo limanena kuti “malipiro a uchimo ndi imfa” komanso limati “munthu amene wafa wamasuka ku uchimo wake.” (Aroma 6:7, 23) Choncho, imfa ndi chilango chokwanira cha uchimo.

a Ponena za puligatoliyo, buku lina linati, “m’Mauthenga Abwino mulibe mawu amenewa.” (Orpheus: A General History of Religions) Buku linanso limati: “Tinganene kuti chiphunzitso cha Chikatolika cha puligatoliyo ndi chochokera ku miyambo, osati Malemba Oyera.”—New Catholic Encyclopedia Buku Lachiwiri, Volume 11, tsamba 825.

b Onani buku lakuti New Catholic Encyclopedia, Second Edition, Volume 11, tsamba 824.