Pitani ku nkhani yake

Kodi Mdyerekezi Amakhala Kuti?

Kodi Mdyerekezi Amakhala Kuti?

Yankho la m’Baibulo

 Mdyerekezi amakhala kumalo osaoneka chifukwa ndi cholengedwa chauzimu. Koma sikuti malo amenewa ndi ku Gehena woyaka moto kumene anthu ena amati anthu oipa amakazunzikako ngati mmene chithunzi cha m’nkhaniyi chikusonyezera.

“Nkhondo kumwamba”

 Nthawi ina Satana ankatha kuyendayenda kumwamba komanso kupita kumene kunali Mulungu ndi angelo okhulupirika. (Yobu 1:6) Koma Baibulo linalosera kuti kudzakhala “nkhondo kumwamba.” Nkhondo imeneyi inachititsa kuti Satana adzachotsedweko “n’kuponyedwa kudziko lapansi.” (Chivumbulutso 12:7-9) Nkhani zimene zinalembedwa m’Baibulo komanso zinthu zimene zikuchitika padzikoli zikusonyeza kuti nkhondo imeneyi inachitika kale. Mdyerekezi panopa ali padziko lapansili.

 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti pali malo enieni padziko lapansi pano kumene kumakhala Mdyerekezi? Mwachitsanzo mzinda wakale wa Pegamo unatchulidwa kuti ndi malo “kumene kuli mpando wachifumu wa Satana” komanso ‘n’kumene Satana akukhala.’ (Chivumbulutso 2:13) Mawu amenewa akungotanthauza kuti anthu ambiri mumzindawu ankakonda kulambira Satana. Baibulo limanena kuti Mdyerekezi amalamulira “maufumu onse a padziko lapansi,” choncho sakhala malo amodzi padzikoli koma ali padziko lapansi.—Luka 4:5, 6.