Pitani ku nkhani yake

Kodi Lamulo Lakuti “Diso Kulipira Diso” Limatanthauza Chiyani?

Kodi Lamulo Lakuti “Diso Kulipira Diso” Limatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Lamulo lakuti “diso kulipira diso” linkapezeka m’Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose. Pa ulaliki wa paphiri, Yesu anatchulanso za lamulo limeneli. (Mateyu 5:38, Ekisodo 21:24, 25; Deuteronomo 19:21) Cholinga cha lamuloli chinali chakuti munthu akapalamula, azipatsidwa chilango chogwirizana ndi zimene walakwa. a

 Lamuloli linkagwira ntchito munthu akavulaza mnzake mwadala. Zimenezi zikachitika, Chilamulo cha Mose chinkanena kuti: “Kuthyola fupa kulipira kuthyola fupa, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino. Mmene wapundulira mnzake nayenso muzim’pundula chimodzimodzi.”​—Levitiko 24:20.

 Kodi cholinga cha lamulo lakuti “diso kulipira diso” chinali chiyani?

 Lamulo lakuti “diso kulipira diso” silinkapereka ufulu woti anthu azibwezera wina akawalakwira. Koma linkathandiza oweruza kuti azipereka chilango choyenera, osati chokhwima kwambiri kapenanso chopepuka kwambiri.

 Lamuloli linali ngati chenjezo kwa aliyense amene ankafuna kuvulaza mnzake mwadala kapena kukonza chiwembu choterocho. Chilamulo chinkanena kuti: ‘Chotero ena onse [omwe aona lamulo la Mulungu la chilungamoli likugwiritsidwa ntchito] adzachita mantha, ndipo sadzachitanso choipa chilichonse ngati chimenechi pakati panu.’​—Deuteronomo 19:20.

 Kodi Akhristu ayenera kugwiritsa ntchito lamulo lakuti “diso kulipira diso?”

 Ayi. Lamuloli silikhudza Akhristu. Nthawi imeneyo lamuloli linali mbali ya Chilamulo cha Mose ndipo linasiya kugwira ntchito Yesu atapereka moyo wake ngati nsembe.​—Aroma 10:4.

 Komabe, lamuloli limatithandiza kudziwa mmene Mulungu amaonera zinthu. Mwachitsanzo, limatithandiza kudziwa kuti Mulungu amaona kuti chilungamo ndi chofunika kwambiri. (Salimo 89:14) Limatithandizanso kudziwa kuti amafuna kuti anthu ochita zoipa azilangidwa “pa mlingo woyenera.”​—Yeremiya 30:11.

 Maganizo olakwika okhudza lamulo lakuti “diso kulipira diso”

 Maganizo olakwika: Lamulo lakuti “diso kulipira diso” linali la nkhanza kwambiri.

 Zoona zake: Lamuloli silinkapereka ufulu woti anthu azichitirana nkhanza komanso kuti oweruza azipereka chilango chokhwima kwambiri. Oweruza asanapereke chilangochi, ankafunika kufufuza kaye ndi kudziwa bwino zonse zomwe zinachitika komanso kupeza umboni wotsimikizira ngati munthuyo analakwadi mwadala. (Ekisodo 21:28-30; Numeri 35:22-25) Choncho tinganene kuti lamulo lakuti “diso kulipira diso,” linkathandiza kuti oweruza asamapereke chilango chokhwima kwambiri.

 Maganizo olakwika: Lamulo lakuti “diso kulipira diso” linkachititsa kuti anthu azingokhalira kubwezerana.

 Zoona zake: Chilamulo cha Mose chinkanena kuti: “Usabwezere choipa kapena kusungira chakukhosi anthu amtundu wako.” (Levitiko 19:18) M’malo mopatsa anthu mphamvu kuti azibwezerana, Chilamulochi chinkawalimbikitsa kuti azisiya nkhani yonse m’manja mwa Mulungu komanso kulemekeza dongosolo lomwe Mulunguyo anaika pofuna kukhazikitsa mtendere.​—Deuteronomo 32:35.

a Nthawi zambiri mfundo ya lamuloli yomwe inkadziwika ndi mawu Achilatini akuti lex talionis, inkapezekanso m’malamulo a m’mayiko ambiri.