Pitani ku nkhani yake

Kodi ndi Mayina a Anthu Otani Amene Amalembedwa “M’buku la Moyo”?

Kodi ndi Mayina a Anthu Otani Amene Amalembedwa “M’buku la Moyo”?

Yankho la m’Baibulo

 “M’buku la moyo,” limene limatchedwanso kuti “mpukutu wa moyo,” kapena “buku la chikumbutso,” mumakhala mayina a anthu amene ali oyenera kudzalandira mphatso ya moyo wosatha. (Chivumbulutso 3:5; 20:12; Malaki 3:16) Mulungu amalemba mayina a anthu okhawo amene amamumvera mokhulupirika.—Yohane 3:16; 1 Yohane 5:3.

 Mulungu wakhala akukumbukira atumiki ake okhulupirika kuyambira “kukhazikitsidwa kwa dziko.” (Chivumbulutso 17:8) Iye amawakumbukira kwambiri ngati kuti mayina awo analembedwa m’buku. Munthu wokhulupirika woyamba amene dzina lake linalembedwa m’bulu la moyo anali Abele. (Aheberi 11:4) Zimene Yehova amachita pokumbukira atumiki ake okhulupirika ndi umboni wakuti iye ndi Mulungu wachikondi amene “amadziwa anthu ake.”—2 Timoteyo 2:19; 1 Yohane 4:8.

Kodi mayina amene analembedwa m’buku la moyo angafufutidwe?

 Inde. Ponena za anthu a mtundu wakale wa Aisiraeli amene sanamumvere, Mulungu ananena kuti: “Amene wandichimwirayo ndi amene ndim’fafanize m’buku langa.” (Ekisodo 32:33) Koma tikakhalabe okhulupirika, dzina lathu silidzafufutika mu “mpukutu wa moyo.”—Chivumbulutso 20:12.