Pitani ku nkhani yake

Kodi “Anzeru a Kum’mawa” Anali Ndani? Kodi Mulungu Ndi Amene Anawachititsa Kuti Alondole Nyenyezi ya ku Betelehemu?

Kodi “Anzeru a Kum’mawa” Anali Ndani? Kodi Mulungu Ndi Amene Anawachititsa Kuti Alondole Nyenyezi ya ku Betelehemu?

Yankho la m’Baibulo

 Mosiyana ndi miyambo yambiri yomwe imachitika pa nyengo ya Khirisimasi, Baibulo siligwiritsa ntchito mawu akuti “anzeru akum’mawa” kapena “mafumu atatu” pofotokoza za anthu omwe anapita kukaona Yesu atabadwa. (Mateyu 2:1) M’malomwake, Mateyu wolemba Uthenga Wabwino anagwiritsa ntchito mawu Achigiriki akuti ma’goi pofotokoza za amuna omwe anapita kukaona Yesu. Mawu akuti ma’goi ayenera kuti amanena za akatswiri okhulupirira nyenyezi komanso zinthu zina zokhudzana ndi zamatsenga. a Pomasulira za anthu amenewa, Mabaibulo ambiri amawatchula kuti ndi “okhulupirira nyenyezi” kapena “amagi.” b

 Kodi “anzeru akum’mawa” analipo angati?

 Baibulo silimanena kuti anthuwo analipo angati, koma anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhaniyi. Buku la Encyclopedia Britannica limanena kuti: “Anthu a kum’mawa amanena kuti okhulupirira nyenyeziwo analipo 12, pamene anthu akumadzulo amanena kuti anthuwo analipo atatu, potengera mphatso zitatu zimene anapereka kwa mwanayo,” zomwe ndi ‘golide, lubani, komanso mule.’—Mateyu 2:11.

 Kodi “anzeru akum’mawa” anali mafumu?

 Ngakhale kuti pamwambo wa Khirisimasi pamakhala zithunzi zosonyeza kuti alendowo anali mafumu, Baibulo silinena zimenezo. Buku la Encyclopedia Britannica limanena kuti patadutsa zaka kuchokera pamene Yesu anabadwa, anthu “anawonjezera mfundo zina” zokhudza kubadwa kwake komanso anayamba kunena kuti alendowo anali mafumu.

 Kodi mayina a “anzeru akum’mawa” anali ndani?

 Baibulo silimatchula mayina a okhulupirira nyenyeziwa. Koma buku lina limanena kuti, “Nkhani zina zongopeka zimapereka mayina osiyanasiyana a anthuwa. Mwachitsanzo, ena amati mayina awo anali Gaspar, Melchior, ndi Balthasar.”—The International Standard Bible Encyclopedia.

 Kodi “anzeru akum’mawa” anapita liti kukaona Yesu?

 N’kutheka kuti okhulupirira nyenyeziwa anapita kukamuona patatha miyezi ingapo kuchokera pomwe iye anabadwa. Tikutero chifukwa Mfumu Herode yemwe ankafuna kuti Yesu aphedwe, analamula kuti ana aamuna azaka ziwiri kutsika m’munsi aphedwe. Iye anatchula zaka zimenezi potengera zomwe okhulupirira nyenyezi anamuuza zokhudza nthawi imene Yesu anabadwa.—Mateyu 2:16.

 Okhulupirira nyenyeziwa sanapite kukamuona Yesu usiku umene anabadwa. Baibulo limanena kuti: “Atalowa m’nyumbamo, anaona mwanayo ndi mayi ake Mariya.” (Mateyu 2:11) Zimenezi zikusonyeza kuti panthawiyi banjali linkakhala m’nyumba osati modyeramo ziweto ndipo Yesu sanalinso wakhanda.—Luka 2:16.

 Kodi Mulungu ndi amene anatsogolera “anzeru akum’mawa” kuti alondole “nyenyezi” ya ku Betelehemu?

 Anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu ndi amene anatumiza nyenyezi ya ku Betelehemu kuti itsogolere okhulupirira nyenyeziwo kumene kunali Yesu. Taganizirani mfundo zotsatirazi zomwe zikusonyeza kuti zimenezi sizingakhale zoona.

  •   Poyambirira nyenyeziyo ndi imene inatsogolera okhulupirira nyenyeziwo ku Yerusalemu. Baibulo limanena kuti: “Okhulupirira nyenyezi ochokera kumadera a kum’mawa anabwera ku Yerusalemu. Iwo ananena kuti: ‘Ili kuti mfumu ya Ayuda imene yabadwa? Chifukwa pamene tinali kum’mawa, tinaona nyenyezi yake ndipo tabwera kudzaigwadira.’”—Mateyu 2:1, 2.

  •   Mfumu Herode ndi amene anali woyamba kuwalozera okhulupirira nyenyeziwo ku Betelehemu. Atamva zimene “mfumu ya Ayuda” idzachite, Herode anafufuza kumene Khristu adzabadwire. (Mateyu 2: 2-6) Atadziwa kuti ndi ku Betelehemu, anauza okhulupirira nyenyezi kuti apite akafufuze kumene mwanayo ali, ndipo akakamupeza adzamudziwitse.

 Pa nthawiyi ndi pamene okhulupirira nyenyeziwo ananyamuka kupita ku Betelehemu. Baibulo limanena kuti: “Atamva zimene mfumu inanena, anapitiriza ulendo wawo. Kenako nyenyezi imene anaiona ali kum’mawa ija inawatsogolera, mpaka inakaima m’mwamba pamalo pamene panali mwanayo.”—Mateyu 2:9.

  •   Anthu atangoona nyenyezi zinthu zinasintha ndipo zinachititsa kuti Moyo wa Yesu ukhale pangozi komanso ana ambiri osalakwa anaphedwa. Okhulupirira nyenyeziwo atangochoka ku Betelehemu, Mulungu anawachenjeza kuti asadutsenso kwa Herode.—Mateyu 2:12.

 Kodi Herode anatani ataona kuti anthu aja sanadutsenso kwa iyeyo? Baibulo limanena kuti: “Herode, poona kuti okhulupirira nyenyezi aja am’pusitsa, anakwiya koopsa. Choncho anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna m’Betelehemu ndi m’zigawo zake zonse, kuyambira azaka ziwiri kutsika m’munsi, mogwirizana ndi nthawi imene anafunsira mosamala kwa okhulupirira nyenyezi aja.” (Mateyu 2:16) Kunena zoona Mulungu sakanachititsa kuti zinthu zoipazi zichitike.—Yobu 34:10.

a Katswiri wina wachigiriki wolemba mbiri yakale dzina lake Herodotus, yemwe anakhalako cha m’ma 400 B.C.E. analemba kuti a ma’goi anali m’gulu la a Amedi ndi Aperisiya omwe anali akatswiri pa nkhani yokhulupirira nyenyezi komanso kumasulira maloto.

b Onani New American Standard Bible, The New American Bible, New English Bible, ndi New International Version Bible Study. Baibulo la King James Version limatchula alendowa kuti “anzeru akum’mawa,” koma silimanena kuti analipo atatu.