Pitani ku nkhani yake

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

Anapirira Mpaka Pamapeto

Anapirira Mpaka Pamapeto

Eliya anamva zoti Mfumu Ahabu yamwalira. Mwina m’maganizo anu mukuona mneneriyu atagwira chibwano chake kuganizira mmene zinthu zinalili zaka zambiri m’mbuyomo akulimbana ndi mfumu ya nkhanzayo. Panthawiyo mfumu Ahabu ndi mkazi wake Yezebeli ankaopseza komanso kusakasaka Eliya kuti amuphe. Tingatero kuti mneneriyu anapirira zambiri. Mfumukazi Yezebeli italamula kuti aneneri ambiri a Yehova aphedwe, Ahabu sanachitepo chilichonse pofuna kuletsa maganizo a mkazi wakeyo. Komanso Ahabu ndi mkazi wakeyu anakonza chiwembu chofuna kupha Naboti ndi ana ake aamuna. Naboti sanalakwe chilichonse ndipo mfumuyo inakonza chiwembuchi chifukwa cha dyera basi. Eliya anapereka uthenga wachiweruzo wochokera kwa Yehova wodzudzula Ahabu ndi anthu a m’banja lake chifukwa chokonza chiwembuchi. Tsopano mawu a Mulungu anali atayamba kukwaniritsidwa. Ahabu anafa mogwirizana ndi zomwe Yehova anali atanena.​—1 Mafumu 18:4; 21:​1-​26; 22:37, 38; 2 Mafumu 9:​26.

Komabe ngakhale zinali choncho, Eliya anadziwa kuti ankafunikabe kupirira chifukwa Yezebeli anali adakali moyo. Mfumukaziyi inapitirizabe kuchitira nkhanza achibale ake komanso nzika za mu ufumuwo. N’zachidziwikire kuti Eliya ankayembekezera kukumana ndi mavuto ambiri. Komanso anali adakali ndi zambiri zoti aphunzitse Elisa yemwe anali mnzake komanso woti adzalowe m’malo mwake. Ndiye tiyeni tsopano tikambirane ntchito zitatu zomwe Eliya ankafunika kugwira. Tikamakambirana nkhaniyi tiona mmene chikhulupiriro chake chinamuthandizira kuti akhale wopirira. Tionanso zomwe ifeyo tingachite kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu makamaka m’masiku ovuta ano.

Kupereka Chiweruzo kwa Ahaziya

Ahaziya anali mwana wamwamuna wa Ahabu ndi Yezebeli. Tsopano Ahaziya anakhala mfumu ya Isiraeli. Koma m’malo mophunzirapo kanthu pa zomwe zinachitikira makolo ake, anatengera mtima wawo woipa. (1 Mafumu 22:52) Nayenso ankalambira Baala ngati mmene ankachitira makolo ake. Anthu amene ankapembedza Baala ankachita makhalidwe oipa monga kuchita uhule pamalo awo opembedzera komanso kupereka nsembe ana. Kodi pali chilichonse chomwe chikanachitika kuti mfumuyi isinthe maganizo ake komanso kuthandiza anthu ake kusiya kuchita zonyansa pamaso pa Yehova?

Mwadzidzidzi mfumu yodzikuzayi inakumana ndi tsoka. Mfumuyi inagwa m’chipinda chake cham’mwamba ndipo inavulala kwambiri. Ngakhale kuti moyo wake unali pangozi, Ahaziya sanafune kupempha thandizo kwa Yehova. Koma m’malo mwake anatumiza anthu kumzinda kwa Ekironi kuti akafunsire kwa mulungu wonyenga Baala-zebubu kuti adziwe ngati angachire. Ekironi unali mzinda wa Afilisiti omwe anali adani a anthu a Mulungu. Yehova anakwiya kwambiri ndi zimene Ahaziya anachita ndipo anatumiza mngelo kwa Eliya kuti akasokoneze anthu omwe anatumidwa ku Ekironi aja. Eliya anabweza anthuwo kwa Ahaziya ndipo anapatsa anthuwo uthenga woopsa woti akauze Ahaziya. Mfumuyi inachita tchimo lalikulu chifukwa inkachita zinthu ngati kuti ku Isiraeli kulibe Mulungu. Yehova anatsimikiza kuti Ahaziya sachira.​—2 Mafumu 1​:2-4.

Ahaziya anafunsa anthuwo kuti: “Kodi munthu amene anabwera kudzakumana nanuyo n’kukuuzani zimenezi anali kuoneka bwanji?” Anthuwo poyankha anafotokoza mmene mneneriyo anavalira ndipo pomwepo Ahaziya ananena kuti: “Ndi Eliya.” (2 Mafumu 1​:7, 8) N’zochititsa chidwi kuti Eliya ankakhala moyo wosalira zambiri ndipo maganizo ake onse anali potumikira Yehova moti anthu ankatha kumuzindikira ndi zovala zomwe ankavala. Zimenezi zinali zosiyana kwambiri ndi Ahaziya komanso makolo ake chifukwa anali adyera komanso okonda kwambiri chuma. Chitsanzo cha Eliyachi chikutikumbutsa malangizo a Yesu oti tizikhala moyo wosalira zambiri ndipo tiziganizira zinthu zomwe ndi zofunika kwambiri.​—Mateyu 6:​22-​24.

Ahaziya anaganiza zobwezera. Choncho anatumiza asilikali 50 ndi atsogoleri awo kuti akagwire Eliya. Anthuwo anamupeza Eliya “atakhala pamwamba pa phiri” * ndipo mwamwano mkulu wa asilikali analamula Eliya m’dzina la mfumu yawo kuti “Tsika.” Mkulu wa asilikaliyo analankhula zimenezi kutanthauza kuti anali okonzeka kutenga mneneriyu kuti akamumange. Eti tangoganizani, ngakhale kuti anthuwa ankadziwa kuti Eliya anali “munthu wa Mulungu,” asilikaliwa ankaona kuti akhoza kumuopseza. Anthuwa sankadziwa chomwe ankachita. Eliya anauza mkulu wa asilikaliyo kuti: “Ngati ndili munthu wa Mulungu, moto utsike kumwamba n’kunyeketsa iweyo ndi asilikali ako 50.” Ndipo ndi zimenedi Mulungu anachita. “Moto unatsikadi kumwamba n’kunyeketsa mtsogoleriyo ndi asilikali ake 50.” (2 Mafumu 1​:9, 10) Zomwe zinachitikira asilikaliwa zikusonyezeratu kuti Yehova zimamupweteka kwambiri anthu akamanyoza atumiki ake.​—1 Mbiri 16:21, 22.

Kenako Ahaziya anatumizanso mtsogoleri wa asilikali ndi asilikali enanso 50. Mtsogoleri wachiwiriyu ndi amene anali wamwano kwambiri kuposa woyamba uja. Ngakhale kuti mwina n’kutheka kuti anaona phulusa la anthu 51 omwe anaphedwawo m’mbali mwa phiri, iye sanaphunzirepo kanthu. Iye anabwerezanso mawu omwe mtsogoleri wa asilikali woyamba uja analankhula pouza Eliya kuti atsike m’phiri. Komabe iye anawonjezera kumuuza kuti “Tsika msanga.” Kunalidi kupanda nzeru chifukwa pamapeto pake iye ndi asilikali akewo anaphedwanso ngati gulu loyamba lija. Komanso mfumu yawo ndi imene inasonyeza kuti inali yopusa kwambiri chifukwa inatumizanso gulu lina lachitatu. Koma n’zochititsa chidwi kuti mtsogoleri wachitatuyi anachita zinthu mwanzeru. Anafika kwa Eliya modzichepetsa ndipo anachonderera kuti iye ndi asilikali ake asawaphe. N’zosakayikitsa kuti Eliya anasonyeza chifundo cha Yehova polankhula ndi mtsogoleri wodzichepetsayo. Mngelo wa Yehova anauza Eliya kuti apite limodzi ndi asilikaliwo. Eliya ananyamukadi ndipo anakabwereza uthenga wachiweruzo wochoka kwa Yehova polankhula ndi mfumuyo. Ahaziya anafadi mogwirizana ndi zimene Yehova ananena. Iye anangolamulira kwa zaka ziwiri zokha.​—2 Mafumu 1:​11-​17.

Eliya anasonyeza chifundo cha Yehova atakumana ndi mtsogoleri wa asilikali wodzichepetsa

Kodi Eliya anakwanitsa bwanji kupirira pomwe ankalimbana ndi anthu opanduka komanso amakaniwo? Nkhani imeneyi ndi yofunika kuiganizira kwambiri masiku ano. Kodi munakhumudwapo mutapereka malangizo kwa munthu wina amene munkamukonda koma iye anakana malangizowo n’kupitirizabe kuchita zolakwikazo? Kodi tingapirire bwanji zimenezi zikachitika? Tingaphunzire mfundo ina tikaganizira za malo omwe Eliya anali. Paja Baibulo limati asilikaliwo ankakamupeza “pamwamba pa phiri.” Sitinganene motsimikiza chomwe chinkachititsa kuti Eliya akhale pamwambapo komabe tikudziwa kuti ankakonda kwambiri kupemphera. Choncho n’kutheka kuti ankaona kuti malowa ankamupatsa mwayi wopemphera kwa Mulungu wake. (Yakobo 5:​16-​18) Ifenso tingachite bwino kupeza nthawi yokhala patokha ndi kupemphera kwa Mulungu, kuitana dzina lake n’kumuuza mavuto athu komanso zomwe zikutidetsa nkhawa. Zimenezi zingatithandize kuti tithe kupirira anzathu akayamba kutsatira njira yolakwika.

Kusiyira Elisa Udindo

Tsopano nthawi yoti Eliya atule pansi udindo wake inali itakwana. Tiyeni tione zomwe anachita panthawiyi. Pamene iye ndi Elisa ankatuluka m’tauni ya Giligala, Eliya anauza Elisa kuti akhalebe mumzindamo ndipo iye apita ku Beteli yekha. Mtundawu unali wa makilomita 11. Elisa sanavomere kusiyana ndi Eliya. Iye ananena kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo ndiponso pali moyo wanu, sindikusiyani.” Atafika ku Beteli, Eliya anauzanso Elisa kuti akupita ku Yeriko ndipo asamulondole. Mtundawo unali wa makilomita 22. Apanso Elisa anakana ndipo ananenanso zomwe ananena poyamba paja. Atafika ku Yeriko, kutatsala makilomita 8 kuti afike kumtsinje wa Yorodano, Eliya anauzanso Elisa kachitatu kuti asamutsatire. Panthawi imeneyinso Elisa anakanitsitsa kuti sangasiyane naye.​—2 Mafumu 2:1-6.

Elisa anasonyeza kuti anali ndi chikondi chenicheni. Chikondi chimenechi ndi chimenenso Rute anasonyeza kwa Naomi. Munthu akamakonda kwambiri munthu wina ndi chikondi choterechi, salola kuti asiyane. (Rute 1:15, 16) Atumiki onse a Yehova amafunika kusonyezana chikondi ngati chimenechi makamaka panopa. Tiziona kuti chikondi chimenechi ndi chofunika kwambiri ngati mmene anachitira Elisa.

Eliya ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi chikondi cha Elisa. Chikondi chimenechi chinachititsa kuti Elisa akhale ndi mwayi woona chozizwitsa chomaliza cha Eliya. Ataima m’mbali mwa mtsinje wa Yorodano, Eliya anamenya madzi a mtsinjewo ndi chovala chake chauneneri. Ngakhale kuti mtsinjewo unali wozama ndipo unkathamanga kwambiri, madziwo anagawanika uku ndi uku. Pamalowa panalinso ‘ana 50 a aneneri’ omwe ankaona zonse. Choncho zikuonekeratu kuti kunali gulu la amuna omwe ankaphunzitsidwa kuti adzatsogolere kulambira koyera m’dzikolo. (2 Mafumu 2​:7, 8) Ndipo n’zachidziwikire kuti anthuwo ankaphunzitsidwa ndi Eliya. Zaka zingapo m’mbuyomo, Eliya ankadziona kuti watsala yekhayekha monga munthu wokhulupirika m’dzikolo. Apa tsopano tingati Yehova anadalitsa Eliya chifukwa cha kupirira kwake popeza panthawiyi anaona gulu la anthu okhulupirira Mulungu.​—1 Mafumu 19:10.

Atawoloka mtsinje wa Yorodano, Eliya anauza Elisa kuti: “Pempha chimene ukufuna kuti ndikuchitire ndisanakuchokere.” Eliya anadziwa kuti nthawi yoti achoke yakwana. Iye sanafune kubisira Elisa mwayi komanso udindo womwe adzakhale nawo m’tsogolo. Eliya anali wokonzeka kumuthandiza pa chilichonse. Elisa anangopempha kuti: “Chonde, magawo awiri a mzimu wanu abwere kwa ine.” (2 Mafumu 2:9) Iye sankatanthauza kuti apatsidwe mzimu woyera wochuluka kuwirikiza kawiri kuposa wa Eliya. Koma iye ankapempha cholowa ngati chomwe chinkaperekedwa kwa mwana woyamba kubadwa. Mogwirizana ndi malamulo a panthawiyo, mwana woyamba ankapatsidwa gawo lalikulu kapena chuma chowirikiza kawiri pa gawo la chuma cha makolo ake chifukwa ankakhala ndi udindo wotsogolera banja. (Deuteronomo 21:17) Elisa analinso ngati mwana woyenera kulandira cholowa kwa Eliya. Choncho kuti akwanitse kugwira ntchito yake, anaona kuti zinali zoyenera kuti apatsidwe mzimu wochita zinthu mwakhama ngati umene Eliya anali nawo.

Eliya anasonyeza kudzichepetsa polola kuti Yehova ayankhe yekha zimene Elisa anapempha. Ngati Yehova akanalola kuti Elisa aone Eliya akutengedwa, zikanasonyeza kuti Mulunguyo wavomera kupatsa Elisa zomwe anapempha. Ndipo patangopita nthawi yochepa “pamene anali kuyenda n’kumalankhulana” panachitika chinachake chodabwitsa.​—2 Mafumu 2:​10, 11.

Eliya ndi Elisa anakwanitsa kupirira mavuto chifukwa ankakondana

Pa nthawiyi kumwamba kunaoneka kuwala kodabwitsa ndipo kuwalako kunkawonjezerekabe. Ganizirani kuti pa nthawiyi mukuona kuwalako kukubwera ndi phokoso lokhala ngati chimkokomo cha mphepo yoopsa kumayandikira amuna awiriwo. Ndipo kuwala kodabwitsako kukuchititsa amunawo kuyamba kudzandira chobwerera m’mbuyo mpaka kulekana. Kuwalako kunali kwa galeta lomwe linali kuyaka ngati moto. Pamene zimenezi zinkachitika Eliya anadziwa kuti nthawi yake yoti atengedwe yakwana. Koma kodi iye anangofikira kukwera galetalo? Nkhaniyi sifotokoza mmene zinachitikira. Koma Eliya anangozindikira kuti chimphepo chamunyamula n’kuyamba kupita m’mwamba kwambiri.

Apa n’kuti Elisa akungoyang’ana modabwa. Popeza kuti Elisa ankaona zomwe zinkachitikazi, sanakayikire kuti Yehova amupatsa “magawo awiri” a mzimu wa Eliya womwe ukanamuthandiza kuchita zinthu molimba mtima. Komabe, Elisa sanaganizire kwambiri za zinthu zomwe anapemphazi chifukwa pa nthawiyi anali wokhumudwa. Iye sanadziwe komwe bwenzi lake Eliya ankapita ndipo n’zachidziwikire kuti ankaganiza kuti sadzamuonanso. Kenako anafuula kuti: “Bambo anga, bambo anga! Galeta lankhondo la Isiraeli ndi okwera mahatchi ake.” Elisa ankayang’anitsitsabe pamene Eliya ankapita mpaka osaonekanso ndipo anang’amba zovala zake chifukwa chokhumudwa.​—2 Mafumu 2:12.

Kodi n’kutheka kuti pamene Eliya ankanyamuka, ankamva kulira kwa Elisa ndipo mwina nayenso analira chifukwa chomva chisoni? Mwina zinaterodi, komabe iye anakumbukira kuti Elisa anamuthandiza kukhala wopirira pamene ankakumana ndi mavuto. Chitsanzo cha Eliya chikutiphunzitsa kuti tizigwirizana kwambiri ndi anthu amene amakonda Yehova komanso amene amayesetsa kuchita zimene iye amafuna.

Yehova anatumiza Eliya kudera lina kuti akachite utumiki watsopano

Utumiki Womaliza

Kodi Eliya atatengedwa anapita kuti? Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti anapita kumwamba kukakhala ndi Mulungu. Koma zimenezi ndi zosatheka. Tikutero chifukwa patadutsa zaka zingapo, Yesu Khristu ananena kuti palibe aliyense amene anakwerako kumwamba mpaka pa nthawi imene iyeyo anabwera padzikoli. (Yohane 3:​13) Choncho tikawerenga kuti “Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho n’kukwera kumwamba,” tizidzifunsa kuti, Kodi kumwamba kwake ndi kuti? (2 Mafumu 2:​11) Nthawi zina Baibulo likamanena za “kumwamba,” silimangotanthauza malo amene Yehova amakhala. Koma limanenanso za kumwamba kumene timaonaku, komwe kuli mitambo komanso komwe kumauluka mbalame. (Salimo 147:8) Choncho Eliya anapita kumwamba komwe timaonaku kapena kuti mlengalenga. Ndiye kodi ulendowo unali wopita kuti?

Mwachidule, Yehova anamupititsa kudera lina mu ufumu wa ku Yuda komwe anakamupatsa utumiki watsopano. Patadutsa zaka zoposa 7 kuchokera pamene Eliya anatengedwa, nkhani ina ya m’Baibulo inasonyeza kuti Eliya ankachitabe utumiki kumeneko. Nthawi imeneyo Mfumu Yehoramu ndi imene inkalamulira ku Yuda koma inali mfumu yoipa. Yehoramu anakwatira mwana wamkazi wa Ahabu ndi Yezebeli ndiye zikuoneka kuti makhalidwe oipa a makolowa ankapitirirabe. Choncho Yehova anauza Eliya kuti alembe kalata yopereka chiweruzo kwa Yehoramu. Kenako mogwirizana ndi zomwe Eliya ananena, Yehoramu anamwalira atadwala matenda oopsa. Kuwonjezera pamenepo, ponena za imfa yake nkhaniyi imamaliza ndi mawu akuti: “Anapita popanda womumvera chisoni.”​—2 Mbiri 21:12-​20.

Apa zikuonekeratu kuti Eliya anali wosiyana kwambiri ndi munthu woipayu. Koma sitikudziwa kuti Eliya anamwalira liti komanso kuti anamwalira bwanji. Komabe tikudziwa kuti sanafe ngati mmene Yehoramu anafera, popanda womumvera chisoni. N’zosakayikitsa kuti Elisa anamusowa kwambiri Eliya ndipo n’kutheka kuti ndi mmenenso aneneri enanso okhulupirika anamvera. Yehova anasonyeza kuti ankaonabe Eliya kukhala munthu wofunika kwambiri chifukwa patadutsa zaka 1,000, anachititsa kuti Eliya aonekere m’masomphenya panthawi imene Yesu anasandulika. (Mateyu 17:​1-9) Kodi inunso mumafuna mutakhala ndi chikhulupiriro ngati cha Eliya kuti chizikuthandizani kupirira mukakumana ndi mavuto? Ngati ndi choncho, muziyesetsa kugwirizana ndi anthu omwe amakondanso Yehova, muziyesetsa kutumikira Yehova ndi mtima wonse komanso muzipemphera mochokera pansi pamtima. Mukatero, nanunso Yehova adzapitiriza kukukondani.

^ ndime 9 Akatswiri ena amati phiri limeneli ndi la Kalimeri pomwe Mulungu anagwiritsa ntchito Eliya yemweyo kugonjetsa aneneri a Baala zaka zam’mbuyomo izi zisanachitike. Komabe Baibulo silinena kuti linali phiri lanji.