Pitani ku nkhani yake

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

“Ndinali Ndi Mafunso Ambiri”

“Ndinali Ndi Mafunso Ambiri”
  • Chaka Chobadwa: 1976

  • Dziko: Honduras

  • Poyamba: Ndinali m’busa

KALE LANGA

 Ndinabadwira ku La Ceiba, ku Honduras. Ndine womaliza m’banja la ana 5, ndipo mnyamata ndilipo ndekha. M’banja lathu ine ndekha ndi amene ndili ndi vuto losamva. Tinkakhala mumzinda woopsa komanso tinali osauka kwambiri. Ndipo zinthu zinaipa kwambiri bambo anga atachita ngozi kuntchito, n’kumwalira. Nthawi imeneyo n’kuti ndili ndi zaka 4 zokha.

 Mayi anga ankachita zonse zimene akanatha kuti azitisamalira, koma sankapeza ndalama zokwanira zoti n’kumatigulira zovala. Kukamagwa mvula, ndinkazizidwa kwambiri chifukwa ndinalibe zovala zamphepo.

 Pamene ndinkakula, ndinaphunzira Chinenero Chamanja cha ku Honduras (chomwe timangochitchula kuti LESHO), ndipo chinkandithandiza kuti ndizilankhulana ndi anzanga omwe analinso ndi vuto losamva. Koma amayi ndi azichemwali anga sankachidziwa bwino chinenero chamanjachi, moti ankangopanga okha zizindikiro zondithandiza kudziwa zimene akunena. Komabe mayi anga ankandikonda kwambiri komanso ankanditeteza. Pa zochepa zomwe ankadziwa zokhudza chinenero chamanjacho, ankandichenjeza kuti ndizipewa makhalidwe oipa monga kusuta komanso kuledzera. Panopa ndimasangalala kwambiri chifukwa ndinayesetsa kupewa makhalidwe amenewa.

 Ndili wamng’ono, mayi anga ankanditenga akamapita kutchalitchi cha Katolika, koma palibe chomwe ndinkamvako chifukwa kunalibe munthu woti azindimasulira m’chinenero chamanja. Ndili ndi zaka 10 ndinasiya kupitako chifukwa sikunkandisangalatsa. Komabe ndinkafuna kudziwa zambiri zokhudza Mulungu.

 Mu 1999, ndili ndi zaka 23, ndinakumana ndi mayi wina wa ku United States yemwe anali wa tchalitchi cha evanjeliko. Mayiyu ankandiphunzitsa Baibulo komanso Chinenero Chamanja cha ku America (ASL). Zimene ndinkaphunzirazo zinkandisangalatsa kwambiri moti ndinaganiza zoti ndidzakhale m’busa. Kenako ndinapita kusukulu yophunzitsa ubusa ya anthu a vuto losamva ku Puerto Rico. Nditabwerera ku La Ceiba mu 2002, ndinayambitsa tchalitchi changa cha anthu a vuto losamva mothandizidwa ndi anzanga ena atatu. Mmodzi mwa anzangawo, Patricia, ndi amene anadzakhala mkazi wanga.

 Monga m’busa, ndinkalalikira m’Chinenero Chamanja cha ku Honduras, ndinkaonetsa zithunzi zofotokozera nkhani za m’Baibulo, komanso kupanga masewero a nkhanizi kuti anzanga enanso a vuto losamva azitha kumva. Ndinkapitanso kumizinda ina yapafupi komwe kunalinso anthu ena a vutoli, kuti ndizikawalimbikitsa komanso kuwathandiza pa mavuto awo. Ndinakachitanso umishonale ku United States ndi ku Zambia. Koma kunena zoona, sindinkadziwa zambiri zokhudza Baibulo. Zomwe ndinkaphunzitsa anthuwo zinali zomwe ndinangouzidwa komanso zomwe ndinazimvetsa pa zithunzi. Moti ndinali ndi mafunso ambiri.

 Tsiku lina, anthu ena atchalitchi changa anayamba kufalitsa mabodza okhudza ineyo. Anandinamizira kuti ndikungokhalira kuledzera komanso ndikumayenda ndi akazi ena. Zinandikhumudwitsa kwambiri ndipo pasanapite nthawi, ine ndi Patricia tinasiya tchalitchicho.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA

 Nthawi zambiri a Mboni za Yehova akabwera kuti adzatiphunzitse, ine ndi Patricia sitinkawalandira. Koma titangosiya tchalitchi chathu chija, Patricia anavomera kuti aziphunzira Baibulo ndi banja lina la Mboni, la a Thomas ndi mkazi wawo Liccy. Ndinachita chidwi kuona kuti banjali linkadziwa chinenero chamanja ngakhale kuti iwowo analibe vuto losamva. Pasanapite nthawi, nanenso ndinayamba kuphunzira nawo.

 Kwa miyezi ingapo, a Mboniwo ankatiphunzitsa pogwiritsa ntchito mavidiyo a Chinenero Chamanja cha ku America. Koma kenako anzathu ena anayamba kunena kuti a Mboni za Yehova amatsatira anthu, choncho tinasiya kuphunzira. Ngakhale kuti Thomas anayesetsa kundionetsa umboni woti a Mboni za Yehova satsogoleredwa ndi munthu, sindinamukhulupirire.

 Patadutsa miyezi ingapo, Patricia anayamba kuvutika maganizo ndipo anapemphera kwa Mulungu kuti a Mboni za Yehova abwerenso kunyumba kwathu. Pasanapite nthawi, neba wathu yemwe anali wa Mboni anabwera kudzamuona Patricia ndipo anamuuza kuti akamupempha Liccy kuti adzamuonenso. Liccy anasonyezadi kuti anali mnzake weniweni wa Patricia moti wiki iliyonse ankabwera kudzamulimbikitsa komanso kudzaphunzira naye Baibulo. Koma ineyo sindinkawakhulupirabe anthu a Mboni.

 Mu 2012, a Mboni za Yehova ankagwira ntchito yapadera yogawira vidiyo yakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? ya Chinenero Chamanja cha ku Honduras ndipo Liccy anatibweretsera vidiyoyi. Nditaionera, ndinadabwa kuti zambiri zomwe ndinkaphunzitsa monga zakuti, kuli moto wa helo komanso mzimu wa munthu suufa, sizipezeka m’Baibulo.

 Wiki yotsatira, ndinapita ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kuti ndikakumane ndi Thomas. Ndinamuuza kuti ndikufuna ndiziphunzitsa choonadi cha m’Baibulo anthu a vuto losamva, koma osati ngati wa Mboni za Yehova. Cholinga changa chinali choti ndiyambitse tchalitchi chatsopano cha anthu a vuto losamva. Thomas anandiyamikira chifukwa cha zomwe ndinkafunazi, koma anandionetsa lemba la Aefeso 4:5, lomwe limalimbikitsa kuti mpingo woona wachikhristu uzichita zinthu mogwirizana.

 Thomas anandipatsanso vidiyo ya Chinenero Chamanja cha ku America yakuti Mboni za Yehova Zinasonyeza Chikhulupiriro, Gawo 1: Kutuluka mu Mdima. Mu vidiyoyi, anafotokoza bwino zimene anthu ena anachita kuti afufuze komanso kumvetsa ziphunzitso zoona za m’Baibulo. Ndikamaionera, ndinkatha kumvetsa mmene anthuwo ankamvera chifukwa nanenso ndinkafunitsitsa nditadziwa choonadi. Vidiyoyi inandithandiza kukhulupirira kuti zimene a Mboni amaphunzitsa komanso kukhulupirira zimachokera m’Baibulo. Choncho ndinayambiranso kuphunzira Baibulo, ndipo mu 2014, ine ndi Patricia tinabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA

 Ndimakonda mpingo wa Mboni za Yehova chifukwa ndi oyera monga mmenenso Mulungu alili woyera. Anthu ake sayankhula zinthu zoipa komanso sachitira anzawo zoipa. Amakonda mtendere komanso amalimbikitsana. Anthu a Mboni ndi ogwirizana ndipo onse amaphunzitsa mfundo za m’Baibulo za choonadi zofanana mosatengera dziko lomwe ali, kapena chilankhulo chawo.

 Ndimasangalala kwambiri kuti ndinadziwa zimene Baibulo limaphunzitsa. Mwachitsanzo, ndinaphunzira kuti Yehova ndi Mulungu Wamphamvuyonse komanso Wolamulira Wamkulu wachilengedwe chonse. Amakonda aliyense kaya ali ndi vuto losamva kapena ayi. Ndimaona kuti chikondi chimene Mulungu amandisonyeza ndi chamtengo wapatali. Ndinaphunziranso kuti dzikoli lidzakhala paradaiso wokongola kwambiri ndipo tidzakhala ndi mwayi wosangalala ndi moyo wosatha popanda kudwala. Ndikuyembekezera mwachidwi nthawi imene zinthu zimenezi zidzachitike.

 Ine ndi Patricia timakonda kuuza anthu ena omwe ali ndi vuto losamva, mfundo za m’Baibulo. Panopa tikuphunzira Baibulo ndi anthu ena atatu omwe tinali nawo limodzi m’tchalitchi chathu chakale chija. Koma sindimakhalanso ndi mafunso okhudza zimene ndikuphunzitsa ngati mmene ndinkachitira ndili m’busa. Kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova kunandithandiza kuti ndipeze mayankho a mafunso anga.