Pitani ku nkhani yake

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinagwirizana ndi Bambo Anga Patatha Zaka Zambiri

Ndinagwirizana ndi Bambo Anga Patatha Zaka Zambiri
  • CHAKA CHOBADWA: 1954

  • DZIKO: Philippines

  • POYAMBA: Anasiyana ndi bambo ake omwe anali ankhanza kwambiri

KALE LANGA

 Alendo ochokera m’mayiko ena amakonda kudzaona mathithi otchuka kwambiri omwe ali kufupi ndi tauni ya Pagsanjan ku Philippines. Derali ndi lomwe bambo anga a Nardo Leron anakulira. Iwo anabadwa mpaka kukula ali mu umphawi. Zinthu zachinyengo zomwe zinkachitika m’boma, ku polisi komanso komwe ankagwira ntchito, zinkachititsa bambo anga kukhala munthu waukali kwambiri.

 Makolo anga ankagwira ntchito mwakhama kuti athe kusamalira ana awofe omwe tonse pamodzi tinalipo 8. Nthawi zambiri ankalima kudera la kumapiri ndipo pankatenga nthawi yaitali asanabwerere kunyumba. Ine ndi mchimwene wanga dzina lake Rodelio, tinkayenera kudzipezera tokha zinthu zofunika komabe nthawi zambiri tinkangokhala ndi njala. Sitinkapezanso nthawi yoti tingasewereko monga ana. Mwana aliyense akakwanitsa zaka 7 ankayenera kuyamba kugwira ntchito zakumunda. Ankafunika kumanyamula matumba olemera a kokonati n’kumadutsa nawo m’tinjira ta m’mapiri. Thumbalo likakhala lolemera kwambiri, tinkachita kulikoka.

 Bambo athu ankangokhalira kutimenya koma chomwe chinkandipweteka kwambiri n’kuwaona akumenya mayi athu. Tinkayesera kuwaletsa koma sizinkaphula kanthu. Kenako ine ndi Rodelio tinakonza chiwembu choti tikadzakula, tidzawaphe. Kunena zoona ndinkafunitsitsa nditakhala ndi bambo wabwino woti azitikonda.

 Ndili ndi zaka 14 zokha ndinachoka pakhomo pothawa nkhanza za bambo anga. Kwa nthawi ndithu, ndinkakhala m’misewu ndipo ndinayamba kusuta chamba. Kenako ndinayamba kugwira ntchito yoyendetsa boti. Ndinkanyamula alendo odzaona malo n’kumakawasiya kokaona mathithi.

 Patapita zaka zochepa, ndinayamba kuphunzira payunivesite ina ku Manila. Koma sindinkapeza nthawi yokwanira yochita maphunziro anga chifukwa wiki iliyonse ikamatha ndinkafunika kubwerera kwathu ku Pagsanjan kukagwira ntchito. Ndinkaona kuti moyo wanga ulibe tsogolo lililonse ndipo kusuta chamba sikunkandithandiza kuthetsa nkhawa zanga. Ndinayambanso kugwiritsa ntchito mankhwala ena osokoneza bongo monga kokeni ndi ena. Ndipotu mankhwala osokoneza bongo ndi khalidwe la chiwerewere zimayendera limodzi. Ndinkaona kuti kulikonse anthu akuvutika ndi umphawi komanso zinthu zopanda chilungamo. Ndinkadana kwambiri ndi boma chifukwa ndinkaona kuti ndi limene linkachititsa mavuto onsewa. Ndiyeno ndinkafuna kudziwa chifukwa chake Mulungu amalola kuti anthu azizunzika. Koma sindinapeze yankho m’zipembedzo zosiyanasiyana zomwe ndinalowa. Kenako ndinaonjeza kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kuti ndiziiwalako za mavuto anga.

 Mu 1972, ana a sukulu ku Philippines anakonza zochita zionetsero zolimbana ndi boma. Ndinalowa nawo m’gululi ndipo pa nthawiyi tinachita zinthu zachiwawa kwambiri. Anthu ambiri anamangidwa ndipo patapita miyezi ingapo asilikali ankapezeka paliponse m’dzikoli.

 Ndinayambiranso kukhala mumsewu poopa akuluakulu a boma chifukwa ndinachita nawo zionetserozo. Kuti ndizipeza ndalama zogulira mankhwala osokoneza bongo, ndinayamba kuba. Ndinayambanso kuchita zachiwerewere ndi anthu achuma komanso ochokera kumayiko ena. Zoti kaya ndifa, ndinalibe nazo ntchito.

 Komabe pa nthawiyi, mayi anga komanso mng’ono wanga anali atayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Bambo anga anakwiya nazo kwambiri moti anawaotchera mabuku omwe ankagwiritsa ntchito. Ngakhale zinali choncho, iwo anapirirabe mpaka kubatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova.

 Tsiku lina wa Mboni wina anacheza ndi bambo anga. Wa Mboniyo anawauza kuti Baibulo limalonjeza kuti m’tsogolomu zinthu zizidzayenda mwachilungamo padziko lonse. (Salimo 72:12-14) Mfundoyi inawachititsa chidwi kwambiri moti anayamba kufufuza zambiri paokha kuti atsimikize ngati zinalidi zoona. Pofufuzapo anapezanso kuti Baibulo limanena za udindo umene mwamuna wokwatira ayenera kuukwaniritsa. (Aefeso 5:28; 6:4) Patapita nthawi yochepa bambo ndi azibale anga ena onse anakhalanso a Mboni. Popeza ndinkakhala kutali, sindinkadziwa kuti umu ndi mmene zinthu zinasinthira kunyumba.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA

 Mu 1978, ndinasamukira ku Australia. Ngakhale kuti dzikoli ndi lolemera komanso la mtendere, sindinkapeza mtendere wamumtima. Kumeneko ndinapitirizabe kuledzera komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Chaka chimenecho chisanathe, kunabwera a Mboni za Yehova. Ndinachita chidwi ndi zimene anandiwerengera m’Baibulo zoti dzikoli lidzakhala lamtendere koma sindinkafuna kuti ndizolowerane nawo.

 Patangopita nthawi yochepa, ndinabwereranso ku Philippines kukacheza kwa mawiki angapo. Azibale anga anandiuza kuti bambo anasinthiratu moti panopa ndi munthu wabwino kwambiri. Koma mumtimamu ndinali nditawasungirabe mkwiyo moti sindinkafuna kuonana nawo.

 Mchemwali wanga wamng’ono anandifotokozera kuchokera m’Baibulo chifukwa chake m’dzikoli muli mavuto ambiri komanso zinthu zopanda chilungamo. Ndinadabwa kwambiri kuona kuti mwana wamng’ono ngati ameneyu wakwanitsa bwanji kuyankha mafunso anga. Ndisananyamuke, bambo anandipatsa buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. a Iwo anandiuza kuti “Mwana wanga ukhazikike. Bukuli lidzakuthandiza kupeza zomwe ukufuna.” Anandilimbikitsa kuti ndikabwereranso ku Australia ndikafufuze a Mboni za Yehova.

 Ndinatsatira zomwe bambo anandiuza moti ndinafufuza Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ku Brisbane chakufupi ndi komwe ndinkakhala. Ndinavomera kuti ndiziphunzira nawo Baibulo. Maulosi a m’Baibulo opezeka pa Danieli chaputala 7 ndi pa Yesaya chaputala 9, anandithandiza kudziwa kuti boma la Mulungu lomwe ndi boma lopanda zachinyengo, lidzalamulira dzikoli m’tsogolomu. Ndinaphunzira kuti dzikoli lidzakhala Paradaiso ndipo tidzakhala ndi moyo wabwino kwambiri. Ndinkafuna kuti Mulungu azindikonda komabe ndinazindikira kuti ndiyenera kupewa kukhala ndi mtima wapachala, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuledzera komanso kuchita zachiwerewere. Ndinasiyana ndi mtsikana amene ndinkakhala naye ndipo ndinasiyiratu mankhwala osokoneza bongo komanso kuledzera. Chikhulupiriro changa chinayamba kulimba ndipo ndinkapemphera kwa Yehova kuti andithandize kusintha.

 Pang’onopang’ono ndinayamba kuona kuti mfundo za m’Baibulo zikhoza kusinthadi munthu. Baibulo limanena kuti tikachita khama, tikhoza kuvala “umunthu watsopano.” (Akolose 3:​9, 10) Pamene ndinkasintha zina ndi zina pa moyo wanga ndinayamba kuvomereza kuti bambo anga ayenera kuti anasinthadi. M’malo mopitiriza kuwasungira mkwiyo, ndinafuna kuti ndikhale nawo pamtendere. Pamapeto pake ndinawakhululukira ndipo ndinachotsa zonse zomwe ndinawasungira mumtima kuyambira ndili mwana.

PHINDU LIMENE NDAPEZA

 Monga wachinyamata, ndinkangotsatira makhalidwe oipa a anzanga. Ndimaona kuti zimene Baibulo limanena ndi zoona. Ndinali ndi moyo wolowerera chifukwa chotengera zochita za anzanga. (1 Akorinto 15:33) Ndinapeza mabwenzi odalirika kwambiri m’gulu la Yehova omwe anandithandiza kukhala munthu wabwino. M’gululi ndinapezamonso mkazi yemwe ndimamukonda dzina lake Loretta. Ine ndi Loretta timaphunzitsa anthu mmene Baibulo lingawathandizire.

Ine ndi mkazi wanga tikudya chakudya limodzi ndi anzathu

 Ndimayamikira kwambiri kuti Baibulo linathandiza bambo anga kuti asinthe zinthu zomwe sindinkalotako n’komwe. Bambo anga anakhala munthu wodzichepetsa, anayamba kukonda kwambiri mayi anga komanso ndi anali Mkhristu wokonda mtendere. Ndinakumananso ndi bambo anga mu 1987 nditabatizidwa. Pa nthawiyi bambo anandikumbatira kwa nthawi yoyamba m’moyo wanga.

 Kwa zaka zoposa 35, bambo ndi mayi anga akhala akugwira ntchito limodzi pophunzitsa anthu Baibulo. Bambo anayamba kudziwika monga munthu wochita zinthu moganizira ena komanso kugwira ntchito yothandiza anthu. Pa zaka zimenezi ndinayamba kuwakonda komanso kuwalemekeza ndipo ndinkanyadira kuti ndine mwana wawo. Iwo anamwalira mu 2016, koma ndimasangalala ndikaganizira kuti ine ndi iwowo tinasintha kwambiri chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Panopa sindinawasungire chifukwa chilichonse mumtima. Ndimathokoza kwambiri kuti ndinadziwa Yehova amene ndi Atate wanga wakumwamba, yemwe analonjeza kuti adzachotsa mavuto onse omwe mabanja amakumana nawo.

a Bukuli linkafalitsidwa ndi a Mboni za Yehova koma panopa anasiya kulisindikiza.